Ganizirani Okalamba Omwe Ali Okhulupirika
1 Ngakhale kuti Anna wa zaka 84 anali mkazi wamasiye, ‘sanali kuchoka ku Kachisi.’ Yehova anam’dalitsa mwapadera chifukwa cha kukhulupirika kwake. (Luka 2:36-38) Masiku ano, abale ndi alongo ambiri amasonyeza mtima ngati wa Anna ngakhale kuti ali pamavuto. Nthaŵi zina anthu okhulupirika ameneŵa amakhumudwa pamene akulimbana ndi matenda kapena ngati ukalamba ukuwalepheretsa kuchita zinthu zina. Tiyeni tione zina mwa njira zabwino zimene tingawalimbikitsire ndiponso kuwathandiza kukhalabe ndi chizoloŵezi chabwino pa zinthu zauzimu.
2 Misonkhano Ndiponso Utumiki: Ngati anthu ena mwachikondi awathandiza pa kayendedwe, okalamba ambiri okhulupirika angamapezeke mosavuta pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse. Zimenezi zimawalimbikitsa mwauzimu atumiki okhulupirika ndi akalekale ameneŵa, komanso zimapindulitsa anthu pampingopo. Kodi munayamba mwachitapo ntchito yabwino imeneyi?—Aheb. 13:16.
3 Akristu oona amapeza chimwemwe mwa kutenga mbali mu utumiki nthaŵi zonse. Koma anthu okalamba ndi odwaladwala, n’kovuta kuchita zimenezi. Kodi n’zotheka kuti mmodzi wa okondedwa ameneŵa akhale ‘wantchito mnzanu’ mwa kuyenda naye pochita mtundu wina wa ulaliki? (Aroma 16:3, 9, 21) Mwina mungawapemphe kudzachitira nanu limodzi ulaliki wa patelefoni kapena kupitira limodzi ku ulendo wobwereza kapenanso ku phunziro la Baibulo. Ngati wokalambayo amangokhala panyumba, kodi wophunzira Baibulo angamabwere kunyumba kwakeko kuti muziphunzirira komweko?
4 Phunziro Ndiponso Mayanjano: Nthaŵi zina, ena amapempha munthu wokalamba kapena wodwaladwala kudzachita nawo phunziro lawo la banja, ngakhalenso kukachitira phunzirolo kunyumba kwake. Mayi wina anapita ndi ana ake aŵiri kwa mlongo wina wokalamba kukachita phunziro lawo mogwiritsa ntchito Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndipo onse analimbikitsidwa ndi mayanjano amene analipo. Anthu ameneŵa amasangalalanso kuwaitana kukadya nawo chakudya kapena kukachita nawo zosangalatsa zina. Ngati okalambawo kapena odwaladwalawo ali ofooka kwambiri moti sangathe kucheza kwa nthaŵi yaitali, mwina mungapite kwawo kwa nthaŵi yochepa kukawaŵerengera, kupemphera nawo limodzi kapena kukawauza nkhani ina yosangalatsa.—Aroma 1:11, 12.
5 Yehova amaona anthu okalamba omwe ali okhulupirika kukhala ofunika kwambiri. (Aheb. 6:10, 11) Tingamutsanzire mwa kuwalemekeza ndiponso kuwathandiza kukhalabe ndi chizoloŵezi chabwino pa zinthu zauzimu.