Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/97 tsamba 1
  • Kukhulupirika Kufupidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhulupirika Kufupidwa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Yehova Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tiziyesetsa Kuwonjezera Utumiki Wathu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Ndinu Wokhulupirika M’zinthu Zonse?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 7/97 tsamba 1

Kukhulupirika Kufupidwa

1 Pa Ahebri 11:6 tikuuzidwa kuti Mulungu “ali wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye.” Njira imodzi imene amafupira atumiki ake odzipereka amene akhala ‘okhulupirika pa zinthu zazing’ono’ ndiyo mwa ‘kuwakhazika pa zinthu zambiri.’ (Mat. 25:23) M’mawu ena, Yehova nthaŵi zambiri amafupa ntchito yakhama mwa kupatsa mboni zake zokhulupirika mwaŵi wina wautumiki.

2 Kukhulupirika kwa mtumwi Paulo kunafupidwa mwa kumpatsa utumiki umene unamfikitsa kumizinda ndi kumidzi ya ku Ulaya ndi Asia Minor. (1 Tim. 1:12) Ngakhale kuti Paulo anafunika kuyesayesa zolimba kuti akwaniritse utumiki wake, iye anaukonda kwambiri mwaŵi umene analandira. (Aroma 11:13; Akol. 1:25) Anasonyeza kuyamikira kwake kochokera pansi pa mtima mwa kufunafuna moona mtima mpata wolalikira. Mwa ntchito yake yachangu, anasonyeza bwino lomwe kuti chikhulupiriro chake chinali chamoyo. Chitsanzo chake chikutisonkhezera kuona mwaŵi wathu wautumiki kukhala wamtengo wapatali.

3 Yehova Watipatsa Utumiki: Kodi timasonyeza motani kuyamikira kofanana ndi kumene Paulo anasonyeza ponena za mwaŵi wautumiki umenewu? Timafunafuna njira zowonjezerera gawo lathu mu utumiki. Timagwiritsira ntchito mpata uliwonse wolalikira mwamwaŵi limodzinso ndi kukhomo ndi khomo. Timabwerera kwa onse amene sitinapeze panyumba ndi kupanga maulendo obwereza kwa onse amene ali ndi chidwi. Ndipo timasunga malonjezo amene timapanga a kukachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba.

4 Ponena za utumiki wathu, Paulo analangiza kuti: “Chita nawo mofulumira.” (2 Tim. 4:2, NW) Chinthu chofulumira chimafuna kuchitapo kanthu nthaŵi yomweyo. Kodi utumiki wathu timauchita monga kuti ngwofulumira, kuuika patsogolo m’moyo wathu? Mwachitsanzo, sitidzafuna kuti zosangulutsa zathu ndi zofuna zina zaumwini pakutha kwa mlungu zitisokonezere nthaŵi imene tiyenera kuthera mu utumiki wakumunda. Popeza tikukhulupirira zedi kuti mapeto a dongosolo lino akufika mwamsanga, tikhulupiriranso kuti kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndiyo ntchito yofunika koposa imene tingachite.

5 Kukhulupirika kwathu kwa Mulungu kumasonyezedwa mwa kukhala kwathu oona kwa iye ndi kummamatira ndi kuchita mosalekeza ntchito imene watipatsa. Tiyeni tikwaniritse utumiki wathu, kuti Yehova afupe kwambiri kukhulupirika kwathu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena