Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/04 tsamba 6
  • Thandizani Ana Kupindula Kwambiri ndi Misonkhano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ana Kupindula Kwambiri ndi Misonkhano
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Yehova Akutitsogolera
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakuthandizeni Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Mumathandiza Kuti Misonkhano Yachikhristu Ikhale Yolimbikitsa?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 12/04 tsamba 6

Thandizani Ana Kupindula Kwambiri ndi Misonkhano

1 Kodi ana anu amamvetseradi akakhala pa misonkhano? Kodi angakwanitse kukufotokozerani panthawi ina zimene anaphunzira pamsonkhano uliwonse? Kodi mumawalimbikitsa kumvetsera mwatcheru ndi kugwiritsa ntchito zimene aziphunzira poonetsetsa zochitika kumeneko? Kodi mwa mayankho anu pamisonkhano mumawasonyeza chitsanzo chabwino choti angaonere, kumva, ndi kutha kuchitsanzira? Kodi ana anu amatsanzira chikhulupiriro chanu? Mayankho oti inde pamafunso amenewa n’ngofunika kwambiri ngati ana ati adzakule n’kukhala atumiki odzipereka a Yehova.

2 Khomerezani mwa Iwo Kuti Kupezeka pa Misonkhano N’kofunika Kwambiri: Mwana amafunika malangizo ochokera m’Baibulo kuti adzakhale ndi moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kuti mwana wanu aphunzire kuyamikira zinthu zauzimu, afunika kumapezeka pa misonkhano nthawi zonse. Koma nthawi zina, makolo safuna kutenga ana awo kupita nawo ku misonkhano chifukwa amaopa kuti anawo azikasokoneza anthu ena. Makolo ena amasiya ana awo kunyumba kuti alemberetu homuweki ya kusukulu. Koma kholo lanzeru, limapita ndi ana ake ku misonkhano.—Deut. 31:12.

3 Chinthu choyambirira chimene mwana ayenera kuphunzira adakali wamng’ono ndicho kudziwa kuti amapita ku Nyumba ya Ufumu kukamvetsera. Koma ngati amapatsidwa zinthu zoti azitanganidwa nazo, zinthu monga zoseweretsa kapena zakudya, kapena ngati amaloledwa kumasewera pamalo pamene wakhala, kodi angaphunzire kumvetsera ndi kuzindikira chifukwa chake timapita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu? N’zoona kuti ana ena amakhala atcheru kwambiri kusiyana ndi ena. Komabe, ngati mwana akuchita zopulupudza, kholo lanzeru limamuwongolera ndi kum’phunzitsa mwachikondi kumvetsera, osati mwa kum’nyengerera ndi maswiti kapena zoseweretsa, koma mwa kugwiritsa ntchito uphungu wa m’Mawu a Mulungu.—Miy. 13:24; Aef. 6:4.

4 Chitsanzo Chanu Monga Kholo: Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 15, 1982, patsamba 17, inafunsa mafunso otsatirawa: “Kodi ana anu amadziwa kuti mumaona misonkhano yophunzira Baibulo kukhala yofunika kwambiri? Kodi anawo amatha kuona kuti mumaona misonkhano kukhala yofunika kwambiri osati mwa kungopezekapo kokha koma mwa kutenga nawo mbali, kupereka ndemanga ngati pakufunikira kutero?” Ngati ana anu amakuonani mukungocheza misonkhano ili m’kati kapena ngati inuyo kapena anthu ena mumasewera ndi ana nthawi ya misonkhano, kodi mukuganiza kuti zimenezi zidzapereka chithunzi chotani kwa iwo? Kodi nthawi ya misonkhano adzaiona ngati nthawi yotani? Popeza kuti ana sachedwa kutengera zinthu, dziwani kuti iwo adzatengera kwambiri chitsanzo chanu.

5 Makolo ena aona kuti zimathandiza kwambiri kupatsa ana awo ngakhale aang’ono buku lawolawo limene likuphunziridwa pamisonkhano. Paphunziro la banja, amathandiza ana awo kukonzekera ndemanga zogwirizana ndi msinkhu wawo. Makolo angalimbikitsenso ana awo mwa kubwereza mfundo zimene zinakambidwa ku misonkhano ndiponso mwa kuwayankha mafunso amene angakhale nawo. Makolo ayeneranso kukhala okonzeka kuyamikira ana awo chifukwa chotenga nawo mbali pa misonkhano.

6 N’zoona kuti makolo afunika kuchita khama kuti aphunzitse ana mwanjira imeneyi. Koma kuchita zinthu m’njira ya Mulungu kumakhala ndi zotsatirapo zabwino. Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi mmene lembali limanenera kuti: ‘Wolungama woyenda mwangwiro, ana ake adala pambuyo pake.’—Miy. 20:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena