Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndimotani mmene tingaperekere ndemanga mogwira mtima koposa pamisonkhano?
Timayembekezera mwachisangalalo kusonkhana pamodzi pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu. Pamenepo timakhala ndi mwaŵi wa kusonyeza chikhulupiriro chathu ndi kulimbikitsa ena mwa kupereka ndemanga kwathu. (Miy. 20:15; Aheb. 10:23, 24) Tiyenera kuona kupereka ndemanga monga mwaŵi ndi kuyesetsa kukhala ndi phande nthaŵi zonse. Kodi ndimotani mmene tingachitire zimenezi mogwira mtima koposa?
Sitepe yoyamba ndiyo kukonzekera. Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pankhaniyo pasadakhale nkofunika. Yesani kupeza tanthauzo la zimene zikunenedwa. Ngakhale kuti nkhaniyo ingakhale itakambitsiridwapo kumbuyoku, funafunani mfundo zilizonse zimene zikulongosoledwa mowonjezereka m’nkhaniyo. Musaiŵale mutu wa nkhani yonseyo. Pokonzekera ndemanga za m’chofalitsidwa chimene chili ndi phunziro lakuya la buku la Baibulo, monga ngati buku la Revelation Climax, yesani kuona mmene vesi lakutilakuti likugwirizanira ndi mavesi ena a m’nkhaniyo. Kutsatira malingaliro ameneŵa kudzasonkhezera luso lanu la kuganiza. Kudzakuthandizani kukonzekera ndemanga zabwino ndi kupeza chimwemwe m’kukhalamo ndi phande kwanu.
Ndemanga zabwino koposa ndizo zazifupi, zofotokozedwa mosavuta, ndi zozikidwa m’chofalitsidwa chimene chikuphunziridwacho. Wopereka ndemanga woyamba ayenera kuyankha funso mwachindunji, akumasiya mfundo zina kuti enanso apereke ndemanga. Peŵani ndemanga zazitali, zosatha zimene zimadya nthaŵi yochuluka ndi kutsekereza ena kuyankha. Fotokozani momasuka m’mawu a inu eni, m’malo mwa kuŵerenga ndemanga yanu liwu ndi liwu m’chofalitsidwacho. Ndemanga zowonjezera zingaphatikizepo mfundo zimene zikufotokozedwa m’Malemba osonyezedwa. Mvetserani mosamalitsa zimene ena akunena kuti mupeŵe kuzibwerezanso kosafunikira.
Kuli bwino kutukula mkono wanu kangapo komano osati pa ndime iliyonse. Tikupempha achichepere kuti nawonso azipereka ndemanga. Ngati muli wamantha pa kukambapo, mungadziŵitse wochititsa phunzirolo pasadakhale za ndime imene mudzakonda kuperekerapo ndemanga, ndipo iye mwachionekere adzakhoza kukupatsani mwaŵi wa kuchita motero.
Tonsefe tiyenera kuyesayesa mwakhama kukhala ndi kanthu kena kogaŵana ndi ena pamisonkhano ya mpingo imene imafuna ndemanga za omvetsera. Kumbukirani kuti, chipambano cha misonkhano yotero kwakukulukulu chimadalira pa kufunitsitsa kwathu ndi kugwira mtima kwathu m’kupereka ndemanga.—Sal. 26:12.