Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/01 tsamba 8
  • Yehova Amapatsa Mphamvu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amapatsa Mphamvu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Funani Yehova, ndi Mphamvu Yake”
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Yehova Amatipatsa Mphamvu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 2/01 tsamba 8

Yehova Amapatsa Mphamvu

1 Kodi mumaganiza zotani mukamva za mtumwi Paulo? Tikamaŵerenga buku la Machitidwe, timaona changu chimene anali nacho potumikira Yehova. Kodi Paulo anatha bwanji kuchita zonse zimene anachita? Iye anati: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afil. 4:13) Ifenso tingapindule nazo mphamvu zimene Yehova amatipatsa. Motani? Mwa kutsatira njira zisanu ndi imodzi zimene wapereka kuti zitipatse mphamvu ndi kutilimbitsa mwauzimu.

2 Mawu a Mulungu: Monga momwe timafunikira chakudya kuti thupi lathu likhalebe lamphamvu, tiyeneranso kudya Mawu a Mulungu kuti tikhale amoyo mwauzimu. (Mat. 4:4) Baibulo limapereka mphamvu yotichirikiza. Kuti tikhalebe achangu ndi okonda choonadi, tiyenera kuchita phunziro laumwini latanthauzo ndi kusinkhasinkha, tsiku lililonse ngati tingakwanitse.—Sal. 1:2, 3.

3 Pemphero: Kuyandikira kwa Yehova n’kofunika, makamaka pamene tili ndi zosoŵa zapadera. Mwa mzimu wake, amapereka mphamvu kwa amene amam’pempha popemphera. (Luka 11:13; Aef. 3:16) Malemba amatilimbikitsa ‘kulimbika chilimbikire kupemphera.’ (Aroma 12:12) Kodi inu mumatero?

4 Mpingo: Timapezanso mphamvu ndi chilimbikitso pamisonkhano ya mpingo ndi mayanjano abwino a abale ndi alongo athu amene timakhala nawo kumeneko. (Aheb. 10:24, 25) Tikakhala m’mavuto, amatilimbikitsa ndi kutithandiza mwachikondi.—Miy. 17:17; Mlal. 4:10.

5 Utumiki Wakumunda: Kulalikira nthaŵi zonse kumatithandiza kuika maganizo athu pa Ufumu ndi madalitso ake. Moyo wathu umasangalala tikaphunzitsa ena za Yehova. (Mac. 20:35) Si tonse amene tingapite kukatumikira kumene kuli kosoŵa kwambiri kapena kuchita utumiki wanthaŵi zonse, koma tikhoza kuchita mokwanira utumiki m’njira zina.—Aheb. 6:10-12.

6 Oyang’anira Achikristu: Timapindula akulu akamatilimbikitsa ndi kutithandiza. Yehova wawapatsa ntchito yoŵeta gulu la nkhosa la Mulungu lili mwa iwo. (1 Pet. 5:2) Oyang’anira oyendayenda amalimbikitsa mipingo imene amatumikira, monga ankachitira Paulo masiku ake.—Aroma 1:11, 12.

7 Zitsanzo za Anthu Okhulupirika: N’zolimbikitsa kupenda zitsanzo zabwino za antchito anzathu okhulupirika, akale ndi amasiku ano omwe. (Aheb. 12:1) Mukafuna mphamvu, bwanji osaŵerenga imodzi mwa nkhani zolimbikitsa za moyo wa ena m’magazini athu, malipoti olimbikitsa mu Yearbook, kapena zina mwa nkhani zosangalatsa za mbiri yamakono ya Mboni za Yehova mu buku la Proclaimers?

8 Mbale wina, amene ali ndi zaka za m’ma 90, anaphunzira choonadi ali mwana. Akadali mnyamata, chikhulupiriro chake chinayesedwa. Choyamba, ena amene anali achangu mu mpingo anasiya gulu la Yehova. Kenako ntchito ya kunyumba ndi nyumba inkamuvuta. Komabe, nthaŵi zonse anadalira Yehova. Mosakhalitsa anayamba kusangalala ndi utumiki. Nanga lero? Ngakhale amadwaladwala, akali m’banja la Beteli ku Brooklyn, akutumikira m’Bungwe Lolamulira. Ali wosangalala kuti wamamatira gulu la Yehova.

9 Mlongo wina m’banja la Beteli ku Britain anabatizidwa ali ndi zaka 13. Anayamba upainiya ndi mlongo wake chaka chotsatira. Patatha chaka chimodzi, bambo ake anamangidwa chifukwa chosaloŵerera mu nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Mlongoyu anadalirabe mphamvu ya Yehova, ndipo anapitiriza kutumikira Mulungu woona. M’kupita kwa nthaŵi, anakwatiwa ndi mbale wokhulupirika, ndipo onse anapitiriza kuchita chifuno cha Yehova. Atakhala zaka 35 m’banja, mwamuna wake anamwalira mwadzidzidzi. Anapezanso mphamvu kwa Yehova, ndipo wapitiriza kum’tumikira mpaka lero, ndipo akufunitsitsa kutumikira Yehova kosatha m’banja la Yehova lapadziko lapansi.

10 Yehova amathandiza ndi kupatsa mphamvu atumiki ake okhulupirika. “Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.” Tingapeze mphamvu m’magwero a mphamvu opanda malire ameneŵa mwa kutsatira njira zonse zisanu ndi imodzi zimene zatchulidwazi. Kumbukirani kuti: “Iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; . . . adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yes. 40:29-31) Paulo anadalira kwambiri mphamvu ya Yehova, ifenso tiyenera kutero.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena