Khalidwe Labwino Lili Chizindikiro Chapadera cha Anthu a Mulungu
1 Lerolino khalidwe labwino n’losoŵa. Kodi n’chifukwa chiyani lili losoŵa? Anthu ndi otanganidwa kwambiri moti nthaŵi zambiri sanena n’komwe mawu ofunika pa khalidwe labwino monga akuti “Chonde,” “Zikomo,” kapena “Pepani.” Mawu a Mulungu ananeneratu za kutha kwa khalidwe labwino m’masiku otsiriza, popeza amanena kuti anthu adzakhala ‘odzikonda okha, odzitamandira, odzikuza, osayamika, opanda chikondi chachibadwidwe, osakhoza kudziletsa, osakonda abwino, aliuma olimbirira.’ (2 Tim. 3:1-4) Zinthu zonsezi zimabala khalidwe loipa. Popeza Akristu ndi anthu a Mulungu, ayenera kuchenjera kuti asatengere kupanda ulemu kumene kuli m’dzikoli.
2 Kodi Khalidwe Labwino N’chiyani? Khalidwe labwino tingati ndi kusamala kwambiri malingaliro a anthu ena, kukhala ndi ena mwamtendere. Makhalidwe ena abwino ndi monga kulingalira za ena, ulemu, kukoma mtima, ndi kudzichepetsa. Khalidwe limeneli limapezeka ndi anthu okonda Mulungu ndi anansi awo. (Luka 10:27) Zimenezi si zovuta, koma n’zofunika kwambiri kuti tikhale bwino ndi ena.
3 Yesu Kristu anali chitsanzo chabwino kwambiri. Nthaŵi zonse anayendera Lamulo la Chikhalidwe lakuti: ‘Monga mufuna inu kuti anthu akuchitireni, muwachitire iwo motero.’ (Luka 6:31) Kodi sitichita chidwi ndi mmene Yesu ankasamalira ndi kukondera ophunzira ake? (Mat. 11:28-30) Khalidwe lake labwinolo sanaphunzire m’mabuku a miyambo ya makhalidwe abwino. Linachokera mu mtima woona ndi wofunitsitsa. Tiyesetse kutsatira chitsanzo chake chabwinochi.
4 Kodi Akristu azisonyeza makhalidwe abwino panthaŵi iti? Kodi ndi panthaŵi zapadera zokhazokha, pamene akufuna kusiya mbiri yabwino? Kodi ndi ofunika kokha tikafuna kukopa anthu ena? Ayi! Tizisonyeza khalidwe labwino nthaŵi zonse. Kodi ndi m’njira ziti kwenikweni zimene tiyenera kusonyeza khalidwe labwino pocheza ndi ena mu mpingo?
5 Pa Nyumba ya Ufumu: Nyumba ya Ufumu ndi malo athu olambirira. Timapezekapo chifukwa chakuti Yehova Mulungu watiitana. Chotero, timakhala alendo. (Sal. 15:1) Kodi tikafika pa Nyumba ya Ufumu timakhala alendo achitsanzo chabwino? Kodi timavala ndi kudzikongoletsa moyenera? Ndithudi tipeŵe kudzikongoletsa kosadzilemekeza kapena kopitirira muyeso. Kaya popita ku msonkhano wachigawo kapena ku misonkhano yathu yampingo ya mlungu ndi mlungu, anthu a Yehova amadziŵika chifukwa cha kuoneka kwawo bwino kumene kuli koyenera anthu olemekeza Mulungu. ( 1 Tim. 2:9, 10) Chotero, timaganizira ndiponso kusonyeza ulemu kwa Wolandira alendo wakumwamba komanso kwa alendo ena amene aitanidwa.
6 Njira ina imene timasonyeza khalidwe labwino pamisonkhano ndiyo kufika nthaŵi yabwino. Kunena zoona zimenezi n’zovuta. Ena amakhala kutali kapena ali ndi banja lalikulu lofunika kulikonzekeretsa. Koma kwapezeka kuti m’mipingo ina, pafupifupi munthu m’modzi mwa anthu anayi alionse ali ndi chizoloŵezi chofika mochedwa, nyimbo yotsegulira ndi pemphero zitatha kale. Imeneyi ndi nkhani yaikulu. Tikumbukire kuti khalidwe labwino limaphatikizapo kulingalira ena. Yehova, Wolandira alendo wathu wachifundo, wakonza maphwando auzimu ameneŵa kuti tipindule nawo. Mwa kufika mofulumira timasonyeza kuti tikuyamikira ndiponso kuti sitifuna kum’khumudwitsa. Komanso, kufika mochedwa pamisonkhano kumadodometsa ndipo kumasonyeza kusalemekeza anthu amene afika msanga.
