‘Chitani Changu’
1 Pamene tinadzipatulira kwa Yehova, tinalonjeza kumpatsa zabwino koposa. Moyenerera, mtumwi Petro analimbikitsa Akristu a m’zaka za zana loyamba kuchita changu potsimikizira kaimidwe kawo pamaso pa Yehova. (2 Pet. 1:10) Ndithudi tikufuna kuchita changu kuti timkondweretse Yehova pomtumikira lerolino. Kodi zimenezo zimaphatikizapo chiyani? Mmene unansi wathu ndi Yehova ukukula ndipo tikumasinkhasinkha zonse zimene watichitira, nthaŵi zonse mitima yathu imatisonkhezera kuchita zimene tingathe mu utumiki wake. Tikufuna kuwongolera utumiki wathu, ndipo ngati nkotheka, kuufutukula.—Sal. 34:8; 2 Tim. 2:15.
2 Mbale wina wachinyamata amene anafuna kuchita zambiri mu utumiki anaona kuti phunziro lokhazikika la Mawu a Mulungu linakulitsa chiyamikiro chake kwa Yehova ndipo linamuwonjezera changu. Zimenezo zinamsonkhezera kufunsira utumiki waupainiya. Mlongo wina amene zinali kumvuta kulankhula ndi anthu osawadziŵa anayeseza maulaliki ena ali m’buku la Kukambitsirana ndipo posapita nthaŵi anayamba kuchita bwino kwambiri mu utumiki. Anakhoza kuchititsa phunziro la Baibulo kwa mwamuna ndi mkazi wake amene analandira choonadi.
3 Kondwerani ndi Zimene Mungachite: Ena a ife amakumana ndi mikhalidwe yovuta yonga thanzi lofooka, chitsutso cha m’banja, umphaŵi, kapena mphwayi m’gawo lathu. Mavuto ena ambiri ofala masiku ano otsiriza angadodometse utumiki wathu. (Luka 21:34; 2 Tim. 3:1) Kodi zimenezi zimatanthauza kuti talephera pakudzipatulira kwathu kwa Yehova? Iyayi, malinga ngati tikumtumikira ndi changu chathu chonse.
4 Si kwanzeru kudziyesa tokha modziyerekezera ndi zimene ena amachita. M’malo mwake, Malemba amatilimbikitsa kuti “yense ayesere ntchito yake ya iye yekha.” Kudzikhutula pamlingo womwe tingakwanitse kumamsangalatsa Yehova ndipo tidzakhala “nako kudzitamandira.”—Agal. 6:4; Akol. 3:23, 24.
5 Tiyenitu tilabadire mawu a Petro ‘kuchita changu kuti Mulungu atipeze mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.’ (2 Pet. 3:14) Mzimu umenewo udzatipangitsa kumva osungika ndipo udzatipatsa mtendere wamaganizo umene ndi Yehova yekha angapereke.—Sal. 4:8.