Yehova Amathandiza Anthu Amene Amamudalira
1 Anthu ambiri amaona ndalama, ulamuliro, ndiponso kukhala ndi luso lapadera kuti ndiye chinsinsi choti munthu zimuyendere bwino. (Sal. 12:4; 33:16, 17; 49:6) Koma amene amaopa Yehova ndi kumudalira, Baibulo limawatsimikizira kuti iye “ndiye mthandizi wawo ndi chikopa chawo.” (Sal. 115:11) Tiyeni tikambirane mbali ziŵiri zimene tifunika kusonyeza kudalira Yehova.
2 Monga Atumiki Achikristu: Tikamakamba nkhani mumpingo kapena tikamaphunzitsa mu utumiki wa kumunda, tiyenera kudalira Mulungu wathu. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, sanadalire nzeru zake kapena luso lake, m’malo mwake anadalira Atate wake wakumwamba ndi mtima wonse. (Yoh. 12:49; 14:10) Ifenso tifunika kuchita chimodzimodzi. (Miy. 3:5-7) Zochepa zimene timachita zingalemekeze Yehova ndiponso zingapindulitse ena ngati iyeyo watithandiza.—Sal. 127:1, 2.
3 Timasonyeza kudalira Yehova mwa kupemphera kuti atitsogolere ndiponso kuti atithandize ndi mzimu woyera. (Sal. 105:4; Luka 11:13) Ndiponso, timasonyeza kudalira Mulungu mwa kuphunzitsa za m’Mawu ake, Baibulo. Uthenga wa m’Baibulo uli ndi mphamvu yokhudza mtima ndiponso yosintha miyoyo. (Aheb. 4:12) ‘Tikamatumikira mu mphamvu imene Mulungu watipatsa,’ Yehova amalemekezedwa.—1 Pet. 4:11.
4 Polimbana ndi Mavuto: Tifunikanso kudalira Yehova kuti atithandize polimbana ndi mavuto. (Sal. 46:1) Mwachitsanzo, bwana anganyinyirike zoti atipatse tchuti kuti tikapezeke pamsonkhano waukulu, kapena tingakhale tikukumana ndi mavuto m’banja mwathu. Timasonyeza kudalira Yehova mwa kum’pempha ndi mtima wonse ndiponso mwa kutsatira malangizo amene iye amapereka kudzera m’Mawu ake ndi m’gulu lake. (Sal. 62:8; 119:143, 173) Akachita zimenezi, atumiki a Yehova amathandizidwa pa miyoyo yawo.—Sal. 37:5; 118:13, 16.
5 Yehova mwiniwakeyo akutitsimikizira kuti: “Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova.” (Yer. 17:7) Tiyenitu tisonyeze kuti tikumudalira pa zonse zimene timachita.—Sal. 146:5.