Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w19 June tsamba 31
  • Akwanitsa Kuwerenga Mpukutu Wakale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akwanitsa Kuwerenga Mpukutu Wakale
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mipukutu Inafikira Pokhala Baibulo Lathunthu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Mpukutu Wotchedwa “Nyimbo ya Panyanja” Umatithandiza Kudziwa Zinthu Zakale
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Tsiku Lopereka Chiweruzo la Mulungu Lidzabweretsa Madalitso Osangalatsa Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
w19 June tsamba 31
Mpukutu wa ku Ein Gedi womwe unapsa; zinali zosatheka kuwerenga chidutswa cha mpukutu wa ku Ein Gedi

Akwanitsa Kuwerenga Mpukutu Wakale

Zinali zosatheka kuwerenga mawu apachidutswa cha mpukutu wakupsa chimene chinapezeka ku Ein Gedi mu 1970. Koma njira yatsopano yochitira sikani zinthu yathandiza kudziwa kuti muli mavesi a Levitiko komanso dzina la Mulungu

MU 1970, asayansi anafukula mpukutu wakupsa ku Ein Gedi m’dziko la Israel chakumadzulo kwa Nyanja Yakufa. Mpukutuwu anaupeza pofukula sunagoge amene anawotchedwa pa nthawi imene mudzi wina wam’deralo unawonongedwa, mwina m’zaka za pakati pa 500 ndi 550 C.E. Mpukutuwu unapsa kwambiri moti zinali zosatheka kuutambasula komanso kuuwerenga. Koma panopa asayansi akwanitsa kuona zimene zili mkati mwake pogwiritsa ntchito njira yamakono yochitira sikani zinthu. Iwo akwanitsa kuwerenga zimene zinalembedwa mumpukutuwu pogwiritsa ntchito pulogalamu yatsopano yapakompyuta.

Kodi mumpukutuwu mwapezeka zotani? Apeza kuti mumpukutuwu muli malemba ena a m’Baibulo. Kachidutswa kamene kanatsala kakusonyeza mavesi ena akumayambiriro kwa buku la Levitiko. M’mavesi amenewa mukupezekanso zilembo zinayi zachiheberi zoimira dzina la Mulungu. Zikuoneka kuti mpukutuwu unalembedwa m’zaka zapakati pa 50 ndi 400 C.E. Choncho umenewu ndi mpukutu wakale kwambiri wa Malemba Achiheberi womwe wapezeka pambuyo pa mipukutu imene inapezeka pafupi ndi Nyanja Yakufa. Munthu wina dzina lake Gil Zohar analemba munyuzipepala ina (The Jerusalem Post) kuti: “Mpukutu wokhala ndi mavesi a m’buku la Levitikowu usanapezeke, mipukutu yakale imene inalipo inali yomwe inapezeka pafupi ndi Nyanja Yakufa komanso wina wotchedwa Aleppo Codex. Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inalembedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo cha m’ma 100 B.C.E. Pomwe wotchedwa Aleppo Codex unalembedwa cha m’ma 930 C.E. Choncho tingati pakati pake panadutsa zaka 1,000. Koma panopa tili ndi mpukutu wina wakale womwe unapezeka ku Ein Gedi uja.” Akatswiri ena akunena kuti mpukutuwu ukusonyeza kuti uthenga wa m’mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo sunasinthe ngakhale kuti panapita zaka zoposa 1,000 ndipo Amasoreti sanakopere Baibulo molakwika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena