Kupanga Ubwenzi Wolimba ndi Yehova
1. Kodi mlongo wina anazindikira chiyani pankhani ya zochita zake zauzimu?
1 “Ndakhala m’choonadi kwa zaka pafupifupi 20 mwa kungopita kumisonkhano ndi kuchita utumiki wakumunda,” anatero mlongo wina wachikristu. Komabe, anapitiriza kuti: “Ndadziŵa kuti ngakhale kuti zinthu zimenezi n’zofunika, kuchita zokhazi sikungandithandize pamene zinthu ziyamba kuvuta. . . . Tsopano ndazindikira kuti ndiyenera kusintha maganizo anga ndi kuyamba pulogalamu yochita phunziro lopindulitsa kuti ndim’dziŵedi Yehova ndi kumukonda ndiponso kuyamikira zimene Mwana wake watipatsa.”
2. N’chifukwa chiyani n’kofunika kupanga ubwenzi wolimba ndi Yehova?
2 Kupanga ubwenzi wolimba ndi Yehova kumafuna khama. Kumafuna zambiri osati kungotsatira ndandanda ya zochita zachikristu. Ngati tilephera kulankhula nthaŵi zonse ndi Yehova, m’kupita kwa nthaŵi akhoza kukhala ngati munthu amene kale anali mnzathu wapamtima amene tinaleka kulankhulana naye. (Chiv. 2:4) Tiyeni tione momwe phunziro la Baibulo laumwini ndi pemphero zingatithandizire kupanga “ubwenzi” wolimba ndi Yehova.—Sal. 25:14, NW.
3. Kodi phunziro laumwini liyenera kuchitika bwanji kuti tiyandikire kwa Mulungu?
3 Pemphero ndi Kusinkhasinkha N’zofunika: Phunziro laumwini limene limafikadi pamtima limafuna zambiri osati kungodula mizere kunsi kwa mfundo zazikulu mu nkhani yophunziridwa ndiponso kungoŵerenga malemba amene aperekedwa koma sanagwidwe mawu. Limafunika kuti tisinkhesinkhe zimene nkhaniyo ikusonyeza ponena za njira za Yehova, miyezo yake, ndi umunthu wake. (Eks. 33:13) Kumvetsa nkhani zauzimu kumakhudza maganizo anthu ndipo kumatilimbikitsa kuganizira za moyo wathu. (Sal. 119:35, 111) Pochita phunziro laumwini tizikhala ndi cholinga choyandikira kwa Yehova. (Yak. 4:8) Kuphunzira mofatsa kumafuna nthaŵi komanso malo abwino, ndipo kuphunzira nthaŵi zonse kumafuna kudziletsa. (Dan. 6:10) Ngakhale kuti mumakhala ndi zochita zambiri pamoyo wanu, kodi tsiku lililonse mumapatula nthaŵi kuti musinkhesinkhe mikhalidwe yabwino kwambiri ya Yehova?—Sal. 119:147, 148; 143:5.
4. Kodi kupemphera tisanayambe phunziro laumwini kumatithandiza bwanji kupanga ubwenzi wolimba ndi Yehova?
4 Pemphero lochokera pansi pa mtima n’lofunika kwambiri kuti phunziro laumwini likhale latanthauzo. Tifunika mzimu woyera wa Mulungu kuti mfundo za m’Baibulo zikhudze mtima wathu ndi kutilimbikitsa ‘kutumikira Mulungu mom’kondweretsa, ndi kum’chitira ulemu ndi mantha.’ (Aheb. 12:28) Choncho, nthaŵi iliyonse tisanayambe phunziro tiziyamba tapempha Yehova kuti atipatse mzimu wake. (Mat. 5:3) Pamene tisinkhasinkha Malemba ndi kugwiritsa ntchito zofalitsa zotithandiza kuphunzira zimene gulu la Yehova limapereka, timam’tsanulira Yehova mtima wathu. (Sal. 62:8) Kuchita phunziro mwa njira imeneyi ndi mbali ya kulambira imene timasonyeza kudzipereka kwathu kwa Yehova ndipo kumakulitsa chikondi chathu pa iye.—Yuda 20, 21.
5. N’chifukwa chiyani n’kofunika kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse?
5 Monga mmene maubwenzi onse amakhalira, ubwenzi wathu ndi Yehova umafunika kuusamalira nthaŵi zonse kuti upitirize kukula kwa moyo wathu wonse. Chotero, tizipeza nthaŵi tsiku lililonse kuti tiyandikire kwa Mulungu, podziŵa kuti kenako iye adzayandikira kwa ife.—Sal. 1:2, 3; Aef. 5:15, 16.