Kodi Amphwayi Mumachita Nawo Bwanji?
1 Mphwayi ndi mkhalidwe wongokhala zii, wopanda chidwi, wosasamala zimene wina akunena. Ndiwo mkhalidwe wofala ndi wovuta womwe timakumana nawo m’munda. Kodi mumachita nawo bwanji? Kodi umakupangitsani kufooka mu utumiki wanu? Kodi mungalake bwanji mphwayi kuti mufikitse uthenga wa Ufumu kwa anthu?
2 Choyamba, dziŵani chifukwa chake anthu a m’dera lanu ali amphwayi. Kodi chingakhale chifukwa chakuti atsogoleri awo achipembedzo ndi andale anawakhumudwitsa? Kodi amaganiza kuti palibe njira yothetsera mavuto awo? Kodi amakayikira malonjezo a kanthu kena kabwino? Kodi samafuna kuganiza za zinthu zauzimu pokhapokha ngati angapeze mapindu ake nthaŵi yomweyo?
3 Afotokozereni Chiyembekezo cha Ufumu: Palibe vuto lina limene Ufumuwo sudzathetsa. Choncho, ngati tingathe kutero, tiyenera kumalankhula za malonjezo a Ufumu, tikumatchula mfundo zazikulu za m’Malemba, ngakhale kuli kosatheka kapena kosayenera kusonyeza lemba la m’Baibulo. (Aheb. 4:12) Komabe, kodi tingakambitsirane nawo bwanji mpaka pamenepo?
4 Anthu afunikira kumvetsetsa chifukwa chimene timawachezera. Afunikira kudziŵa kuti timawafikira chifukwa chakuti timakonda anansi athu ndipo timadera nkhaŵa anthu. Tingawafunse funso lanzeru ngati ili, “Kodi mukuganiza kuti chingathetse [mavuto a anthu nchiyani]?” Ngati njira imodzi siinatheke, yesani inanso.
5 M’dera lina la anthu achuma kwambiri kumene eni nyumba anali amphwayi pa uthenga wa Ufumu, ofalitsa anayesetsa kupeza mawu oyamba omwe akanachititsa chidwi. Pamene anali kusonyeza buku la Chidziŵitso, mwamuna wina ndi mkazi wake anayesa mawu oyamba awa: “Kodi mukuganiza kuti kukhala wophunzira bwino nkofunika kuti munthu zimuyendere bwino padziko lero? Kodi mukuvomereza kuti kuphunzira bwino kumaphatikizaponso kudziŵa Baibulo?” Kumasana kokha anagaŵira mabuku atatu, lina anagaŵira mkazi wina yemwe tsiku lina anadzanena kuti waŵerenga buku lonse la Chidziŵitso, ndipo anadzavomereza phunziro la Baibulo.
6 Pamene mukumana ndi munthu wamphwayi, yesani njira zosiyanasiyana, funsani mafunso odzutsa chidwi, ndipo gwiritsirani ntchito mphamvu ya Mawu a Mulungu. Mwa kutero mudzakhoza kuthandiza ena kulandira chiyembekezo chathu chosangalatsa cha Ufumu.