Sukulu Yophunzitsa Utumiki—Khomo Lalikulu Loloŵera M’ntchito Yochuluka
1 Yehova ananeneratu kudzera mwa mneneri Yeremiya kuti: ‘Ndidzaikira [anthu anga] abusa amene adzawadyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhaŵa, sipadzasoŵa mmodzi yense.” (Yer. 23:4) Ntchito ya ubusa imeneyi ikuchitika masiku ano pakati pa anthu a mitundu yonse. Amene akuchita ntchito imeneyi m’mipingo ndi akulu zikwizikwi. Kuwonjezera pamenepo, pali achinyamata ambiri monga mame amene adzipereka okha kuti atumikire Yehova. (Sal. 110:3) Abale odzichepetsa ameneŵa alidi dalitso lalikulu ku mipingo ya anthu a Mulungu! Pamene ntchito yauzimu yotuta imeneyi ikupitirira, pakufunika abale oyenerera amene angadzipereke kuti atumikire abale awo.
2 Njira yabwino kwambiri yophunzitsira akulu ndi atumiki otumikira osakwatira kuti akhale ndi maudindo owonjezereka ndiyo Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Kuchokera pamene sukulu imeneyi inayamba mu 1987, ophunzira oposa 22,000 ochokera ku mayiko pafupifupi 140 alandira maphunziro ameneŵa m’makalasi okwana 999. Kwa abale ameneŵa, sukulu imeneyi yakhala khomo lalikulu loloŵera m’ntchito yochuluka.—1 Akor. 16:9.
3 Cholinga Chake cha Sukulu Imeneyi: Cholinga cha Sukulu Yophunzitsa Utumiki imeneyi ndicho kuphunzitsa amuna oyenerera kuti akhale okonzeka kusamalira maudindo kulikonse kumene angafunikire m’gululi. Sukulu imeneyi imathandiza kukhala ndi luso lotsogolera m’ntchito yolalikira, kuŵeta gulu, ndi kuphunzitsa mu mpingo. Akamaliza maphunziro awo, ena amakakhala apainiya apadera kapena oyang’anira oyendayenda kudziko la kwawo kapena kumayiko ena. Ena amakatumikira limodzi ndi mpingo wakwawo kapena kumadera ena kumene kuli kusoŵa kwakukulu m’dziko lawo lomwelo.
4 M’milungu isanu ndi itatu, ophunzira ameneŵa amaphunzira Baibulo mozama kwambiri. Amaphunzira bwinobwino ziphunzitso zambiri za m’Baibulo limodzinso ndi udindo woŵeta gulu, ndi malangizo a mmene angachitire ndi mavuto okhudza moyo wachikristu. Amaphunziranso zimene Malemba amaphunzitsa pa za ntchito ya oyang’anira, chiweruzo, ndi nkhani zina zokhudza gulu. Amalandiranso maphunziro apadera a mmene angalankhulire pamaso pa anthu ndipo amapatsidwanso thandizo lapadera aliyense payekha kuti akule mofulumira mwauzimu.
5 Ziyeneretso Zake: Mwachionekere, ziyeneretso zakuti munthu ukachite nawo sukulu imeneyi n’zapamwamba kwambiri. Amene akufunsira kukaloŵa nawo sukuluyi ayenera kukhala mkulu kapena mtumiki wotumikira amene watumikira kwa zaka zosachepera ziŵiri mosalekeza. Ayenera kukhala wosakwatira ndi wa zaka za pakati pa 23 mpaka 50. Iwo ayenera kudziŵa kuŵerenga, kulemba, ndi kulankhula bwino chinenero chimene sukuluyi imachitikira, ndipo ayenera kukhala ndi thanzi labwino, losafunikira chisamaliro chapadera kapena zakudya zapadera. Mwayi woyambirira umapita kwa awo amene akuchita utumiki wa upainiya wokhazikika.
6 Onse amene adzipereka ayenera kukhala oti akufunitsitsa ndipo akhoza kukatumikira kulikonse kumene angafunikire. Zimenezi zikutanthauza kuti ayenera kukhala ndi mzimu ngati wa mneneri Yesaya amene anadzipereka yekha ndi mtima wonse kuchita ntchito yapadera pamene anati: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yes. 6:8) Iye anasonyezanso kudzichepetsa pa moyo wake wonse. Onse amene akufunsira kuloŵa nawo Sukulu Yophunzitsa Utumiki ayenera kutero chifukwa chakuti amakonda abale awo ndipo ali ndi mtima wofuna kuwatumikira abalewo, osati chifukwa chofuna kutchuka kapena malo apamwamba. Akamaliza kulandira maphunziro apamwamba ameneŵa, ophunzira amayembekezereka kuchita zimene aziphunzira kuti athandize ena.—Luka 12:48.
7 Phindu Lake: Pa milungu isanu ndi itatu ya maphunziro ozama ameneŵa, ophunzirawo ‘amaleredwa m’mawu a chikhulupiriro ndi malangizo abwino.’ (1 Tim. 4:6) Chifukwa cha zimenezi amakhala okonzeka kuthandiza ndi kulimbikitsa ena m’mipingo ndi madera amene agaŵiridwa. Kumadera ambiri kumene omaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki atumizidwa, ntchito yolalikira yapita patsogolo; ambiri ayamba utumiki wa upainiya, makamaka achinyamata; ndipo atsopano ambiri amene akusonkhana ndi anthu a Mulungu alandira chisamaliro chapadera aliyense payekha.
8 Kodi ndinu mkulu kapena mtumiki wotumikira wosakwatira amene muli ndi zaka za pakati pa 23 mpaka 50? Bwanji osafunsira kuloŵa nawo Sukulu Yophunzitsa Utumiki? Kodi ndinu wachinyamata amene mukukonza zolinga zanu za m’tsogolo zotumikira Yehova? Bwanji osakhala ndi moyo wosafuna zambiri ndiponso wopanda zododometsa kuti mudzathe kuloŵa pa khomo lalikulu loloŵera m’ntchito yochuluka limeneli? Mungathe kupeza chimwemwe chochuluka. Ndithudi, Sukulu Yophunzitsa Utumiki imeneyi yakhala dalitso osati kwa omaliza maphunziro okhawo komanso ku mipingo ya anthu a Mulungu padziko lonse.
[Bokosi patsamba 3]
Phindu Limene Anapeza pa Maphunziro Ameneŵa
“Ndithudi maphunziro ameneŵa andithandiza kwambiri kukhala ndi luso mu utumiki wanga ndi luso loŵeta gulu mwanzeru mwa kugwiritsa ntchito Malemba.”
“Sukulu imeneyi yandithandiza kuti ndizitha kusamalira bwinobwino maudindo osiyanasiyana mu mpingo popanda kudzikayikira.”
“Yasintha pafupifupi moyo wanga wonse, kuphatikizapo mmene ndimaonera ulamuliro wa Mulungu ndi gulu lake.”
“Maphunziro amene ndinalandira andithandiza kuzindikira kuti ndifunika kudzipereka kukatumikira kumene kuli kusoŵa.”