Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w18 October tsamba 32
  • Kodi Mukudziwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Nkhani Yofanana
  • “Sitefano Anali ndi Mphamvu Ndipo Ankachita Kuonekeratu Kuti Mulungu Ali Naye”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Stefano Aponyedwa Miyala
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Yendani M’kuwopa kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
w18 October tsamba 32

Kodi Mukudziwa?

N’chiyani chinathandiza Sitefano kuti akhalebe wodekha pamene ankazunzidwa?

Sitefano anali wodekha poweruzidwa ndi Khoti Lalikulu la Ayuda

SITEFANO anali pakati pa gulu la anthu okwiya kwambiri mu Khoti Lalikulu la Ayuda. Khotili linali ndi oweruza 71 ndipo anthu amenewa anali amphamvu kwambiri mu Isiraeli. Apa n’kuti patangopita miyezi yochepa kuchokera pamene mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa ankatsogolera zinthu pa nthawi imene Yesu anaweruzidwa kuti aphedwe. (Mat. 26:57, 59; Mac. 6:8-12) Ndiye Kayafa yemweyu anasonkhanitsanso oweruza n’kumaitana mboni zonama kuti zimuneneze. Koma onse anadabwa kuti nkhope ya Sitefano inkaoneka “ngati nkhope ya mngelo.”​—Mac. 6:13-15.

Kodi n’chiyani chinathandiza Sitefano kuti asaope koma akhalebe wodekha? Iye asanapititsidwe kukhotili ankagwira ntchito ya Mulungu mwakhama ndipo mzimu woyera unkamuthandiza kwambiri. (Mac. 6:3-7) Ndiye akuzengedwa mlandu, mzimu womwewo unkamulimbikitsa komanso kumuthandiza kukumbukira malemba. (Yoh. 14:16) Mfundo zimene Sitefano ananena pofotokoza mbali yake pamlanduwu, zikupezeka m’chaputala 7 cha Machitidwe ndipo mzimu woyera unamuthandiza kukumbukira mavesi oposa 20 a m’Malemba Achiheberi. (Yoh. 14:26) Koma chikhulupiriro cha Sitefano chinalimba kwambiri ataona masomphenya a Yesu ali kudzanja lamanja la Mulungu.​—Mac. 7:54-56, 59, 60.

Mwina nafenso tsiku lina tidzakhala pakati pa anthu olusa. (Yoh. 15:20) Tikakhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu komanso kulalikira, timalola mzimu wa Yehova kuti uzitithandiza. Ndipo mzimuwo ukhoza kutithandiza kuti tidzakhale ndi mtendere wamumtima pa nthawi imene anthu ena akutizunza.​—1 Pet. 4:12-14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena