Kodi Mukupirira?
1 ‘Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ana anga akuyenda m’choonadi.’ (3 Yoh. 4) Kupirira kwa ana auzimu a Yohane kunam’patsa chimwemwe chachikulu. Si mmene zimam’kondweretsera Atate wathu wakumwamba kuona mamiliyoni a ana ake ‘akuyenda m’choonadi’!—Miy. 23:15, 16; 27:11.
2 Ngakhale anthu onse a Mulungu akulimbikira kukhala achangu mu ntchito yachikristu, ena abwerera m’mbuyo pang’onopang’ono. Ngakhale kuti anthu ameneŵa atangophunzira kumene choonadi anali achangu kwambiri, m’kupita kwa zaka, akhala ndi chizoloŵezi chochita pang’ono chabe kapena modumphadumpha m’kagwiridwe kawo ka ntchito yopanga ophunzira.
3 Ndithudi ena abwerera m’mbuyo chifukwa cha matenda ndiponso mavuto obwera chifukwa cha ukalamba. Komabe, n’ngofunika kuwayamikira chifukwa cha kupirira kwawo. Akuchita zimene angathe. Koma aliyense amene anapatulira moyo wake kwa Mulungu ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndatanganidwa kwambiri ndi zinthu zakuthupi kwakuti zinthu za Ufumu zilibe malo kwenikweni m’moyo wanga? Kodi tsopano ndine “wofunda,” kapena kodi ndikupitirizabe ‘kuyesetsa’ kwambiri?’ (Chiv. 3:15, 16; Luka 13:24) Tonsefe mwapemphero tione zimene tikuchita ndipo tiwongolere pofunika kutero, podziŵa kuti Yehova amalonjeza kupereka “ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino.”—Aroma 2:10.
4 Mmene Mungapiririre: Kodi n’chiyani chinam’thandiza Yesu kuti athe kupirira? Paulo analongosola kuti: “Chifukwa cha chimwemwe chimene chinali kum’dikira, Iyeyu anapirira zoŵaŵa za pamtanda. Sanasamaleko manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano ali kukhala kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Aheb. 12:1-3, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Chimwemwe chimene chinali kum’dikira Yesu chinali choposa ziyeso za kanthaŵi zimene anakumana nazo. Kudziŵa chimwemwe chimene chikutidikira kungatithandizenso kupirira. (Chiv. 21:4, 7; 22:12) Ngati tiyang’ana kwa Yehova kuti atipatse nyonga mwa phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse, ndi kusaleka kupemphera, tidzatha kupitiriza kugwira ntchito imene watipatsa kuti tichite.
5 Yehova amasangalala kuona anthu ake okhulupirika akupirira. Choncho tiyeni tiwonjezere chimwemwe chake mwa kupitiriza ‘kuyenda m’choonadi.’