Ngongole Imene Tili Nayo kwa Ena
1 Mtumwi Paulo ankaona kuti ndi udindo wake kulalikira kwa anthu. Ankadziwa kuti Yehova kudzera m’mwazi wamtengo wapatali wa Mwana Wake watheketsa kuti anthu onse apulumuke. (1 Tim. 2:3-6) Chotero, Paulo ananena kuti: “Ine ndili wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.” Choncho iye anagwira ntchito mwachangu ndiponso mwakhama kuti abweze ngongole imeneyo kwa anthu mwa kuwauza uthenga wabwino.—Aroma 1:14, 15.
2 Mofanana ndi Paulo, Akristu masiku ano amayesetsa kuuza anansi awo uthenga wabwino pa mpata uliwonse. Popeza kuti ‘chisautso chachikulu’ chikuyandikira mofulumira kwambiri, ntchito yathu yofunafuna anthu oona mtima ikufunika kuchitidwa mwachangu. Ndiyetu kukonda kwathu anthu kochokera pansi pa mtima kutithandize kukhala akhama pa ntchito yopulumutsa moyo imeneyi.—Mat. 24:21; Ezek. 33:8.
3 Kubweza Ngongole Yathu: Njira yaikulu imene timafikira nayo anthu ambiri ndiyo kulalikira khomo ndi khomo. M’magawo amene anthu ambiri sakonda kupezeka panyumba, tingachite bwino kulemba molondola kuti panyumba zakutizakuti sitinapezepo anthu, ndiyeno n’kusunga zimenezo kuti tidzabwerenso tsiku lina panthawi yosiyana ndi imene tinapitirayo. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti tifikire anthu ambiri. (1 Akor. 10:33) Tikhozanso kufikira anthu mwa kulalikira m’gawo la malonda, kulalikira mu msewu, m’mapaki, m’malo oimika magalimoto, ndi patelefoni. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndikuyesetsa kugwiritsa ntchito njira zonse za ulaliki n’cholinga chakuti ndiuze ena uthenga wabwino wopatsa moyo?’—Mat. 10:11.
4 Mlongo wina yemwe ndi mpainiya anali wofunitsitsa kufikira aliyense m’gawo lake. Koma panali nyumba ina imene nthawi zonse akapitapo amapeza kuti makatani ali otseka, komanso samapezapo munthu aliyense. Koma tsiku lina pamene iye sanali mu utumiki, anaona kuti panyumbapo pali galimoto. Posafuna kuphonya mwayi umenewu, iye anakagogoda pakhomopo. Mwamuna wa panyumbapo atatuluka, anayamba kukambirana naye ndipo kukambirana koyambaku kunapereka mwayi woti mlongoyo limodzi ndi mwamuna wake achite maulendo ambiri obwereza. M’kupita kwa nthawi, mwamunayo anavomera kuphunzira Baibulo, ndipo panopa ndi mbale wobatizidwa. Amathokoza mlongoyo chifukwa chodziona kuti anali ndi ngongole yolalikira kwa ena.
5 Popeza nthawi ikufulumira kwambiri kupita kumapeto, inoyi ndi nthawi yoti tibweze ngongole yathu kwa anthu mwa kudzipereka mwamphamvu mu ntchito yolalikira.—2 Akor. 6:1, 2.