‘Kulitsani’ Chikondi
1. Kodi tonsefe tili ndi udindo wotani?
1 Mu ubale wachikristu, tonsefe tili ndi udindo wothandizira kuti pakhale ubwenzi mumpingo. (1 Pet. 1:22; 2:17) Ubwenzi woterowo umakhalapo ngati ‘tikulitsa’ chikondi chathu kwa wina ndi mnzake. (2 Akor. 6:12, 13) N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuwadziŵa bwino abale ndi alongo athu?
2. N’chifukwa chiyani n’kofunika kupanga ubwenzi ndi okhulupirira anzathu?
2 Maubwenzi Amalimba: Tikawadziŵa bwino okhulupirira anzathu, timafika poyamikira kwambiri chikhulupiriro chawo, kupirira kwawo, ndiponso makhalidwe awo ena abwino. Zofooka zawo zimaoneka zazing’ono, ndipo ubwenzi wathu umalimba. Tikadziŵana bwino timatha kumangirirana ndi kulimbikitsana. (1 Ates. 5:11) Tingakhale ‘chotonthoza mtima’ kwa wina ndi mnzake kuti tikanize zinthu zoipa za m’dziko la Satanali. (Akol. 4:11) Malinga ndi mmene masiku otsiriza odzala ndi mavutoŵa alili, tikuyamikira kwambiri kuti tili ndi mabwenzi abwino kwambiri pakati pa anthu a Yehova.—Miy. 18:24.
3. Kodi tingakhale bwanji otonthoza mtima kwa ena?
3 Mabwenzi apamtima angatipatse mphamvu ndi kutilimbikitsa mwapadera tikakumana ndi mavuto aakulu. (Miy. 17:17) Mkristu wina amene anali kuvutika ndi maganizo odziona kuti ndi wopanda pake anati: “Panali mabwenzi amene ankandiuza zinthu zabwino zimene ndimachita pondithandiza kugonjetsa maganizo ofooketsa amene ndinali nawo.” Mabwenzi oterowo ndi dalitso lochokera kwa Yehova.—Miy. 27:9.
4. Kodi tingatani kuti tiwadziŵe bwino ena mumpingo?
4 Chitani Chidwi ndi Anthu Ena: Kodi tingakulitse bwanji chikondi chathu kwa okhulupirira anzathu? Kuwonjezera pa kupatsa moni ena pamisonkhano yachikristu, yesetsani kulankhula nawo zinthu zothandiza. Asonyezeni chidwi, koma musaloŵerere nkhani zokhudza iwowo paokha zimene n’zachinsinsi. (Afil. 2:4; 1 Pet. 4:15) Njira ina yosonyezera chidwi kwa ena ndiyo kuwaitana kuti mudzadye nawo limodzi chakudya. (Luka 14:12-14) Kapena mungakonze zoti mugwire nawo ntchito limodzi mu utumiki wa kumunda. (Luka 10:1) Pamene tikuchitapo kanthu kuti tidziŵane bwino ndi abale athu, timalimbikitsa mgwirizano mumpingo.—Akol. 3:14.
5. Kodi ndi njira ina iti imene tingapangire maubwenzi ndi anthu osiyanasiyana?
5 Kodi timakonda kusankha mabwenzi athu apamtima pakati pa anthu okhawo amene tikufanana nawo msinkhu kapena amene zokonda zawo n’zofanana ndi zathu? Tisalole kuti zinthu zimenezi zitilepheretse kupanga ubwenzi ndi anthu ena mumpingo. Davide ndi Yonatani komanso Rute ndi Naomi anapanga maubwenzi olimba kwambiri ngakhale kuti anali osiyana misinkhu ndiponso miyoyo yawo inali yosiyana. (Rute 4:15; 1 Sam. 18:1) Kodi mungapange maubwenzi ndi anthu osiyanasiyana? Kuchita zimenezo kudzabweretsa madalitso osayembekezeka.
6. Kodi ndi phindu lanji limene limakhalapo tikakulitsa chikondi chathu kwa abale athu?
6 Mwa kukulitsa chikondi chathu kwa ena, timalimbikitsana ndipo timalimbikitsa mtendere mumpingo. Ndiponso, Yehova amatidalitsa chifukwa cha chikondi chimene timasonyeza kwa abale athu. (Sal. 41:1, 2; Aheb. 6:10) Bwanji osakhala ndi cholinga choti mudziŵane ndi anthu ambiri monga momwe mungathere?