Kulalikira Kumatithandiza Kupirira
1 Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Aheb. 12:1) Wothamanga amafunika kupirira kuti apambane, ifenso tifunika kupirira kuti tikalandire mphoto ya moyo wosatha. (Aheb. 10:36) Kodi utumiki wachikristu ungatithandize bwanji kuti tipirire mokhulupirika mpaka kumapeto?—Mat. 24:13.
2 Kulimbikitsidwa Mwauzimu: Tikamalalikira za malonjezo osangalatsa a m’Baibulo onena za dziko latsopano la chilungamo, zimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo cholimba. (1 Ates. 5:8) Tikamapita nawo mu utumiki wa kumunda nthawi zonse, timakhala ndi mwayi wodziwitsa ena choonadi chimene taphunzira m’Baibulo. Timakhala ndi mwayi woikira kumbuyo chikhulupiriro chathu, zimene pambuyo pake zimatilimbikitsa mwauzimu.
3 Kuti tithe kuphunzitsa ena mogwira mtima, m’pofunika kuti ifeyo tizichimvetsa bwino choonadi cha m’Baibulo. Tifunika kufufuza ndi kusinkhasinkha pa nkhaniyo. Kuchita zimenezi mwakhama kumazamitsa zimene tikudziwa, kumalimbitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso kumatipatsa mphamvu mwauzimu. (Miy. 2:3-5) Motero, pamene tikuyesetsa kuthandiza ena, timakhalanso tikudzilimbitsa ife eni.—1 Tim. 4:15, 16.
4 Kuchita nawo utumiki mwachangu ndi njira yofunika kwambiri ‘yovalira zida zonse za Mulungu,’ zimene timafunikira kuti tithe kuchirimika polimbana ndi Mdyerekezi ndi ziwanda. (Aef. 6:10-13, 15) Tikamatangwanika mu utumiki wopatulika, zimatithandiza kuti tiziganizira zinthu zabwino zokhazokha ndipo timapewa kusokonezedwa ndi dziko la Satanali. (Akol. 3:2) Tikamaphunzitsa ena njira za Yehova, timakumbutsidwa za kufunika kokhala ndi khalidwe loyera.—1 Pet. 2:12.
5 Mulungu Amatipatsa Mphamvu: Pomaliza, kutenga nawo mbali mu ntchito yolalikira kumatiphunzitsa kudalira Yehova. (2 Akor. 4:1, 7) Limeneli ndi dalitso lalikulu zedi. Chifukwa cha chidaliro choterocho, timakhala okonzeka kukwanitsa utumiki wathu komanso kuthana ndi mavuto alionse amene tingakumane nawo m’moyo wathu. (Afil. 4:11-13) Zoonadi, m’pofunika kuphunzira kudalira Yehova ndi mtima wonse kuti tipirire. (Sal. 55:22) Kulalikira kumatithandiza kupirira m’njira zambiri.