Sonyezani Kuyamikira Kwanu
1 Ngakhale kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa,” tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira Yehova. (2 Tim. 3:1) Chifukwa chachikulu mwa zifukwa zimenezi ndicho mphatso ya mtengo wapatali ya Mwana wake amene anamupereka m’malo mwathu. (Yoh. 3:16) Ndiponso, ngakhale kuti anthu amene ali m’zipembedzo zonyenga ali ndi njala yauzimu, ife tili ndi chakudya chambiri chauzimu. (Yes. 65:13) Tili mu ubale wa padziko lonse ndipo tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito yosangalatsa kwambiri yokulitsa kulambira koona. (Yes. 2:3, 4; 60:4-10, 22) Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira Yehova chifukwa cha madalitso amene amatipatsa?—Akol. 3:15, 17.
2 Kutumikira Mosangalala Ndiponso ndi Mtima Wonse: Pofotokoza za kupereka zinthu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akor. 9:7) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pankhani ya kutumikira kwathu Mulungu. Timasonyeza kuyamikira pamene tikonda kwambiri choonadi, kukhala osangalala pa misonkhano yachikristu, kukhala achangu mu utumiki wa kumunda, ndiponso kukondwera pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu.—Sal. 107:21, 22; 119:14; 122:1; Aroma 12:8, 11.
3 Mu Israyeli wakale, Chilamulo sichinanene kuti munthu azipereka zinthu zochuluka bwanji pa zopereka zina. Wolambira aliyense akanasonyeza kuyamikira kwake mwa kupereka “monga mwa mdalitso wa Yehova” umene analandira. (Deut. 16:16, 17) N’chimodzimodzinso masiku ano, mtima woyamikira udzatilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu pogwira ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. Ena amagwiritsa ntchito nthaŵi imene ali patchuti kuntchito ndi kusukulu powonjezera nthaŵi imene amathera mu utumiki wakumunda, ngakhalenso kuchita upainiya wothandiza. Kodi mungawonjezere utumiki wanu?
4 Kuchulukitsa Chiyamiko: Njira yaikulu imene timasonyezera kuyamikira kwathu Yehova ndiyo pemphero. (1 Ates. 5:17, 18) Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti ndi chikhulupiriro ‘tichulukitse chiyamiko.’ (Akol. 2:7) Ngakhale pamene tatanganidwa kwambiri kapena tikuvutika maganizo, nthaŵi zonse tiyenera kuphatikizapo kuyamikira pa mapemphero athu a tsiku ndi tsiku. (Afil. 4:6) Inde, mwa kuchita utumiki ndiponso mwa kupemphera, tiyeni ‘tichulukirenso mwa Mulungu mwa mayamiko ambiri.’—2 Akor. 9:12.