7 Tikafika pamsonkhano kodi timaona anthu atsopano amene abwera? Kuwalandira anthu ameneŵa ndi mbali ya khalidwe labwino. (Mat. 5:47; Aroma 15:7) Moni wachimwemwe, kugwirana chanza mwaubwenzi, ndi kumwetulira mwachikondi n’zinthu zochepa, koma n’zina zimene zimatipangitsa kukhala Akristu oona. (Yoh. 13:35) Mwamuna wina paulendo wake woyamba kupita ku Nyumba ya Ufumu, atabwerako anati: “Tsiku limodzi lokha ndinakumana ndi anthu achilendo okondana zedi, amene sindinawaonepo ku tchalitchi chimene ndakulira. Zinali zachidziŵikire kuti ndapeza choonadi.” Choncho, anasintha moyo wake, ndipo patatha miyezi isanu ndi iŵiri anabatizidwa. Inde, khalidwe labwino limathandiza kwambiri!
8 Ngati timasonyeza khalidwe labwino kwa amene sitiwadziŵa, kodi si kofunika kuchita zomwezo ‘makamaka kwa iwo a pa banja la chikhulupiriro’? (Agal. 6:10) Mfundo yachikhalidwe ndi yoti: ‘Muchitire ulemu munthu wokalamba.’ (Lev. 19:32) Tisanyalanyaze anthu ameneŵa pamisonkhano yathu.
9 Kumvetsera Kwambiri: Pamisonkhano yampingo, atumiki a Mulungu achikristu amalankhula, kutipatsa mphatso zauzimu zotilimbikitsa. (Aroma 1:11) Tingasonyeze kupanda khalidwe kwambiri ngati tisinza, kutafuna masiwiti mwaphokoso, kunong’onezana pafupipafupi ndi amene tayandikana nawo, kupitapita kuchimbudzi, kuŵerenga zinthu zina, kapena kuchita zinthu zina msonkhano uli m’kati. Akulu akhale chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Khalidwe labwino lachikristu lidzatisonkhezera kulemekeza wokamba nkhani ndi uthenga wake wa m’Baibulo mwa kumvetsera kwambiri zimene akunena.
10 Komanso, posonyeza kulingalira wokamba nkhani ndi anthu omvetsera, tiyenera kusamalira zinthu zolira ndiponso matelefoni a m’manja kuti zisadodometse misonkhano yathu.
11 Khalidwe la Ana: Nthaŵi zonse makolo aziyang’anira khalidwe la ana awo. Ngati mwana ayamba kulira kapena mphulupulu msonkhano uli m’kati ndipo zikudodometsa ena, ndi bwino kutuluka naye mwamsanga kukam’tonthoza. Nthaŵi zina zimenezi zingakhale zovuta, koma kumbukirani kuti zimasonyeza kulingalira ena. Nthaŵi zambiri makolo a ana aang’ono amphulupulu amakhala kumbuyo kwa holo kuti asadodometse anthu ambiri akafuna kutuluka misonkhano ili m’kati. Komabe, ena onse opezekapo angasonyeze kulingalira mabanja otereŵa mwa kuwasiyira malo a kumbuyo kuti azikhala kumeneko, ngati akufuna.
12 Makolo aziyang’aniranso khalidwe la ana awo misonkhano isanayambe komanso itatha. Ana asamathamangethamange mu holo, chifukwa zingapangitse ngozi. Kuthamanga kuja kwa Nyumba ya Ufumu kungakhalenso kovulaza, makamaka usiku pamene munthu saona bwino. Kulankhulana mokweza panja kungadodometse anthu okhala pafupi ndi holoyo ndipo kungapereke chithunzi choipa cha kulambira kwathu. Makolo amene amayesetsa kuyang’anira ana awo m’kati ndiponso panja pa Nyumba ya Ufumu tiziwathokoza chifukwa zimenezi zimathandiza kuti kukhala kwathu pamodzi mogwirizana kukhale kokondweretsa.—Sal. 133:1.
13 Pa Phunziro la Buku: Timathokoza kuchereza kwa abale ndi alongo athu amene amaloleza nyumba zawo kuchitiramo phunziro la mpingo. Tikapitako tizisonyeza ulemu ndi kusamala katundu wawo. Tizipukuta nsapato zathu bwinobwino tisanaloŵe m’nyumba kuti tipeŵe kudetsa simenti kapena kapeti. Makolo aziyang’anira ana awo, azionetsetsa kuti akhala malo ochitira phunziro la bukuwo basi. Ngakhale kuti gululo lingakhale lochepa, ndipo tingakhale omasuka paphunziropo, tisatayirire m’nyumba za eni. Makolo aziwaperekeza ana awo akafuna kuchimbudzi. Ndiponso popeza phunziro la buku ndi msonkhano wampingo, tizivala monga mmene timavalira popita ku Nyumba ya Ufumu.
14 Makhalidwe Abwino ndi Ofunika: Khalidwe labwino sikuti limangosiya mbiri yabwino ya utumiki wathu komanso limathandiza kuti tikhale pa unansi wabwino ndi ena. (2 Akor. 6:3, 4, 6) Monga olambira a Mulungu wachimwemwe, tisamavutike kumwetulira, komanso kuvomerezana ndi ena, ngakhale kuwachitira zinthu zing’onozing’ono zimene zingawasangalatse. Makhalidwe abwino ameneŵa adzakometsa miyoyo yathu monga anthu a Mulungu.