Kupirira Kuli ndi Mphoto Yake
1 “Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiriro.” (Luka 21:19) Mawu ameneŵa amene ndi mbali ya ulosi umene Yesu ananena wokhudza “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” amasonyeza bwino lomwe kuti pamene tikukhala okhulupirika, tiyeneranso kukhala okonzekera kukumana ndi ziyeso. Koma mwa mphamvu ya Yehova, aliyense wa ife akhoza ‘kulimbika chilimbikire kufikira chimaliziro’ ndi ‘kupulumuka.’—Mat. 24:3, 13; Afil. 4:13.
2 Zinthu zingakhale zovuta tsiku lililonse chifukwa cha chizunzo, matenda, mavuto a zachuma, ndi kuvutika maganizo. Komabe, tisaiwale kuti Satana akuyesetsa kuwononga chikhulupiriro chathu mwa Yehova. Tsiku lililonse limene takhulupirika kwa Atate wathu, timakhala titathandizira kupereka yankho kwa Wotonza ameneyo. N’zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti “misozi” imene timagwetsa pokumana ndi mavuto siiŵalika! Yehova amaiona kukhala yamtengo wapatali, ndipo kukhulupirika kwathu kumasangalatsa mtima wake!—Sal. 56:8; Miy. 27:11.
3 Ziyeso Zimatiyenga: Mavuto angavumbule mbali inayake imene sili bwino pa chikhulupiriro chathu kapena pa umunthu wathu, monga kunyada kapena kusaleza mtima. M’malo moyesa kuzemba kapena kuthetsa ziyeso potsata njira zomwe si za m’malemba, tifunika kumvera langizo la Mawu a Mulungu lakuti “chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kupirira ziyeso mokhulupirika kumatithandiza ‘kukhala angwiro ndi opanda chilema.’ (Yak. 1:2-4) Kupirira kungatithandize kukhala ndi makhalidwe ena ofunika, monga kulolera, kuganizira ena ndiponso chifundo.—Aroma 12:15.
4 Chikhulupiriro Choyesedwa: Tikapirira ziyeso, timakhala ndi chikhulupiriro choyesedwa chimene chili chamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. (1 Pet. 1:6, 7) Chikhulupiriro chotero chimatithandiza kuti tidzakhale olimba pamene tidzakumana ndi ziyeso zina m’tsogolo. Kuwonjezera pamenepo, timatha kuona kuti Mulungu akutiyanja, ndipo zimenezi zimalimbitsa chiyembekezo chathu. Chiyembekezo chathu chikalimba, chimakhala chodalirika kwambiri.—Aroma 5:3-5.
5 Mphoto yaikulu ya kupirira yalembedwa pa Yakobo 1:12, pamene pamati: “Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo.” Ndiyetu, tiyeni tikhalebe olimba pa kudzipereka kwathu kwa Yehova, podziŵa kuti adzapereka mphoto yaikulu kwa “akum’konda Iye.”