Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiyenera kutsatira malangizo ati polalikira kwa akaidi?
Padziko lonse lapansi pali akaidi pafupifupi 8,000,000 ndipo ena mwa iwo amachita chidwi ndi uthenga wabwino. (1 Tim. 2:4) Mwezi uliwonse ofesi ina ya nthambi imalandira makalata pafupifupi 1,400 ochokera kwa akaidi ndi achibale awo, opempha mabuku kapena munthu wina kuti awayendere. Ngakhale kuti akaidi ambiri amakhaladi ndi chidwi, kwapezeka kuti ena amangonamizira n’cholinga chodyera anthu a Mulungu. Pachifukwa chimenechi, anthu onse ayenera kutsatira malangizo otsatiraŵa polalikira kwa akaidi.
Nthaŵi zambiri akaidi amalalikiridwa kudzera m’makalata. Ndibwino kwambiri kuti alongo asamalembere makalata akaidi aamuna, ngakhale cholinga chawo chili kuwathandiza mwauzimu. Abale oyenerera okha ndi amene ali ndi udindo umenewu. Alongo oyenerera angauzidwe kuti azilembera makalata akaidi aakazi amene achitadi chidwi ndi choonadi cha m’Baibulo. Osatumizira akaidi ndalama kapena mphatso ngakhale atapempha.
Mkaidi akachita chidwi, perekani dzina ndi adiresi yake ku mpingo wa m’gawo limene muli ndendeyo. Kaŵirikaŵiri abale oyenerera kumeneko amadziŵa mochitira ndi chilichonse chimene chingabukepo. Ngati mpingowo simukuudziŵa, tumizani zimenezo ku ofesi ya nthambi.
N’kololeka kuti abale amene auzidwa kupita ku ndendeko azichititsa misonkhano ndi akaidi, kuti akaidi ambiri aziphunzirira pamodzi. Komabe, zochitika zapadera zimene ofalitsa angacheze mwaufulu ndi akaidi zisamachitikire ku ndende. Komanso si nzeru ofalitsa kupita ku ndende wambawamba ndi kucheza kwambiri ndi akaidi.
Tiyenitu tikhale “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda” pouza akaidi uthenga wabwino.—Mat. 10:16.