Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/01 tsamba 8
  • Chitirani Umboni mwa Kukhala Mnansi Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitirani Umboni mwa Kukhala Mnansi Wabwino
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Abwino Okhala Nawo Pafupi Ndi Ofunika Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Uzikonda Mnzako Mmene Umadzikondera Wekha”
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi ‘Mumakonda Anzanu Ngati Mmene Mumadzikondera Nokha’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 4/01 tsamba 8

Chitirani Umboni mwa Kukhala Mnansi Wabwino

1 Yesu anati “uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” (Mat. 22:39) Mosakayika, ‘mumachitira chokoma’ okhulupirira anzanu, koma kodi mungakulitse chikondi chanu mwa kukondanso anthu amene mumakhala nawo pafupi? (Agal. 6:10) Mungachite zimenezi motani?

2 mwa Kudzidziŵikitsa: Kodi anansi anu amadziŵa kuti ndinu Mboni? Ngati sadziŵa, bwanji osadzerako muli mu utumiki wakumunda? Mudzadabwa ndi zotsatira zake! Kapena ngati mukuona kuti si kovuta, alalikireni mwamwayi. Muli paja mungawaone akugwira ntchito pabwalo pawo kapena akuwongola miyendo. Afikireni mukumwetulira. Limbani mtima kuwauza zikhulupiriro zanu, malo a Nyumba ya Ufumu, ndi zimene zimachitika kumeneko, ndipo atchulireni anthu apafupi amene amapitanso komweko. Aitanireni ku misonkhano. Tsimikizani mtima kuchitira umboni za uthenga wabwino kwa aliyense amene mumam’dziŵa.—Mac. 10:42; 28:23.

3 mwa Khalidwe Lanu Labwino: Khalidwe lanu labwino limanena zambiri za inu ndipo lingapereke mpata wochitira umboni. Ndiponso ‘limakometsera chiphunzitso cha Mulungu.’ (Tito 2:7, 10) Chitanidi chidwi ndi anansi anu. Khalani wochezeka ndi womvetsa zinthu. Apatseni ulemu nthaŵi imene akufuna kukhala okha pamalo aphee. Ngati wina akudwala, akomereni mtima ndi kuwathandiza. Banja lina likasamukira cha kwanuko, pitani kukalilonjera. Khalidwe lokoma mtima ngati limeneli limapereka mbiri yabwino ndipo limakondweretsa Yehova.—Aheb. 13:16.

4 mwa Maonekedwe a Zinthu Zanu: Kukhala mnansi wabwino kumaphatikizapo kusamalira nyumba yanu kukhala yooneka bwino. Nyumba ndi malo audongo ndiponso okongola zimapereka umboni wabwino. Koma nyumba yauve kapena ya zinyalala mbwee ingadodometse ena kumvetsera uthenga wa Ufumu. Choncho, mufunikadi kusamalira nyumba yanu, malo ndi galimoto zanu kukhala zaudongo ndi zabwino.

5 Posamalira anthu amene sali mu mpingo wachikristu mumasonyeza kuti mumakonda anansi anu. Kodi chingachitike n’chiyani? Mwina ena ‘angalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.’—1 Pet. 2:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena