Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp19 No. 2 tsamba 10-11
  • Ngati Mukudwala Matenda Aakulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngati Mukudwala Matenda Aakulu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE ZATHANDIZA ENA
  • Matenda Aakulu Ndi Nkhani ya Banja Lonse
    Galamukani!—2000
  • Ndi Motani Mmene Mungakhalire Osangalala Ngakhale Mukudwala?
    Galamukani!—2001
  • Mmene Mabanja Amapiririra Matenda Aakulu
    Galamukani!—2000
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndikudwala Chonchi?
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
wp19 No. 2 tsamba 10-11

Ngati Mukudwala Matenda Aakulu

A Linda omwe ali ndi zaka 71 ananena kuti: “Adokotala atandiuza kuti andipeza ndi khansa ya m’mapapo komanso m’matumbo, ndinangoona kuti ndiye kuti basi ndifa. Koma nditafika kunyumba, ndinadziuza kuti, ‘N’zoona kuti zimenezi si zimene ndimayembekezera, koma zateremu ndikungofunika kupeza njira yondithandiza kupirira mavuto angawa.’”

A Elise azaka 49 anati: “Ndimadwala matenda enaake opweteka kwambiri amene amachititsanso kuti mitsempha yakumanzere kwa nkhope yanga isamagwire bwino ntchito. Nthawi zina ndimavutika maganizo chifukwa choti ndimamva kupweteka kwambiri. M’mbuyomu zikatero ndinkaona kuti ndili ndekhandekha ndipo ndinkaganiza zongodzipha.”

Bambo amene akudwala ali panjinga ya olumala ndipo ali ndi anthu amene amamukonda

NGATI inuyo kapena munthu amene mumamukonda anapezeka ndi matenda aakulu, muyenera kuti mukudziwa mmene zoterezi zimapwetekera. Kuwonjezera pa matendawo, nthawi zambiri munthu amavutikanso ndi nkhawa, maganizo ofooketsa komanso amakhala ndi mantha. Zimenezi zimawonjezereka akamaganizira zoti akufunika kukaonana ndi dokotala, akamalephera kupeza thandizo loyenera la matendawo kapena ndalama zolipirira kuchipatala kapenanso akamakumana ndi mavuto ena chifukwa cha mankhwala amene akulandira. Zonsezi zikusonyeza kuti munthu amene akudwala matenda aakulu amakumana ndi mavuto ambiri.

Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi zoterezi? Anthu ambiri amaona kuti akamadalira Mulungu n’kumapemphera kwa iye komanso kuwerenga mavesi olimbikitsa a m’Baibulo, zimawathandiza. Tingapezenso thandizo kuchokera kwa achibale komanso anzathu omwe amatikonda.

ZIMENE ZATHANDIZA ENA

A Robert azaka 58 ananena kuti: “Muzidalira Mulungu ndipo adzakuthandizani kuti mupirire. Muzipemphera kwa iye n’kumuuza mmene mukumvera. Muzimupemphanso kuti akupatseni mzimu woyera komanso mphamvu kuti muzilimbikitsa banja lanu ndiponso kuti muthe kupirira.”

A Robert ananenanso kuti: “Zimakhala zothandiza anthu a m’banja lako akamakulimbikitsa kuti usamade nkhawa. Tsiku lililonse munthu mmodzi kapena awiri amandiimbira foni n’kundifunsa kuti, ‘Lero mwadzukako bwanji?’ Komanso anzanga amene amakhala m’madera osiyanasiyana amandilimbikitsa. Zimenezi zimandipatsa mphamvu komanso zimachititsa kuti ndizimvako bwino.”

Mukapita kukaona mnzanu amene akudwala muzikumbukira zimene a Linda ananena. Iwo anati: “Munthu amene akudwala amafuna kuti azikhala ngati munthu wina aliyense ndipo nthawi zambiri safuna kuti muzingokambirana za matenda akewo. Choncho yesetsani kuti muzicheza naye nkhani zina.”

Mothandizidwa ndi Mulungu, mfundo za m’Baibulo, achibale komanso anzathu, tingakwanitse kupirira n’kumaona kuti tingathe kupitirizabe kukhala ndi moyo ngakhale kuti tikudwala matenda aakulu.

Mavesi Amene Angakuthandizeni

Muzidalira Mulungu.

“Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha, pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa. Wosautsikayu anaitana ndipo Yehova anamva.”​—Salimo 34:4, 6.

A Linda amene tawatchula kale aja anati: “Sindipemphera kuti, ‘Ndichiritseni.’ Nthawi zonse ndimapemphera kuti, ‘Mundipatse mphamvu komanso mundithandize kupirira matenda angawa.’”

Muziwerenga Mawu a Mulungu kuti mupeze mphamvu.

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

Muziganizira zimene Mulungu walonjeza kuti adzachita m’tsogolo. Zimenezi zidzakuthandizani kupeza mphamvu kuti muthe kupirira.

Muzipempha achibale komanso anzanu kuti akuthandizeni.

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.

A Elise amene tawatchula kale aja ananena kuti: “Musamadzipatule. Muzilola kuti anzanu akuthandizeni. Nthawi zina mungamaone kuti muli nokha ndipo Mulungu sakumvetsera pemphero lanu, komabe musamadzipatule.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena