Chikondi Chimatisonkhezera Kulalikira
1 Monga Mboni za Yehova timadziŵika bwino ndi kulalikira uthenga wa Ufumu mwachangu. (Mat. 24:14) Anthu oposa sikisi miliyoni padziko lonse ali pakalikiliki; chiŵerengero chimakula atsopano akayamba kulalikira nawo. Amaŵerenga okhawo amene akugwira nawo ntchitoyi.
2 Kodi n’chiyani chimatisonkhezera kudzipereka kugwira ntchito yovuta ngati imeneyi? Sitikakamizidwa, kukopeka ndi chuma chakuthupi kapena kufuna ulemu wapadera. Poyamba, ambirife tinali amantha chifukwa timadziona kuti sitikuyenera, komanso nthaŵi zambiri anthu ankatsutsa. (Mat. 24:9) Ambiri sangamvetse chimene chimatisonkhezera. Koma pali chifukwa chimene chimatisonkhezera kupitirizabe.
3 Mphamvu ya Chikondi: Yesu anatchula lamulo lalikulu koposa onse pamene anati ‘tizikonda Ambuye Mulungu wathu ndi mtima wathu wonse, ndi moyo wathu wonse, ndi nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse.’ (Marko 12:30) Timam’konda kwambiri Yehova chifukwa timayamikira umunthu wake ndi zochita zake—Wolamulira Wamkulu, Mlengi wa zinthu zonse woyenera “kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu.” (Chiv. 4:11) Mikhalidwe yake yodabwitsayo n’njosayerekezeka.—Eks. 34:6, 7.
4 Kudziŵa Yehova ndi kumukonda kumatisonkhezera kuwalitsa kuunika kwathu pamaso pa anthu. (Mat. 5:16) Kuunika kwathu kumawala pamene tim’tamanda poyera, tilankhula za ntchito zake zodabwitsa, ndi pamene tifalitsa uthenga wa Ufumu wake. Mofanana ndi mngelo wouluka pakati pa mlengalenga, tili ndi ‘uthenga wabwino wosatha, tiulalikire kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.’ (Chiv. 14:6) Chikondi n’chimene chimatisonkhezera kugwira ntchito yolalikira yapadziko lonse.
5 Dziko limaona ntchito yathu yolalikira kukhala ‘yopusa’ yofunika kuinyalanyaza. (1 Akor. 1:18) Anthu ayesa njira zosiyanasiyana kuti athetse ntchito yathu. Chikondi chenicheni chatilimbikitsa kulengeza molimba mtima kuti: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva. . . . Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Mac. 4:20; 5:29) Ntchito yolalikira ikupitirira kukula m’mbali zonse za dziko lapansi ngakhale pali zitsutso.
6 Kukonda kwathu Yehova kuli ngati moto wotentha umene umatisonkhezera kulalikira ponseponse zoposa zake. (Yer. 20:9; 1 Pet. 2:9) Tidzapitiriza ‘kulalikira machitidwe ake mwa mitundu ya anthu pakuti wachita zaulemerero’!—Yes. 12:4, 5.