Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/01 tsamba 8
  • Kodi Ntchito Imakulepheretsani Kulalikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ntchito Imakulepheretsani Kulalikira?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • “Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • ‘Pitirizanibe Kufunafuna Choyamba Ufumuwo’
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • “Muthange Mwafuna Ufumu”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 9/01 tsamba 8

Kodi Ntchito Imakulepheretsani Kulalikira?

1 Anthu ambiri ndi otanganidwa. Mboni za Yehova zili m’gulu la anthu otanganidwa kwambiri—timaŵerenga Mawu a Mulungu, kupezeka pamisonkhano yampingo, ndi kuloŵa muutumiki wakumunda. Ndiponso, timatanganidwa ndi ntchito yolembedwa, ntchito zapanyumba kapena zakusukulu, ndi ntchito zina zambiri, zonse zofuna nthaŵi. Izi n’zovuta kwambiri makamaka kwa mitu ya mabanja.

2 M’madera ambiri chifukwa cha mavuto a zachuma, mitu ya mabanja imagwira ntchito nthaŵi yaitali ndiponso molimbika kuti ipeze zofunika pamoyo. Ntchito ikakhala yotenga nthaŵi ndi mphamvu zawo zambiri, mitu ya mabanjayo imatsala ndi nthaŵi yochepa ya ntchito yolalikira. Popeza ndi udindo wawo kupezera mabanja awo zinthu, ena angaone kuti palibe kanthu ngakhale achite zochepa chabe muutumiki. (1 Tim. 5:8) N’zoona kuti masiku ano zimavuta kwambiri kupeza zinthu zofunika pamoyo. Koma ntchito isamalepheretse kulalikira uthenga wabwino. (Marko 13:10) Chotero, tidzipende kuti tione kuti tikuchita motani.

3 Popeza zochitika m’dzikoli zimasinthasintha, mutu wabanja ungathere nthaŵi yambiri kuntchito, pofuna kuti apeze ndalama zimene angasunge kuti zidzathandize pamavuto a mwadzidzidzi. (1 Akor. 7:31) Kugwira ntchito yochuluka kungaoneke kuti kumathandiza kupeza zinthu zakuthupi zambiri kapena kuti kumapereka mipata yambiri yoseŵera ndi kusangalala. Koma kodi banja lingasangalale ndi kukhala lokhutira kwambiri ndi zinthu zimenezi ngati zikuwalepheretsa kuchita zinthu zauzimu ndi kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse? Ndithudi tifunika kupeŵa zonse zimene zingawononge moyo wathu wauzimu. Ndi chinthu chanzeru kwambiri kumvera malangizo a Yesu ‘okundika chuma m’Mwamba,’ ndi kukhala nacho “chuma cha kwa Mulungu.”—Mat. 6:19-21; Luka 12:15-21.

4 Funani Choyamba Zinthu za Ufumu: Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuika zinthu zauzimu patsogolo pa zonse. Anawalangiza kuti: “Musadere nkhaŵa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani?” Kodi ananeneranji zimenezi? Iye anafotokoza kuti: “Pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziŵa kuti musoŵa zonse zimenezo.” Ngati timakhulupiriradi zimenezi, palibe chimene chidzatilepheretse kuchita zimene Yesu ananena kenako, kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo [zinthu zofunika] zidzawonjezedwa kwa inu.” Mulungu adzaonetsetsa kuti tili ndi zinthu zofunika zimenezi. (Mat. 6:31-33) Ino si nthaŵi yoti tidodometsedwe ndi nkhaŵa chifukwa cha zinthu zofunika pamoyo kapena chifukwa cha kufunitsitsa kukhala pamoyo wa mwanaalirenji, m’dongosolo la zinthu limene litha posachedwapa.—1 Pet. 5:7; 1 Yoh. 2:15-17.

5 Cholinga chenicheni pogwira ntchito ndicho kupeza zosoŵa zathu zakuthupi. Koma kodi timafunika zochuluka motani? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” Kodi tikuyesa kupeza zambiri kuposa zimenezi? Ngati ndi choncho, tikhoza kukolola zimene Paulo anachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” (1 Tim. 6:8, 9; Mat. 6:24; Luka 14:33) Kodi tingadziŵe bwanji kuti kufuna zinthu zambiri kukutibwezera m’mbuyo?

6 Ngati ntchito yathu imatilepheretsa kuchita zochuluka muutumiki wakumunda kapena kutilepheretsa kuona kufunika kodzimana zinthu zina chifukwa cha uthenga wabwino, ndiye kuti m’pofunika kusintha zochita zathu. (Aheb. 13:15, 16) Moyo wosalira zinthu zambiri udzathandiza kwambiri kugonjetsa cholepheretsa ulaliki wathu chimenechi. Zinthu za Ufumu zizikhala patsogolo nthaŵi zonse pamene tikugwiritsa ntchito nthaŵi ndi mphamvu zathu.

7 Ntchito Imene Siili Chabe: Mawu a Paulo akutilimbikitsa kuti tizikhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa [kwathu] sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akor. 15:58) “Ntchito ya Ambuye” yofunika kwambiri ndiyo kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kuti tichite zochuluka, mlungu uliwonse tiyenera kupatula nthaŵi ya utumiki wakumunda ndipo tiziyesetsa kusagwiritsa ntchito nthaŵi imeneyo pa zinthu zina. (Aef. 5:15-17) Tikatero ndiye kuti ntchito kapena china chilichonse sichidzalepheretsa utumiki wathu.

8 Ngati tidzipereka kuuza ena choonadi cha m’Baibulo, timapeza chimwemwe chachikulu chimene chimadza chifukwa chopatsa. (Mac. 20:35) Mwakugwira ntchito yolalikira Ufumu, tingadikire za m’tsogolo ndi chikhulupiriro “pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito [yathu], ndi chikondicho [ti]dachionetsera ku dzina lake.”—Aheb. 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena