Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/99 tsamba 8
  • Kodi Mukanena Chiyani kwa Wosakhulupirira Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukanena Chiyani kwa Wosakhulupirira Mulungu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Anali M’gulu la Zigawenga Kenako Anayamba Kutumikira Mulungu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Anthu Okhulupirira Kuti Kulibe Mulungu Ali pa Kampeni
    Galamukani!—2010
  • Kodi N’zotheka Kuyamba Kukhulupirira Mlengi?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Pali Umboni Wasayansi Wotsimikizira Zoti Kulibe Mulungu?
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 12/99 tsamba 8

Kodi Mukanena Chiyani kwa Wosakhulupirira Mulungu?

1 “Sindikhulupirira Mulungu,” anatero pulofesa wina wa ku Poland kuuza m’mishonale wa ku Afirika. Komabe, mlongoyo anakambirana ndi mkaziyo ndipo anamupatsa buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Pamene m’mishonaleyo anabwererako mlungu wotsatira, pulofesayo anamuuza kuti: “Sindinenso wosakhulupirira Mulungu!” Anali ataŵerenga buku lonse la Creation ndipo tsopano anapempha phunziro la Baibulo. Kodi mungatani kuti mukhale wachipambano pochitira umboni kwa awo amene amati sakhulupirira Mulungu? Choyamba, onani zifukwa zosiyanasiyana zimene anthu amanenera choncho.

2 Zina mwa Zifukwa Zimene Zimapangitsa Kusakhulupirira Mulungu: Si osakhulupirira Mulungu onse amene analeredwa choncho. Ambiri anali m’zipembedzo ndipo nthaŵi ina ankakhulupirira Mulungu. Komabe, matenda, mavuto a m’banja kapena kusoŵa chilungamo kumene anachitidwa kunafooketsa chikhulupiriro chawo. Kwa ena, maphunziro a m’masukulu apamwamba apereka malingaliro oipa pa malingaliro awo okhudza Mulungu. Onani zitsanzo zotsatirazi za osakhulupirira Mulungu amene m’kupita kwa nthaŵi anayamba kukhulupirira kwambiri Yehova Mulungu ndi kukhala Mboni zake.

3 Mkazi wina ku Paris anabadwa wopuwala. Ngakhale anali Mkatolika wobatizidwa, ankati sakhulupirira Mulungu. Pamene anafunsa aviligo chifukwa chimene Mulungu analolera kuti iye abadwe wopuwala motero, anam’yankha kuti: “Chifukwa amakukonda.” Iye anakana kukhulupirira lingaliro lopusali. Lingaliraninso za mnyamata wina wa ku Finland amene atam’pima anam’peza kuti anali ndi matenda osachiritsika ndipo anali kumayenda panjinga ya opuwala. Mayi ake anapita naye kwa mwamuna wina wa Pentecostal amene ankati amachiza anthu odwala mozizwitsa. Koma kumeneko sanachiritsidwe. Ndiyeno, mnyamatayo anataya chidwi chake mwa Mulungu ndipo anakhala wosakhulupirira Mulungu.

4 Mwamuna wina wa ku Honduras analeredwa m’chipembedzo cha Katolika koma anaphunzira filosofi ya Sosholizimu komanso maphunziro a kusakhulupirira Mulungu. Mosonkhezeredwa ndi maphunziro akuyunivesite amene amanena kuti munthu anachita kusinthika, iye analeka kukhulupirira Mulungu. Mofananamo, mayi wina ku United States analeredwa m’chipembedzo cha Methodist. Ku koleji, anatenga maphunziro a zamaganizo. Kodi zikhulupiriro zake zinakhudzidwa motani? Iye anati: “M’nthaŵi ya chilimwe yokha anali atandiwonongera chikhulupiliro changa chonse chimene ndinali nacho m’chipembedzo.”

5 Kufika Mitima ya Anthu Oona Mtima: Anthu ambiri amene amati sakhulupirira Mulungu angakonde kudziŵa ngati pali njira zothetsera mavuto a matenda, kusagwirizana m’banja, kusoŵa chilungamo, ndi zina zotero. Ndi ofunitsitsa kupeza mayankho a mafunso monga akuti: ‘Chifukwa chiyani pali kuipa?’ ‘Chifukwa chiyani zinthu zoipa zimachitikira anthu abwino?’ komanso ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’

6 Mwamuna ndi mkazi amene akukhala ku Switzerland analeredwa monga osakhulupira Mulungu. Pamene anafikiridwa koyamba ndi choonadi, anakana. Koma anali ndi mavuto akulu m’banja lawo ndipo anali kufuna kusudzulana. Pamene banja la Mboni linawafikiranso, Mbonizo zinasonyeza aŵiriwo kuchokera m’Baibulo mmene angathetsere mavuto awo. Banjalo linachita chidwi ndi uphungu wothandiza wopezeka m’Malemba, ndipo linavomera kuphunzira Baibulo. Ukwati wawo unalimba, ndipo anapita patsogolo mwauzimu, ndiyeno anabatizidwa.

7 Zimene Munganene kwa Wosakhulupirira Mulungu: Pamene wina wakuuzani kuti sakhulupirira Mulungu, yesetsani kudziŵa chifukwa chake akutero. Kodi n’chifukwa cha maphunziro amene anaphunzira, mavuto amene wakhala nawo, kapena chinyengo cha zipembedzo ndi ziphunzitso zonama zimene amaona? Mungam’funse kuti: “Kodi mwakhala mukuganiza chonchi nthaŵi zonse?” kapena “Chifukwa chiyani mukunena chonchi?” Yankho lake lidzakuthandizani kuona zoti munene.

8 Mungapitirize kukambirana ndi wosakhulupirira Mulungu mwa kufunsa kuti:

◼ “Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti: ‘Ngati kuli Mulungu, chifukwa chiyani pali kuvutika ndi kusoŵa chilungamo kochuluka chonchi m’dziko?’ [Yembekezerani yankho.] Kodi ndingakusonyezeni zimene Baibulo limanena pankhaniyi?” Ŵerengani Yeremiya 10:23. —Kuti mupeze malingaliro owonjezereka, onani m’buku la Kukambitsirana, masamba 311-13.

9 Kunena zoona, si osakhulupirira Mulungu onse amene adzalandira choonadi. Komabe pali ambiri amene akufuna kudziŵa malingaliro ena. Gwiritsani ntchito nzeru, chikoka ndipo koposa zonse, mphamvu ya Mawu a Mulungu kuti iwathandiza kudziŵa choonadi.—Mac. 28:23, 24; Aheb. 4:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena