Ocheperapo Msinkhu Amafuna Chitsanzo Chabwino
1 Tikusangalala kukhala ndi chiŵerengero chomakula cha anthu achichepere amene ‘akulemekeza dzina la Yehova.’ (Sal. 148:12, 13) Ambiri a iwo adakali aang’ono kwambiri m’zaka. Kupita kwawo patsogolo kwakukulukulu kumachititsidwa ndi maphunziro ndi chitsanzo choperekedwa ndi makolo awo ndi achikulire ena mu mpingo. Komabe, chinthu chosayenera kunyalanyazidwa ndicho chisonkhezero choperekedwa ndi anthu achichepere ena, makamaka achinyamata osinkhukirapo ndi achikulirepo ena. Ngati muli m’gulu limeneli la msinkhu, ndemanga izi zingakupindulitseni.
2 Achichepere m’zaka zawo zaubwana amakhala okhoterera pa kutsanzira achinyamata osinkhukirapo. Ali ndi chikhumbo chachibadwa cha kukhala ofanana ndi mabwenzi apafupi amene amachita nawo kaso. Amakonda kulemekeza achichepere ena amene ali osinkhukirapo ndi amene amaonekera kukhala achidziŵitso ndi aluntha kwambiri. Monga chotulukapo chake, iwo angatsanzire kalankhulidwe kanu ndi khalidwe ndiponso kuyamikira kwanu zinthu zauzimu ndi kukhala kwanu ndi phande mu ntchito za mpingo.
3 Monga wachinyamata wosinkhukirapo, muli ndi mwaŵi ndiponso thayo lolemera. Panthaŵi inoyo, chitsanzo chanu mwinamwake chikusonkhezera mabwenzi anu ocheperapo msinkhu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nchisonkhezero chotani chimene ndimapereka kwa ocheperapo msinkhu? Kodi ndilibe chibwana, ndi kumapeŵa kupusa ndi “zilakolako zaunyamata” zolakwa? Kodi ndimasonyeza kumvera ndi ulemu kwa makolo anga, akulu, ndi anthu ena achikulire?’ (2 Tim. 2:22; Akol. 3:20) Zimene mumanena ndi kuchita zingakhale ndi mbali yaikulu m’kupita patsogolo kwauzimu kwa ocheperapo msinkhu ena amene amaona zochita zanu.
4 Kulalikira uthenga wa Ufumu kuli ntchito yaikulu ya mpingo. Kukhalamo kwanu ndi phande mofunitsitsa ndi mwanthaŵi zonse kungalimbikitse mabwenzi anu kukhala okangalika kwambiri. Ngati muli wokhoza kuloŵa utumiki waupainiya, mabwenzi anu adzasonkhezeredwa mofananamo. Kupereka ndemanga pamisonkhano ndi kudzipereka kuthandiza m’kuchita ntchito zofunika pa Nyumba Yaufumu kungaikenso chitsanzo chabwino.
5 Ngakhale kuti Timoteo sanalinso m’zaka zake za pakati pa 13 mpaka 19 pamene Paulo anampatsa uphungu wotsatirawu, inu azaka za pakati pa 13 mpaka 19 mungathe kuugwiritsira ntchito: “Khala chitsanzo kwa iwo okhulupira, m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.” (1 Tim. 4:12) Kukhala ndi phande kwanu kwachangu ndi kwa mtima wonse mu utumiki wa Yehova kungasonkhezere oyanjana nanu ndi okupenyani ocheperapo msinkhu m’njira yomangirira, kuwathandiza kupanga kupita patsogolo kulinga kukukhala amuna aakulu msinkhu mwauzimu. (Aef. 4:13) Azaka za pakati pa 13 mpaka 19 amene ali mbali ya mabanja amene angoyamba kumene kuphunzira angakopedwe kuloŵa m’choonadi ndi zimene amaona mwa inu.
6 Chofunika koposa nchakuti, khama lanu m’kusonyeza mikhalidwe yaumulungu limalemekeza Yehova ndi gulu lake. (Miy. 27:11) Openyerera oona mtima adzadabwa ndi kusiyana kwakukulu pakati panu ndi achichepere a dziko. Chotero muli ndi mpata wapadera wa kuthandiza ocheperapo msinkhu pamene mukupereka chichirikizo chofunika ku chitamado cha Yehova.—Sal. 71:17.