Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp19 No. 3 tsamba 14-15
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUKHALA WOKHUTIRA
  • NGATI MUKUDWALA
  • KULIMBITSA BANJA
  • Makiyi Aŵiri a Ukwati Wokhalitsa
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kumaumanga Moyo Wabanja Wacimwemwe
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Mwetulirani—N’zothandiza kwa Inu!
    Galamukani!—2000
  • Magwero Apamwamba Kwambiri a Nzeru
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
wp19 No. 3 tsamba 14-15
Mmodzi mwa asayansi amene atchulidwa poyamba aja, akuphikira limodzi chakudya ndi mkazi wake

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala

INUNSO mungathe kudzakhala ndi moyo wopanda matenda, ukalamba komanso imfa. Koma panopa moyo ndi wa mavuto okhaokha. Ndiye kodi mungatani kuti muzikhala wosangalala? M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni. Tiyeni tione mmene Baibulo lingatithandizire kukhala osangalala.

KUKHALA WOKHUTIRA

Malangizo a m’Baibulo: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”—Aheberi 13:5.

Masiku ano pali zinthu zambiri zimene anthu a m’dzikoli amati tiyenera kukhala nazo. Koma Baibulo limanena kuti mungathe kumakhala “okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” Ndiye kodi mungatani kuti muzikhala okhutira?

Muzipewa “kukonda ndalama.” Anthu ena amalolera kuwononga thanzi lawo, kusokoneza banja lawo, kudana ndi anzawo, kuchita makhalidwe oipa kapenanso kudzichotsera ulemu chifukwa ‘chokonda ndalama.’ (1 Timoteyo 6:10) Komatu kumeneku n’kupanda nzeru. Ndipo anthu oterewa pamapeto pake amakhalabe ‘osakhutira.’​—Mlaliki 5:10.

Muziona kuti anthu ndiye ofunika kwambiri. N’zoona kuti zinthu zina zomwe tili nazo ndi zothandiza. Koma zinthu zimenezi sizingatikonde kapena kutiyamikira. Anthu ndi amene angachite zimenezi. Kukhala ndi “bwenzi lenileni” kumatithandiza kuti tizikhala okhutira.​—Miyambo 17:17.

TIKHOZA KUMASANGALALA NGATI TIMATSATIRA MALANGIZO A M’BAIBULO

NGATI MUKUDWALA

Malangizo a m’Baibulo: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”​—Miyambo 17:22.

Mofanana ndi “mankhwala ochiritsa,” kukhala osangalala kungatithandize kupirira matenda. Koma kodi munthu angakhale bwanji wosangalala ngati akudwala?

Muzikhala ndi mtima woyamikira. Tikamangoganizira za mavuto athu, “masiku onse” akhoza kumangokhala oipa. (Miyambo 15:15) Koma Baibulo limatiuza kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akolose 3:15) Phunzirani kumayamikira pa zinthu zabwino, ngakhale zitakhala zing’onozing’ono. Zinthu monga kuona mmene kumwamba kumakongolera dzuwa likamalowa, kamphepo kayeziyezi komanso munthu amene timam’konda akatimwetulira, zimatithandiza kukhala osangalala.

Muzithandiza ena. Ngakhale zitakhala kuti tikudwala tizikumbukira kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Anthu ena akatiyamikira pa zimene tawachitira, timasangalala kwambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti tiiwaleko mavuto athu. Tikamathandiza ena kuti azisangalala nafenso timasangalala.

KULIMBITSA BANJA

Malangizo a m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

Anthu okwatirana amene sakhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu limodzi akhoza kusokoneza banja lawo. Choncho mwamuna ndi mkazi angachite bwino kumaona kuti banja lawo ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri.

Muzichita zinthu limodzi. M’malo momangochita panokha zinthu zimene zimakusangalatsani, mungachite bwino kukonza zoti muzichitira limodzi zinthu. Baibulo limati: “Awiri amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Mukhoza kumachitira limodzi zinthu monga kuphika chakudya, kuchita masewera olimbitsa thupi, kumwa zakumwa zoziziritsa kukhosi kapenanso kuchitira limodzi zinthu zina zimene mumakonda.

Muzisonyezana chikondi. Baibulo limati anthu okwatirana ayenera kumakondana komanso kulemekezana. (Aefeso 5:28, 33) Zinthu monga kumwetulirana mwachikondi, kukumbatirana kapenanso kupatsana timphatso zimalimbitsa banja. Komanso anthu okwatirana sayenera kusonyeza anthu ena chikondi chimene amafunika kusonyeza mwamuna kapena mkazi wawo yekha.​—Aheberi 13:4.

“PANOPA MOYO WANGA ULI NDI CHOLINGA”

​—Yofotokozedwa ndi a Ryoko Miyamoto a ku Japan.

Tinkakumana ndi mavuto ambiri. Mwamuna wanga anali chidakwa ndipo chifukwa cha zimenezi ntchito sinkachedwa kumuthera. Komanso ankakana kusamalira ana athu 4. Ngakhale kuti ndinkayesetsa kugwira ntchito mwakhama, palibe chimene chinkayenda. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi limeneli ndi tsoka? Kapena ndikulangidwa chifukwa cha machimo amene ndinachita m’mbuyomu?’

Kenako kunyumba kwathu kunabwera wa Mboni. Anandiuza za Ufumu wa Mulungu komanso moyo wosatha ndipo ankalankhula akumwetulira ndiponso mosonyeza kuti zomwe akunenazo amazikhulupirira. Kenako anandipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo. Pasanapite nthawi ndinaphunzira kuti kuli Mulungu ndipo ndi wanzeru, wachilungamo komanso wachikondi. Ndinaphunziranso zimene zimachitika munthu akamwalira ndiponso zoti sindinkavutika chifukwa choti ndili ndi tsoka.

Koposa zonse, ndinazindikira kuti munthu amakhala wosangalala akakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Kudziwa choonadi cha m’Baibulo kwandilimbikitsa, kwandipatsa ufulu komanso kwandithandiza kukhala wosangalala. Panopa moyo wanga uli ndi cholinga.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena