‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
1 Ndi mawu ali pamwambaŵa, Paulo analongosola Trufena ndi Trufosa, alongo aŵiri amene anali kugwira ntchito molimbika mu mpingo wa Roma. Za mlongo wina, Persida, anati: “Anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.” Mofananamo ananena zabwino za Febe monga “wosungira ambiri.” (Aroma 16:2, 12) M’Malemba, Dorika anatchulidwa monga amene “anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo.” (Mac. 9:36) Si dalitso lake kukhala ndi akazi auzimu m’mipingo!
2 Kodi timawayamikira alongo amene amagwira ntchito molimbika mu mpingo mwathu? Amachita mbali yaikulu pa ntchito yolalikira, kuchititsa maphunziro a Baibulo ochuluka, ndiponso kuthandiza atsopano ambiri. Amakhalanso ndi nthaŵi yaitali kuthandiza ana kupita patsogolo mwauzimu. Akazi achikristu amachita mbali yawo kukulitsa mzimu wa chikondi, chimwemwe, mtendere, ndi changu mu mpingo. Amachirikiza amuna awo ndi ena m’banja lawo m’njira zambiri kuti achite zochuluka mu utumiki wa Yehova.
3 Alongo Amene Ali mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse: Mwa amene amagwiritsa ntchito mwa Ambuye pali alongo amene ali amishonale, ndipo ambiri apititsa patsogolo ntchito yolalikira m’mayiko akunja. Akazi a oyang’anira oyendayenda amakhala otanganidwa mu utumiki wakumunda m’mipingo imene amuna awo amatumikira ndipo izi zimalimbikitsa alongo ambiri. Sitiyeneranso kuiŵala alongo a pa Beteli, amene amachita utumiki wopatulika mwachangu pochirikiza gulu la Yehova. Ndiponso alongo athu amene ali apainiya okhazikika amene, mwa khama lawo lonse komanso kukhulupirika kwawo potamanda Mulungu, akuthandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi.
4 Akazi okhulupirika ameneŵa amapeza chikhutiro chenicheni pamoyo wawo wodzimana umenewu. (1 Tim. 6:6, 8) Afunika kuwayamikira ndi kuwalimbikitsa komanso kuwachirikiza mwanjira ina iliyonse imene tingathe.
5 Akazi achikristu ndi chuma chamtengo wapatali m’gulu la Yehova, ndipo akuchita utumiki wokhulupirika wodzetsa madalitso kwa onse. Tipitirizetu kuwayamikira akazi otereŵa ndi kupempherera kuti madalitso a Yehova akhalebe pa iwo pamene akupitiriza ‘kugwiritsa ntchito mwa Ambuye.’