Konzekeretsani Ophunzira Baibulo kaamba ka Utumiki
1 Chonulirapo chachikulu m’kuchititsa maphunziro a Baibulo ndicho kupanga ophunzira atsopano, antchito amene adzagwirizana nafe m’kuphunzitsa ena. (Mat. 28:19, 20) Chotero chifuno cha phunziro sichili cha kungogaŵira chidziŵitso; chiyenera kukhala cha kusonkhezera chikhulupiriro cha mumtima wonse mwa ophunzira athu ndi kuwakonzekeretsa kunena za chiyembekezo chawo kwa ena. (2 Akor. 4:13) Kodi ndi njira zotani zogwira ntchito zimene tingawathandizire nazo kukhala oyenerera kuphunzitsa ena?—2 Tim. 2:2.
2 Ikani Utumiki Monga Chonulirapo: Kuyambira pachiyambi penipeni, mveketsani bwino lomwe kuti kulambira koona kumaphatikizapo “chilengezo chapoyera cha chipulumutso.” (Aroma 10:10, NW) Dzina lathu lenilenilo, Mboni za Yehova, limapereka lingaliro lakuti tiyenera kulankhula kwa ena. Athandizeni kuona kuti kuphunzitsidwa kwawo sikuli chabe kaamba ka chipulumutso chawo. Pamene akhala aphunzitsi iwo eniwo, awo amene amawamvetsera nawonso ali ndi mwaŵi wa kupeza chipulumutso.—1 Tim. 4:16.
3 Pendani Zimene Zikuphunziridwa: Kupenda kwa nthaŵi ndi nthaŵi zimene zaphunziridwa kuli chithandizo china chopindulitsa chophunzitsira. Kumathandiza wophunzira kukula mwauzimu pamene choonadi chongophunziridwa kumene chikhomerezeka m’maganizo mwake ndi mumtima. Taona zimenezi ife enife poyankha mafunso openda amene amaphatikizidwa m’Phunziro la Nsanja ya Olonda. Linganizani mafunso osavuta ndi achindunji kuti wophunzira wanu ayankhe m’mawu ake.
4 Kupenda kwanu mungakuchite mumkhalidwe wa utumiki wakumunda. Funsani funso kapena fotokozani mkhalidwe wina wofala umene umapezeka pochitira umboni kwa ena. Inuyo mukumachita monga ngati mwininyumba, lolani wophunzira wanuyo kuti asonyeze zimene anganene. Muyamikireni pa zimene wachita bwino, ndipo m’patseni malingaliro ena opindulitsa amene adzamthandiza kukhala wogwira mtima kwambiri panthaŵi yotsatira. Kuyeseza kumeneku kudzamphunzitsa mmene angagwiritsire ntchito zimene waphunzira ndipo kudzakulitsa luso lake logwiritsira ntchito Baibulo.
5 Buku la Kukambitsirana: Tsimikizirani kuti wophunzira wanuyo ali ndi kope la buku la Kukambitsirana, ndipo m’phunzitseni mmene angaligwiritsirire ntchito. Sonyezani mmene limaperekera malingaliro akuyambitsa makambitsirano, kuyankha mafunso a Baibulo, kapena kuchita ndi zitsutso. Gwiritsirani ntchito bukulo pa phunziro kusonyezera njira zolankhulira kwa ena m’njira yokhutiritsa maganizo. Buku limeneli lingakulitse chidaliro chake, kuwonjezera luso lake la kulengeza uthenga wa Ufumu.
6 Gogomezerani Kufunika kwa Misonkhano: Misonkhano yampingo, makamaka Msonkhano Wautumiki ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki, yalinganizidwira kutikonzekezeretsa kaamba ka utumiki wakumunda. Mfundo zonse zazikulu za kuchitira umboni kogwira mtima zimapendedwa ndi kusonyezedwa ndi awo amene ali ndi chidziŵitso ndi luso. Gogomezerani kufunika kwa misonkhano, ndipo chitani zimene mungathe kumthandiza kufikapo. Kufika nthaŵi zonse pamisonkhano kungapatse wophunzira wanu chisonkhezero chimene akufunikira kuti akhale wophunzira weniweni wa Yesu.
7 Chinthu china chosafunika kunyalanyazidwa ndicho chitsanzo cha inu mwini. Kufunitsitsa kwanu ndi kukhala wokhazikika m’ntchito yolalikira kumasonyeza chiyamikiro chanu chachikulu kaamba ka choonadi. Njira yotero imalimbikitsa wophunzira wanu kuchita zowonjezereka kuti asonyeze chikhulupiriro chake. (Luka 6:40) Zonsezi zingathandize munthu watsopano kuona utumiki monga mwaŵi ndi kukhala woyamikira kuchita mbali yake.—1 Tim. 1:12.