Makolo—Khomerezani Zizoloŵezi Zabwino mwa Ana Anu
1 Munthu sabadwa ndi zizoloŵezi zabwino, komanso sakhala nazo mwangozi. Ndipo kukhomereza zizoloŵezi zabwino mwa ana kumatenga nthaŵi. “Kukhomereza” kumatanthauza “kuphunzitsa pang’onopang’ono” kapena “kuloŵetsa dontho limodzilimodzi.” Makolo ayenera kusasinthasintha kuti athe ‘kulera [ana awo] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’—Aef. 6:4.
2 Yambani Ali Makanda: Nzeru imene makanda ali nayo yokhoza kuphunzira ndi kuchita zinthu zatsopano n’njodabwitsa. Ngakhale achikulire amavutika nthaŵi zambiri kuphunzira chinenero, ana oti sanayambe sukulu akhoza kuphunzira zinenero ziŵiri kapena zitatu nthaŵi imodzi. Musaganize kuti mwana wanu ndi wamng’ono kwambiri kuti sangaphunzire zizoloŵezi zabwino. Malangizo a choonadi cha m’Baibulo akayamba msanga n’kusaimira panjira, mwanayo podzafika zaka zingapo, maganizo ake amakhala atadzaza ndi chidziŵitso chimene chidzam’patsa “nzeru kufikira chipulumutso.”—2 Tim. 3:15.
3 Utumiki Wakumunda Ukhale Chizoloŵezi: Chizoloŵezi chabwino chofunika kukhomereza m’zaka zimene mwana amaphunzitsika ndicho kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu nthaŵi zonse. Makolo ambiri amayamba izi mwa kumatenga ana awo akadali makanda mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Makolo amene amagwira ntchito yochitira umboni mokhazikika amathandiza ana awo kukhala oyamikira ndi achangu mu utumiki. Makolo angasonyeze ana mmene angachitire umboni pambali zonse za utumiki wakumunda.
4 Kulembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase kumathandizanso ana. Imawaphunzitsa zizoloŵezi zabwino za kuphunzira ndi mmene angaŵerengere moti amvetse. Amaphunzira kukambirana nkhani za m’Baibulo, kupanga maulendo obwereza, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Maphunziro otereŵa angawalimbikitse kuchita upainiya ndiponso kukalamira utumiki wapadera. Anthu ambiri a pabeteli ndiponso amishonale amasangalala kukumbukira masiku awo oyambirira m’sukuluyi ndipo amati ndiyo inawathandiza kukhala ndi zizoloŵezi zabwino.
5 Tonse tili ngati dongo m’manja mwa Woumba Wamkulu, Yehova. (Yes. 64:8) Dongo likakhala lofeŵa, silivuta kuumba. Likauma, limalimba kwambiri. N’chimodzimodzi anthu. Ngati ndi ana, amakhala ofeŵa kwambiri—ndipo akakhala ana aang’ono kwambiri, zimakhala bwino zedi. Zaka zawo zaukhanda ndi nthaŵi imene amaphunzitsika, pamene amaumbika kukhala abwino kapena oipa. Monga kholo losamala, yambani msanga kukhomereza zizoloŵezi zabwino za utumiki wachikristu mwa ana anu.