Ndandanda ya Banja ya Misonkhano ya Mpingo
1 Ngati ndinu kholo lachikristu, mumafuna kuti ana anu akule akukonda Yehova ndi kum’tumikira kuti adzapeze moyo wosatha m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Kodi mungawathandize bwanji kuti kupembedza Yehova kukhale patsogolo m’moyo wawo? Njira yabwino kwambiri ndiyo chitsanzo chanu. (Miy. 20:7) Pokumbukira chitsanzo cha mayi ake amene ndi Mboni, mlongo wina anati: “Sizinali zochita kufunsa ngati titi tipite ku misonkhano kapena ayi.” Kwa mlongoyu chimenechi n’chitsanzo chosaiwalika.
2 Kodi banja lanu, limadziwadi bwino cholinga cha misonkhano ya mpingo? Malangizo amene timalandira pa misonkhano imeneyi amatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo mayanjano abwino amene timakhala nawo ndi abale athu amatilimbikitsa kwambiri. (Yes. 54:13; Aroma 1:11, 12) Komabe, cholinga chachikulu cha misonkhano imeneyi n’choti tipereke ulemerero kwa Yehova “m’masonkhano.” (Sal. 26:12) Misonkhano yachikristu imatipatsa mwayi wosonyeza chikondi chathu kwa Yehova ndi kum’lambira.
3 “Penyani Bwino Umo Muyendera”: Ngati timazindikira kuti misonkhano yathu ili ndi cholinga chopatulika, ‘tidzapenya bwino umo tiyendera’ kuti tipewe chizolowezi chophonya misonkhano chimene chimayamba pang’onopang’ono chifukwa cha zinthu zina zosafunika kwenikweni. (Aef. 5:15, 16; Aheb. 10:24, 25) Pokonza ndandanda ya banja lanu, mungayambe ndi kuika nthawi ya misonkhano ya mpingo. Mukatero, khalani osamala kuti musalole zochita zina kusokoneza nthawi imeneyi. Onetsetsani kuti kupezeka pa misonkhano kuli patsogolo pabanja lanu.
4 Kodi sizitikhudza mtima tikawerenga za abale athu amene amayesetsa kuthana ndi zovuta n’cholinga choti akapezeke ku misonkhano ya mpingo ndi misonkhano ikuluikulu? Ngakhale kuti moyo wanu sungakhale ndi mavuto ngati awo, n’zachidziwikire kuti nanunso mumakuma ndi mavuto. Satana akuchita zonse zimene angathe kuti anthu a Mulungu azivutika kwambiri popembedza Yehova. Koma dziwani kuti ana anu amaona mmene banja lanu limayesetsera kukapezeka pa misonkhano ya mpingo. Inde, mwa kuchita zimenezi, mungapatse ana anu mphatso yauzimu imene sadzaiiwala m’pang’ono pomwe.