Kuthandiza Ena Kulemekeza Yehova
1 Anthu padziko lonse akuuzidwa uthenga wofunika kwambiri, wakuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruzo chake; ndipo m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:6, 7) Ndi mwayi wathu kugwira nawo ntchito youza anthu uthenga umenewu. Kodi n’chiyani chimene anthu akufunika kudziŵa zokhudza Yehova kuti amuope ndi kum’lambira?
2 Dzina Lake: Anthu akufunika kuti azitha kusiyanitsa dzina la Mulungu yekha woona ndi la milungu yambiri yonyenga imene anthu amalambira masiku ano. (Deut. 4:35; 1 Akor. 8:5, 6) Ndipotu, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito dzina lokwezeka lakuti Yehova maulendo oposa 7,000. Ngakhale kuti n’koyenera kuona pofunika kutchula dzina la Mulungu, tisamalibise kapena kupeŵa kuligwiritsa ntchito. Mulungu akufuna kuti anthu onse alidziŵe dzina lake.—Sal. 83:18.
3 Makhalidwe Ake: Kuti anthu alemekeze Yehova, akufunika kudziŵa kuti iye ndi Mulungu wamtundu wanji. Tiyenera kuwaphunzitsa kuti ndi wachikondi kwambiri, wanzeru zoposa, wachilungamo chokhachokha ndiponso wamphamvuyonse. Komanso tiwaphunzitse za chifundo chake, kukoma mtima kwake ndi makhalidwe ake ena apadera. (Eks. 34:6, 7) Ayeneranso kuphunzira kuopa Mulungu ndi kum’lemekeza kwambiri chifukwa, kuti akhale ndi moyo m’pofunika kuti Yehova atiyanje.—Sal. 89:7.
4 Kuyandikana ndi Mulungu: Kuti anthu apulumuke chiŵeruzo cha Mulungu chikubwerachi, akufunika kuitanira pa Yehova mwachikhulupiriro. (Aroma 10:13, 14; 2 Ates. 1:8) Izi sizikutanthauza kungophunzira dzina la Mulungu ndi makhalidwe ake basi. Tiyenera kuthandiza anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, ndikuti am’khulupirire ndi mtima wawo wonse. (Miy. 3:5, 6) Akamagwiritsa ntchito zimene akuphunzira, kupemphera kwa Mulungu moona mtima, ndi kuona kuti akuwathandiza pamoyo wawo, chikhulupiriro chawo chidzakula, ndipo zidzawathandiza kuyandikana ndi Yehova.—Sal. 34:8.
5 Tiyenitu tilengeze mwachangu dzina la Mulungu ndi kuthandiza ena kuti am’khulupirire ndi mtima wawo wonse ndiponso kuti amuope. Tikhoza kuthandiza ena ambiri kudziŵa Yehova ndi kumulemekeza monga “Mulungu wa chipulumutso” chawo.—Sal. 25:5.