Msonkhano Wachigawo Upereka Chiitano Chosonkhezera!—Tamandani Yehova Mwachimwemwe Tsiku ndi Tsiku!
1 “Ngati lipenga lipereka mawu osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?” anafunsa motero mtumwi Paulo. (1 Akor. 14:8) Kodi chiitano chimene chinaperekedwa pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” chinali chachikulu ndi chomveka? Indedi. Uthenga wake wosonkhezera unali wakuti ‘Tamandani Yehova mwachimwemwe tsiku ndi tsiku’! Kodi mtima wanu unasonkhezeredwa ndi chiitano chimenechi cha kuchitapo kanthu? Programu ya msonkhanowo inali ndi zifukwa zamphamvu zambiri za kutamandira kwathu Yehova, Mfumu yamuyaya nthaŵi zonse.—Sal. 35:27, 28.
2 Thambo lochititsa mantha limalengeza ulemerero wa Yehova “usana ndi usana.” (Sal. 19:1-3) Ngati zinthu zolengedwa zopanda moyo ndi zosalankhula zimatamanda Yehova nthaŵi zonse, kodi anthu anzerufe sitiyenera kusonkhezeredwa kufuula momtamanda nthaŵi zonse chifukwa cha mikhalidwe ndi zochita zake zosayerekezeka? Kodi ndaninso ali woyenerera chitamando chathu chachimwemwe koposa Mlengi wathu wabwino kwambiriyo?—Sal. 145:3, 7.
3 Tsiku ndi Tsiku: Wamasalmo wouziridwayo analemba kuti: “Lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu.” (Sal. 96:2, 4) Kodi zimenezi zimangokhudza apainiya okha? Ayi! Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tonsefe tiyenera kuuza ena za Yehova panthaŵi iliyonse ndi kumalo alionse amene tili, ngakhale pamasiku amene sitili mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba? Inde! Kufunika kwa kutamanda Yehova tsiku ndi tsiku ndi kuuza ena za njira yake ya chipulumutso nkofulumira. Anthu afunikira kudziŵa kuti Yehova ndiye Mfumu Yamuyaya ndi kuti Iye wapereka ulamuliro wa dziko kwa Mwana Wake wolemekezeka, Yesu Kristu. Kukonda Yehova ndi anthu kudzatichititsa kunena za uthenga umenewu ndi za makonzedwe ake a chipulumutso paliponse pamene tipeza anthu.—Sal. 71:15.
4 Tsiku lililonse la utumiki wake wa pa dziko lapansi, Yesu Kristu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri monga wotamanda Yehova wosabisa mawu. Iye anati: “[Ndikutamandani poyera, NW ], Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi.” (Mat. 11:25) Mogwirizana ndi mawu ake, kulikonse kumene Yesu anali, anatamanda Yehova poyera. Ndipo kulikonse kumene makamu anasonkhana—kaya m’masunagoge, pakachisi mu Yerusalemu, pa phiri, kapena m’mphepete mwa nyanja—anatamanda Yehova. Ngati titsatira kwambiri mapazi a Yesu mwa kuchita ntchito mosalekeza tsiku ndi tsiku ya kutamanda Yehova poyera, tidzalandira zipatso zosangalatsa.
5 Kuyankha Chiitanocho: Kodi mudzayankha chiitano cha kutamanda Yehova poyera tsiku lililonse? Kumbukirani, usinkhu suli chinthu chopinga. Salmo 148:12 limapempha anyamata, anamwali, nkhalamba, ndi ana kutamanda Yehova. Ananu, kodi mudzatamanda Yehova pakati pa anzanu akusukulu ndi aphunzitsi mkati mwa chaka chino cha sukulu? Inu anthu achikulire, kodi amene mumagwira nawo ntchito kuntchito kwanu akumva za Yehova ndi zifuno zake, pamene muli ndi mpata wa kulankhula nawo? Tonsefe tiyenera kupanga kulankhula za Yehova kukhala mbali yathu yaikulu ya moyo wathu monga mmene kulili kupuma ndi kudya. Ngakhale ngati anthu amphwayi samvetsera zimene timanena, pali Uyo amene amatero, ndipo adzatifupa.—Mal. 3:16.
6 Pamene mapeto a dongosololi ayandikira, chiitanocho chikufika kumalekezero a dziko lapansi: “Haleluya.” (Sal. 106:1) Mfuu yathu yachitamando ikhaletu ikukulabe pamene tsiku lililonse likupyola kotero kuti onse adziŵe kuti Uyo amene dzina lake ndi Yehova ndiye Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.—Sal. 83:18.