Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp19 No. 2 tsamba 8-9
  • Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MAVESI AMENE ANGAKUTHANDIZENI
  • Kulimbana ndi Mavuto mwa Kukhala N’zolinga
    Galamukani!—2001
  • Zimene Zingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kodi Kuyanjananso N’kotheka?
    Galamukani!—1999
  • Ndinasankha Ntchito Yabwino Kwambiri
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
wp19 No. 2 tsamba 8-9
Mzimayi akupemphera

Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika

Maria, yemwe amakhala ku Spain, anati: “Mwamuna wanga atandiuza kuti akufuna kundisiya kuti akakwatire kamtsikana, zinandipweteka kwambiri mumtima moti ndinkaona kuti bola kungofa. Ndinkaona kuti si chilungamo, makamaka ndikaganizira zinthu zambirimbiri zimene ndinamuchitira.”

Bill, yemwenso amakhala ku Spain, anati: “Mkazi wanga atandithawa, ndinkangoona ngati mbali ina ya thupi langa yafa. Ndinkaona kuti maloto ndi mapulani athu onse athera pompo. Nthawi zina ndinkaona ngati ndasiya kuda nazo nkhawa, koma pakangotha masiku angapo ndinkayambiranso kuda nkhawa kwambiri.”

ZIMAKHALA zowawa kwambiri, mkazi kapena mwamuna akachita zinthu zosakhulupirika m’banja. N’zoona kuti amuna kapena akazi ena amasankha kukhululukira mnzawoyo ngati wapepesa ndipo amayesetsa kuti ayambirenso kumakhala bwinobwino.a Koma kaya banjalo likhalapobe kapena ayi, wolakwiridwayo amamva ululu woopsa mumtima mwake. Ndiye kodi n’chiyani chingawathandize anthu oterewa kupirira?

MAVESI AMENE ANGAKUTHANDIZENI

Ngakhale kuti zimakhala zowawa mkazi kapena mwamuna akakhala wosakhulupirika, anthu ambiri amene zoterezi zawachitikirapo aona kuti Mawu a Mulungu amathandiza kwambiri. Mawu a Mulungu awathandiza kudziwa kuti Yehova amaona kulira kwawo ndipo nayenso amamva ululu.​—Malaki 2:13-16.

“Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”​—Salimo 94:19.

Bill ananena kuti: “Nditawerenga vesi limeneli, ndinkamva ngati Yehova akunditonthoza mokoma mtima ngati mmene bambo wachikondi amachitira.”

“Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.”​—Salimo 18:25.

Carmen, amene mwamuna wake anakhala wosakhulupirika kwa miyezi ingapo, anati: “Mwamuna wanga sankakhulupirika. Koma ndinkakhulupirira kuti Yehova akhalabe wokhulupirika kwa ine ndipo sandikhumudwitsa.”

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”​—Afilipi 4:6, 7.

Sasha ananena kuti: “Lemba limeneli ndinkaliwerenga mobwerezabwereza. Ndinkati ndikapemphera, Mulungu ankandipatsa mtendere wamumtima.”

Anthu onse amene tawatchula munkhaniyi, pa nthawi ina ankaona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Koma anadalira Yehova ndipo mfundo za m’Baibulo zinawalimbikitsa. Bill anati: “Pamene zinkaoneka ngati palibenso chomwe chikuyenda, chikhulupiriro ndi chimene chinandithandiza. Zinali ngati ndikuyenda ‘m’chigwa cha mdima wandiweyani,’ koma Yehova anali nane.”​—Salimo 23:4.

a Nkhani zofotokoza ngati munthu angasankhe kukhululukira kapenanso kusakhululukira mkazi kapena mwamuna wake, zikupezeka mu Galamukani! ya May 8, 1999, yamutu wakuti, “Pamene Mwamuna Kapena Mkazi Akhala Wosakhulupirika.”

Zimene Zathandiza Ena

Kuganizira mavesi olimbikitsa.

Bill anati: “Ndinawerenga m’Baibulo buku la Yobu komanso la Masalimo ndipo ndinkadula mzere pansi pa ziganizo zomwe zikugwirizana ndi vuto langa. Ndinazindikira kuti Yobu komanso anthu amene analemba Masalimo nawonso anakumana ndi mavuto ngati anga ndipo ankada nkhawa.”

Kumvetsera nyimbo.

Carmen anati: “Usiku ndikamalephera kugona, ndinkamvetsera nyimbo ndipo ndinkaona kuti zimenezi zinkandithandiza.” Nayenso Daniel ananena kuti: “Ndinaphunzira kuimba gitala, ndipo nyimbo zinkandithandiza kukhala ndi mtendere wamumtima.”

Kufotokozera ena.

Daniel ananenanso kuti: “Poyamba sindinkakonda kuuza ena mmene ndikumvera. Koma ndinali ndi anzanga abwino ndipo tsiku lililonse ndinkacheza nawo. Kenako ndinayamba kumawafotokozera nkhawa zanga pocheza kapena pochita kuwalembera uthenga. Zimenezi zinandithandiza kwambiri.” Sasha anati: “Makolo anga anandithandiza kwambiri. Amayi ankandilimbikitsa kuti ndizimasuka kuwafotokozera chilichonse ndipo ndikamawafotokozera ankamvetsera mwachidwi. Bambonso ankandichititsa kuona kuti ndine wotetezeka ndipo ankachita nane zinthu moleza mtima.”

Kulimbikira kupemphera.

Carmen ananena kuti: “Ndinkapemphera pafupipafupi ndipo ndinkaona kuti Yehova ali pafupi nane, ankandimvetsera komanso ankandithandiza. Pa nthawi ya mavutoyi, ubwenzi wanga ndi Mulungu unalimba kwambiri.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena