Madalitso Amene Amabwera Chifukwa Choyamikira Chikondi cha Yehova—Gawo 1
1 Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tikonda ife, chifukwa anayamba [Yehova] kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Tikaganizira zonse zimene Yehova watipatsa, nafenso timalimbikitsidwa kusonyeza kuyamikira kwathu ndi mtima wonse. Yesu anapereka chitsanzo cha zimenezi mwa kulalikira mofunitsitsa dzina la Mulungu ndi Ufumu wake. (Yoh. 14:31) Ndi bwino kuona njira zina zomwe tingasonyezere kuyamikira kwathu chikondi cha Yehova komanso kuona madalitso amene tingapeze.
2 Kupita Kunyumba ndi Nyumba: Yesu anaphunzitsa ophunzira ake momwe angachitire ntchito yolalikira Ufumu. Malangizo ake amasonyeza bwinobwino kuti ankapita kunyumba ndi nyumba, kukafalitsa uthenga wabwino. (Luka 9:1-6; 10:1-7) Kuti tipitirizebe kupita kukhomo ndi khomo ngakhale tipeze anthu opanda chidwi ndi otsutsa, tifunika kukonda Mulungu ndi anansi. Komabe, kuchita zimenezi kumapindulitsa ife tomwe chifukwa chikhulupiriro chathu chimalimba ndipo chiyembekezo chathu chimakhala choŵala.
3 Pogwira ntchitoyi motsogozedwa ndi angelo, tapeza anthu ambiri amene ali anjala ndi aludzu mwauzimu. (Chiv. 14:6) Eninyumba ena anena kuti nthaŵi yomwe Mboni zinkafika panyumba pawo n’kuti akupemphera kuti athandizidwe. Alongo aŵiri ndi mwana anali kulalikira kunyumba ndi nyumba pa chilumba cha Caribbean. Alongo aja ataganiza zobwerera kwawo, mwana uja anapita yekha kunyumba ina ndipo anagogoda. Ndiyeno kunabwera mtsikana kudzatsegula chitseko. Alongo aja ataona zimenezi, anam’tsatira kukalankhula naye. Mtsikana uja anawauza kuti aloŵe m’nyumba ndipo anati wangotha kumene kum’pempha Mulungu kuti atumize Mboni kuti zidzam’phunzitse Baibulo!
4 Kulalikira Mumsewu: Popeza m’malo ena n’kovuta kupeza anthu panyumba, kulalikira mumsewu ndi njira yabwino kwambiri yowauzira anthu uthenga wabwino. Komanso, anthu ambiri amakhala m’dera la nyumba za mipanda kapena zachitetezo champhamvu komwe sitingapite kukhomo ndi khomo. Komabe, kuyamikira kwathu chikondi cha Yehova kumatilimbikitsa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse umene tingapeze kuuza anthu uthenga wa Ufumu, kuphatikizapo ulaliki wa mumsewu.—Miy. 1:20, 21.
5 Kubwerera Kumene Tinapitako Kale: Popeza tikufunafuna anthu amene ali “ozindikira zosoŵa zawo zauzimu,” tikufuna kuchita zomwe tingathe kuti tithetse vutoli. (Mat. 5:3, NW) Izi zimafunika kupitakonso kukathirira mbewu za choonadi zimene tinaoka. (1 Akor. 3:6-8) Mlongo wina ku Australia anagaŵira thirakiti kwa mayi wina amene ankaoneka ngati sankafuna. Komabe, mlongoyo analimbikira kupita kwa mayiyo ngakhale samam’peza panyumba. Mlongo wathuyu atam’peza mayi uja panyumba, anapeza kuti atasiyana naye pa ulendo woyamba uja mayiyo anakagula Baibulo lokwera mtengo. Mlongo uja anayamba kuphunzira naye!
6 Kuchititsa Maphunziro a Baibulo: Iyi ndi mbali yosangalatsa ndi yopindulitsa kwambiri ya utumiki wathu. Ndi dalitso zedi kuthandiza anthu kuphunzira za Yehova, kuwaona akusintha moyo wawo kuti am’kondweretse, komanso kuonerera ubatizo wawo wachikristu posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu!—1 Ates. 2:20; 3 Yoh. 4.
7 M’kope lathu lotsatira, tidzapenda njira zina zimene timapezera madalitso amene amabwera chifukwa choyamikira chikondi cha Yehova.