Nthaŵi Zasintha
1 Baibulo limatiuza kuti “mkhalidwe wa dzikoli ukusintha.” (1 Akor. 7:31, NW) Zimenezotu nzoona kwambiri! Ngakhale m’moyo wathu, taona kusintha kwakukulu kwa malingaliro ndi khalidwe la anthu m’mbali iliyonse ya chitaganya cha anthu. Kuti tikhoze kuwafika ndi uthenga wa Ufumu, kafikidwe kathu kakhale kogwirizana ndi nthaŵi zomasinthazi. Tiyenera kupereka uthenga wabwino mwa njira yakuti isangalatse anthu ndi kuwafika pamtima.
2 Zaka zapitazo, m’maiko ambiri ntchito ya umboni inali yovuta chifukwa, kwenikweni, anthu anali ndi moyo wabata, ndipo anali kumva kukhala otetezereka. Chipembedzo chinali ndi malo opatulika m’moyo wawo. Baibulo anali kulilemekeza kwambiri. Masiku amenewo umboni nthaŵi zambiri unali wakupereka zigomeko zotsutsa ziphunzitso. Lerolino, moyo wa anthu uli pa mavuto. Chipembedzo amachinyoza. Oŵerengeka ndiwo amakhulupirira Baibulo. Ndipo ambiri, chiphunzitso cha chisinthiko chawawonongera chikhulupiriro mwa Mulungu.
3 Woyang’anira woyendayenda wina anati: “Tsopano zikuoneka kuti pali mavuto ndi zothetsa nzeru zochuluka kwambiri m’moyo wa anthu kwakuti tiyenera kuwaphunzitsa mokhalira ndi moyo.” Mwachibadwa nkhani zazikulu zimene anthu amafuna tsopano ndi zija zokhudza iwo, mabanja awo, ndi nkhaŵa zawo. Izi ndizo zimene amakambitsirana kwambiri atakhala pamodzi. Tifunikira kukumbukira zimenezo pamene tili m’ntchito yathu ya umboni.
4 Ufumu wa Mulungu Ndiwo Chiyembekezo Chokha Chotsimikizirika cha Mtsogolo: Anthu ambiri alibe chidaliro kwenikweni m’maboma a anthu. Amaona kuti alibe chiyembekezo chakuti adzaona dziko labwino m’moyo wawo. Chipembedzo chonyenga chalephera kuwapatsa maziko alionse a chiyembekezo. Nchifukwa chake chinthu chachikulu koposa chimene anthu afunikira ndicho kumva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Sonyezani mmene potsirizira pake udzathetsera mavuto onse amene anthu akukumana nawo.
5 Baibulo Ndilo Magwero Okha a Chitsogozo Chodalirika: Unyinji lerolino wasocheretsedwa ndi atsogoleri amene amadalira nzeru za anthu ndi mafilosofi a dziko. Anthu afunikabe kuzindikira kuti “sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yer. 10:23) Phunziro lofunika kwambiri limene angatengepo nlakuti iwo ayenera ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wawo wonse, osachirikizika pa luntha lawo.’ (Miy. 3:5) Pamene kuli kwakuti nthaŵi zasintha, Baibulo silinatero. Chifukwa chake, mu utumiki wathu tiyenera nthaŵi zonse kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu, tikumaphunzitsa ena kuzindikira chitsogozo chake chouziridwa chaumulungu. (2 Tim. 3:16, 17) Kuti tikwaniritse chifuno chimenecho, tiyenera kusonyeza anthuwo kufunika kwa Baibulo mwa kulozera kwa ilo m’maulaliki athu, kuligwiritsira ntchito kuyankha mafunso awo, ndi kuwalimbikitsa kuliphunzira ndi kutsatira nzeru yake yogwira ntchito.
6 Ngakhale kuti nthaŵi zasintha lerolino, zolinga zathu mu utumiki zidakali chimodzimodzi. Tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, kukulitsa chidaliro m’Mawu a Mulungu, ndi kuthandiza ena kuona kufunika kwakuti aphunzire nafe Baibulo. Zolankhula zathu ziyenera kugwirizana ndi zimene aja amene timachitirako umboni akufunikira panthaŵiyo. Mwa kuchita zimenezi, tingakhale ogaŵana ndi ena uthenga wabwino, mwakutero tikumapindula ochuluka.—1 Akor. 9:19, 23.