Kukwaniritsa Kudzipatulira Kwathu
1 Mwina mwabatizidwa posachedwapa kapena munabatizidwa kale. Mulimonsemo, mukukumbukirabe chochitika chapadera chimenechi pamoyo wanu. Ubatizo wathu sindiwo mapeto a zonse ayi koma ndi kuyamba kwa utumiki wodzipatulira wa moyo wathu wonse umene ungafike mpaka muyaya. (1 Yoh. 2:17) Kodi kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kumafunikira chiyani?
2 Kutsanzira Chitsanzo cha Kristu: Yesu atabatizidwa, “anayamba ntchito yake” yolalikira “Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 3:23; 4:43) Ifenso tikasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Yehova mwa ubatizo, timakhala atumiki oikidwa a uthenga wabwino. Ngakhale kuti m’pofunika nthaŵi ndi khama kuti tipeze zofunika pamoyo, ntchito yathu yaikulu ndiyo utumiki wachikristu. (Mat. 6:33) M’malo mofunitsitsa chuma kapena kutchuka, anthu odzipatulira kwa Mulungu amafuna ‘kulemekeza utumiki wawo’ ngati mmene mtumwi Paulo anachitira. (Aroma 11:13) Kodi mumaukonda ndi mtima wonse mwayi wanu wotumikira Yehova ndi kuchita utumikiwo mwakhama?
3 Mofanana ndi mmene Yesu anachitira, tifunika ‘kukaniza Mdyerekezi.’ (Yak. 4:7) Yesu atabatizidwa, Satana anamuyesa, ndipo amateronso ndi atumiki a Yehova odzipatulira masiku ano. (Luka 4:1-13) Popeza kuti tikukhala m’dziko la Satana, tifunika kudziletsa ndi kupeŵa chilichonse chimene chingadetse maganizo athu kapena kuipitsa mtima wathu. (Miy. 4:23; Mat. 5:29, 30) Akristu akulangizidwa kuti ‘sangathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.’ (1 Akor. 10:21) Zimenezi zimafuna kuti tipeŵe zinthu zoipa pamene tikusangalala, mayanjano oipa, ndi zoipa zimene tingakumane nazo pogwiritsira ntchito makompyuta. Zimafunanso kuti tipeŵe zinthu zokhudzana ndi ampatuko. Kukhala maso pa machenjera ameneŵa ndi enanso a Satana kudzatithandiza kukwaniritsa kudzipatulira kwathu.
4 Kugwiritsira Ntchito Zimene Mulungu Watipatsa: Pofuna kutithandiza kukwaniritsa kudzipatulira kwathu, Yehova wapereka thandizo la Mawu ake ndi mpingo wachikristu. Khalani ndi chizoloŵezi choŵerenga Baibulo ndi kupemphera kwa Yehova tsiku ndi tsiku. (Yos. 1:8; 1 Ates. 5:17) Sangalalani ndi misonkhano ya mpingo. (Sal. 122:1) Yanjanani ndi anthu oopa Yehova amene amasunga malamulo ake.—Sal. 119:63.
5 Pothandizidwa ndi Yehova, mutha kukwaniritsa kudzipatulira kwanu kwa iye ndi kukhala ndi mwayi wom’tumikira mpaka muyaya.—Sal. 22:26, 27; Afil. 4:13.