Kukwaniritsa Choŵinda Chathu tsiku ndi Tsiku
1 Wamasalmo Davide anasonkhezeredwa kulengeza kwa Yehova kuti: “Ndidzaimba zolemekeza dzina lanu ku nthaŵi zonse, kuti ndichite zoŵinda zanga tsiku ndi tsiku.” (Sal. 61:8) Davide anadziŵa kuti kupanga choŵinda ndiyo nkhani ya kudzifunira kwa munthu. Komabe, anazindikiranso kuti ngati anapanga choŵinda, anafunikira kuchikwaniritsa. Ngakhale kuti zinali choncho, anatamanda Yehova chifukwa cha mpata wa kukwaniritsa zoŵinda zake tsiku ndi tsiku.
2 Pamene tinadzipatulira kwa Yehova, tinaŵinda mofunitsitsa kuchita chifuniro chake. Tinadzikana ndi kupanga utumiki wa Yehova kukhala cholondola chathu chachikulu m’moyo. (Luka 9:23) Chifukwa chake, nafenso tiyenera kukwaniritsa choŵinda chathu tsiku ndi tsiku. (Mlal. 5:4-6) Chilengezo chathu chapoyera chopangidwa panthaŵi yaubatizo wa m’madzi chiyenera kusonyezedwa m’moyo wathu wonse, popeza kuti timadziŵa kuti “ndi m’kamwa [munthu] avomereza kutengapo chipulumutso.” (Aroma 10:10) Zimenezi zimaphatikizapo kulalikira uthenga wabwino. (Ahebri 13:15) Mikhalidwe yamunthu mwini imasiyanasiyana kwambiri, koma tsiku ndi tsiku ife tonse tikhoza kusumika maganizo pa kufunika kwa kuuza ena uthenga wabwino.
3 Pangani Mipata ya Kulalikira Tsiku ndi Tsiku: Kuuza wina uthenga wabwino kuli chinthu chosangalatsa. Kuti tichite zimenezi tsiku ndi tsiku, tiyenera kupanga mipata ya kulalikira panthaŵi iliyonse pamene mikhalidwe yathu itilola. Zokumana nazo zambiri zachitika kwa aja amene ayamba kuchitapo kanthu kuchitira umboni mwamwaŵi kwa anthu kuntchito kapena kusukulu ndi anansi kapena ena amene amakumana nawo tsiku lililonse. Ngakhale kulemba makalata kapena kugwiritsira ntchito telefoni kungakhale njira yochitira umboni kwa ena. Kugwiritsira ntchito mwaŵi wa njira zonsezi ndiponso kupatula nthaŵi mokhazikika ya kuchitira umboni kukhomo ndi khomo ndi kupanga maulendo obwereza kungabweretse chimwemwe chapadera chimene chimadza pa kuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba. Inde, tsiku lililonse tingakhale okhoza kupanga mipata ya kulalikira.
4 Mlongo wina anayamba kuŵerenga Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku mkati mwa nthaŵi ya kupuma kwake kuntchito. Anapempha wantchito mnzake kuŵerenga naye lemba la tsikulo, ndipo posapita nthaŵi zimenezo zinayambitsa phunziro la Baibulo ndi mkaziyo. Anali kuphunzira theka la ola tsiku lililonse, masiku asanu pa mlungu. Wantchito mnzake wina ankaona phunziro lawo la tsiku ndi tsiku. Potsirizira pake iyeyo anadzidziŵikitsa kukhala mbale wofooka. Atasonkhezeredwa ndi changu cha mlongoyo, anafikira mkulu kuti ayambitsidwenso kukangalika. Mlongo ameneyu anakhudza mitima ya anthu aŵiri m’njira yothandiza chifukwa cha kukwaniritsa mosamala choŵinda chake tsiku ndi tsiku.
5 Pamene tisonkhezeredwa ndi mtima wodzala ndi chiyamikiro pa zinthu zonse zabwino zimene Yehova watichitira, kukwaniritsa choŵinda chathu cha kudzipatulira monga momwe tingathere tsiku lililonse kumatibweretsera chimwemwe ndi chikhutiro. Monga wamasalmo tingalengeze kuti: “Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse.”—Sal. 86:12.