Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/95 tsamba 7
  • Mpingo Uli Wofunika kwa Ife

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mpingo Uli Wofunika kwa Ife
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Mpingo Uyenera Kutamanda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Mpingo Uyenera Kulimbikitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Ndinu Amtengo Wapatali Mumpingo wa Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Yamikirani Malo Anu Mumpingo wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 10/95 tsamba 7

Mpingo Uli Wofunika kwa Ife

1 Ana a Kora nthaŵi ina anasonyeza chiyamikiro chawo kaamba ka mpingo wa Yehova motere: “Tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.” (Sal. 84:10) Kwa iwo, palibe chimene dziko likanawapatsa cholingana ndi zimenezo. Ngati inunso muli ndi maganizo amenewo, muyenera kusumika moyo wanu wonse pa mpingo.

2 Kuchokera pamene unayamba, mpingo Wachikristu wasonyeza kuti uli ndi dalitso la Yehova. (Mac. 16:4, 5) Yense wa ife sayenera kuona mpingo mopepuka kapena kuganiza kuti wangokhala chabe njira ya kuyanjana pamodzi. Mpingo ndiwo malo kolimbitsira Mboni za Yehova m’dera lililonse. Umatitheketsa kukhala ndi mayanjano a chigwirizano kotero kuti tiphunzitsidwe ndi Yehova ndi kukhala okonzeka kuchita ntchito ya Ufumu.—Yes. 2:2.

3 Mpingo Wachikristu ndiwo njira yaikulu yotiphunzitsira choonadi. (1 Tim. 3:15) Otsatira a Yesu onse ayenera kukhala “amodzi”—ogwirizana ndi Mulungu, ndi Kristu, ndi wina ndi mnzake. (Yoh. 17:20, 21; yerekezerani ndi Yesaya 54:13.) Kulikonse kumene tingapite m’dziko, abale athu amakhulupirira ziphunzitso ndi miyezo ya Baibulo, ndipo amazitsatira.

4 Timaphunzitsidwa ndi kukonzekeretsedwa kukwaniritsa ntchito yathu yopanga ophunzira. Mwezi uliwonse, Nsanja ya Olonda, Galamukani!, ndi Utumiki Wathu Waufumu zimakhala ndi mawu otithandiza kuyambitsa makambitsirano a m’Malemba. Misonkhano imakonzedwa mwa njira yakuti itisonyeze mmene tingapezere anthu ndi kukulitsa chidwi chawo. Chiwonjezeko chimene tikuona padziko lonse chikusonyeza kuti Mulungu akutichirikiza pantchitoyi.—Mat. 28:18-20.

5 Kupyolera mumpingo, timalandira chilimbikitso tsiku ndi tsiku ‘chotifulumiza ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24, 25) Timalimbitsidwa kupirira mayesero mokhulupirika. Oyang’anira achikondi amatithandiza kulimbana ndi mavuto ndi nkhaŵa. (Mlal. 4:9-12) Timapatsidwa uphungu wofunika tikakhala pangozi ya kusokera. Kodi pali gulu lina limene limasamalira ena mwachikondi chonchi?—1 Ates. 5:14.

6 Yehova akufuna kuti tikhale pafupi ndi gulu lake kuti tisunge umodzi wathu. (Yoh. 10:16) Njira ina imene mpingo umatithandizira kukhala ogwirizana ndi kagulu ka kapolo wokhulupirika ndiyo kutumiza oyang’anira oyendayenda kudzatilimbikitsa. Kutsatira kwathu chitsogozo chachikondi kumatigwirizanitsa pamodzi pa unansi umene umatithandiza kukhalabe olimba mwauzimu.

7 Mpingo uli wofunika kwambiri kuti tikhalebe amoyo mwauzimu. Sikungatheke kutumikira Yehova movomerezeka popanda uwo. Choncho, tiyeni tikhale pafupi ndi chimene Yehova wapereka. Tiyeni tichite mogwirizana ndi zonulirapo zake ndi kugwiritsira ntchito moona mtima uphungu umene timalandira. Iyi ndiyo njira yokha imene tingasonyezere mmene mpingo ulili wofunika kwa ife.—Sal. 27:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena