Umodzi Weniweni Wachikristu—Kodi Umatheka Motani?
1 Kodi n’chiyani chingapangitse anthu oposa sikisi miliyoni ochokera m’mayiko 234 ndiponso olankhula zinenero pafupifupi 380 kukhala ogwirizana? Ndi kulambira Yehova Mulungu yekha basi. (Mika 2:12; 4:1-3) Mboni za Yehova zimadziŵa kuti panopo umodzi weniweni wachikristu si nkhambakamwa chabe. Monga “gulu limodzi” la “mbusa mmodzi,” timayesetsa kukaniratu mzimu wosagwirizana wa dzikoli.—Yoh. 10:16; Aef. 2:2.
2 Cholinga chotsimikizirika cha Mulungu n’chakuti zolengedwa zonse zanzeru zigwirizane pa kulambira koona. (Chiv. 5:13) Popeza Yesu anadziŵa kufunika kokhala ogwirizana, iye anapemphera ndi mtima wonse kuti otsatira ake akhale ogwirizana. (Yoh. 17:20, 21) Kodi aliyense wa ife angalimbikitse motani umodzi wachikristu mu mpingo?
3 Mmene Timapezera Umodzi: Popanda Mawu a Mulungu ndi mzimu wake, umodzi wachikristu ngosatheka. Kugwiritsa ntchito kwathu zimene timaŵerenga m’Baibulo kumatheketsa kuti mzimu wa Mulungu uzigwira ntchito mwaufulu pamoyo wathu. Zimenezi zimatithandiza “kusunga umodzi wa mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.” (Aef. 4:3) Zimatithandizanso kukhala wololerana wina ndi mnzake mwachikondi. (Akol. 3:13, 14; 1 Pet. 4:8) Kodi inu mumalimbikitsa umodzi mwa kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse?
4 Ntchito yathu yolalikira ndi kupanga ophunzira imatipangitsanso kuti tikhale ogwirizana. Pamene tikulalikira pamodzi ndi ena mu utumiki wachikristu, ‘pogwirira pamodzi chikhulupiriro cha uthenga wabwino,’ ‘timakhala othandizana m’choonadi.’ (Afil. 1:27; 3 Yoh. 8) Tikamachita zimenezi, chikondi chimene chimapangitsa kuti tikhale ogwirizana mu mpingo chimalimba. Bwanji osapemphako wina amene simunalalikire naye posachedwapa kuti mupite naye mu utumiki wakumunda mlungu uno?
5 Ndifetu odala zedi chifukwa chokhala mbali ya ubale wokhawo weniweni wa padziko lonse masiku ano! (1 Pet. 5:9) Posachedwapa, anthu ambirimbiri adzionera okha mgwirizano wa padziko lonse umenewu pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.” Tiyenitu aliyense payekha alimbikitse mgwirizano wamtengo wapataliwu mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, mwa kuthetsa kusiyana maganizo mwachikondi, ndiponso mwa kulalikira uthenga wabwino ‘tonse pamodzi.’—Aroma 15:6.