Mmene Tingalalikire Achibale
1. N’chifukwa chiyani kuzindikira kuli kofunika polalikira achibale?
1 Tingakhaledi osangalala kwambiri kulowa m’dziko lapansi latsopano limodzi ndi achibale anthu n’kugwirizana nawo limodzi kulambira Yehova. Achibale athuwa angakhale ndi chiyembekezo chimenechi titawalalikira. Koma kuti tichite zimenezi m’njira yotsitsimula, m’pofunika kukhala ozindikira. Woyang’anira dera wina anati: “Amene amachita bwino kwambiri pa ntchito imeneyi ndi aja amene amakopa chidwi cha achibale awo mwa kuwalalikira pang’ono ndi pang’ono.” Kodi tingachite bwanji zimenezi?
2. Kodi kukhala ndi chidwi ndi achibale athu kungatithandize bwanji kukopa chidwi chawo?
2 Kopani Chidwi Chawo: Ganizirani kaye mofatsa zimene mungachite kuti mukope chidwi cha achibale anu. (Miy. 15:28) Kodi ali ndi nkhawa zotani? Kodi akukumana ndi mavuto otani? N’kutheka kuti mwina mungawasonyeze nkhani kapena kutchula lemba lokhudza nkhani imene ali nayo chidwi. Ngati achibale anu amakhala kutali, mukhoza kuchita zimenezi powalembera kalata kapena kuwaimbira telefoni. Popanda kuwatopetsa ndi zambirimbiri, bzalani mbewu za choonadi, n’kuyang’ana kwa Yehova kuti akulitse mbewu zimenezo.—1 Akor. 3:6.
3. Kodi chidwi chimene achibale amakhala nacho ndi ife chingatsegule bwanji njira yoti tiwalalikire?
3 Yesu anauza munthu amene anam’chotsa ziwanda kuti: “Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.” (Marko 5:19) Taganizani mmene zimenezi zinasangalatsira achibale ake a munthuyu! Ngakhale kuti zofanana ndi zimenezi sizinayambe zakuchitikirani, n’zachidziwikire kuti achibale anu amachita chidwi ndi zimene mumachita kapena zimene amachita ana anu. Kutchula za nkhani imene munakamba mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, msonkhano wachigawo umene munapitako, ulendo wa ku Beteli, kapena za chinthu chosangalatsa ndi chosaiwalika chimene chinakuchitikirani zingathe kutsegula njira yoyamba kukambirana nawo za Yehova ndi gulu lake.
4. Kodi ndi mbuna ziti zomwe tiyenera kupewa tikamalalikira achibale?
4 Khalani Ozindikira: Mukamalalikira achibale, pewani kuwauza zinthu zambiri nthawi imodzi. Mbale wina pokumbukira nthawi imene anayamba kuphunzira Baibulo anati: “Ndinali kuvutitsa mayi anga kwa maola angapo n’kuwafotokozera pafupifupi zonse zimene ndinali nditaphunzira m’Baibulo, ndipo zimenezi kawirikawiri zimayambitsa mkangano, makamaka ndi bambo anga.” Ngakhale zitakhala kuti wachibale ali n’chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo, muyankheni m’njira yoti munthuyo akhalebe ndi chikhumbo chofuna kudziwa zambiri. (Miy. 25:7) Nthawi zonse muzikhala waulemu, wokoma mtima, ndi woleza mtima, monga mmene mukanachitira mukanakhala kuti mukulankhula ndi anthu achilendo mu utumiki wakumunda.—Akol. 4:6.
5. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati achibale akukana tikamawalalikira?
5 Nthawi inayake, achibale ake a Yesu anaganiza kuti Yesu wachita misala. (Marko 3:21) Komabe pambuyo pake, ena a iwo anadzakhala okhulupirira. (Mac. 1:14) Ngati pakali pano mukuyesetsa kuuza achibale choonadi koma akukana, musaleke. Zinthu pamoyo wawo komanso maganizo awo zikhoza kusintha. Choncho, yesetsani kupeza mpata wina woti muwauze mfundo inayake imene ikhoza kuwachititsa chidwi. Mukhoza kudzakhala ndi chimwemwe choti munawathandiza kuti ayambe kuyenda panjira ya kumoyo wosatha.—Mat. 7:13, 14.