Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/05 tsamba 3-6
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mabuku Ophunzitsira
  • Mmene Mungakonzekerere
  • Gwirizanitsani Nkhaniyo ndi Zosowa Zake
  • Phunzitsani Kuchokera M’Mawu a Mulungu
  • Kudula Mizere ndi Kulemba Notsi
  • Kupenda Nkhani Yonse Mwachidule ndi Kubwereramo
  • Mangani Chikhulupiriro Cholimba
  • Phunzirolo Liziyenda
  • Khalani Wozindikira
  • Khalani Wodzichepetsa
  • Mmene Tingayambire Kumapemphera pa Phunziro
  • Zimene Mungaphatikize M’pemphero
  • Misonkhano ya Mpingo
  • Gwiritsani Ntchito Mavidiyo Kuti Muwathandize Kuyamikira Gulu
  • Alimbikitseni Kulalikira
  • Aphunzitseni Mmene Angauzire Ena Zimene Amakhulupirira
  • Kukonzekera Limodzi
  • Kulalikira Limodzi
  • Kukonzekera Ulendo Wobwereza
  • Chitani Khama Kubwerera kwa Anthu Achidwi
  • Kupempha Ena Kuti Tiziphunzira Nawo Baibulo
  • Kuphunzitsa Ophunzira Kukhala Aphunzitsi
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Konzekerani Bwino Pokaphunzitsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 9/05 tsamba 3-6

Sungani

Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo

Mu mphatika ino muli mfundo zonse zikuluzikulu zochokera m’magawo onse a nkhani za kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo zimene zakhala zikutuluka mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Tikulimbikitsa nonse kuisunga ndi kumaiwerenga mukamachititsa maphunziro a Baibulo. Kuwonjezeranso pamenepa, mfundo zimene zili mu mphatika imeneyi mukhoza kumazigwiritsa ntchito pa msonkhano wokonzekera utumiki wa kumunda, ndiponso oyang’anira utumiki akhoza kumaigwiritsa ntchito kukonzera nkhani zimene amakamba akamayendera magulu a phunziro la buku.

Gawo 1: Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?

Ngati mumakambirana za Baibulo nthawi zonse mwadongosolo, ngakhale mwachidule, pogwiritsa ntchito Baibulo kapenanso limodzi ndi buku limene amati tiyenera kuliphunzira ndi anthu, ndiye kuti mukuchititsa phunziro la Baibulo. Muyenera kuchitira lipoti phunzirolo ngati mwaphunzira maulendo awiri kuchokera pamene munam’sonyeza kachitidwe kake ndiponso ngati zikuonetsa kuti phunzirolo lidzapitirira.—km-CN 7/04 tsa. 1.

Mabuku Ophunzitsira

◼ Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?

◼ Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha

◼ Lambirani Mulungu Woona Yekha

◼ Bulosha la Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! mungathe kuligwiritsa ntchito kuphunzira ndi anthu amene sanapite kusukulu mokwanira bwino kapena amene ali ndi vuto lowerenga.

Gawo 2: Kukonzekera Kuchititsa Phunziro

Pophunzitsa tiyenera kum’fika pamtima wophunzira wathu. Zimenezi zimafuna kuti tizikonzekera mokwanira bwino ndiponso tiziganiza za wophunzira wathuyo pamene tikukonzekera.—km-CN 8/04 tsa. 1.

Mmene Mungakonzekerere

◼ Lingalirani za mutu wa nkhaniyo, timitu ta m’kati, ndiponso zithunzi zake.

◼ Pezani mayankho a mafunso amene aperekedwa m’nkhaniyo, ndi kudula mzere kunsi kwa mawu okhawo amene ali ofunika kwambiri.

◼ Sankhani malemba oti mukawerenge paphunzirolo. Lembani timawu tochepa m’mphepete mwa tsamba la buku lanu lophunzitsiralo.

◼ Konzani zoti mukabwerere mu mfundo zikuluzikulu mwachidule.

Gwirizanitsani Nkhaniyo ndi Zosowa Zake

◼ Pemphererani wophunzirayo ndi zosowa zake.

◼ Yesani kuona mfundo zimene wophunzirayo zingam’vute kuzimvetsa kapena kuzivomereza.

◼ Ganizirani kuti: Kodi n’chiyani chimene afunika kumvetsetsa kapena kuwongolera kuti apite patsogolo mwauzimu? Kodi ndingam’fike bwanji pamtima?

◼ Ngati kuli kofunika, konzani fanizo, kapena konzani zokamveketsa bwino mfundo inayake kapenanso kukonza zokafunsa mafunso angapo kuti mukam’thandize wophunzirayo kumvetsa bwino mfundo inayake kapena lemba.

Gawo 3: Kugwiritsa Ntchito Malemba Mogwira Mtima

Cholinga chathu pochititsa maphunziro a Baibulo ndicho ‘kupanga ophunzira’ mwa kuthandiza anthu kumvetsa ndi kuvomereza ziphunzitso za Mawu a Mulungu ndi kuzigwiritsa ntchito pa moyo wawo. (Mat. 28:19, 20; 1 Ates. 2:13) Pachifukwa chimenechi, phunziro liyenera kuzikika kwambiri pa Malemba.—km-CN 11/04 tsa. 4.

Phunzitsani Kuchokera M’Mawu a Mulungu

◼ Muonetseni wophunzirayo mmene angapezere malemba amene akufuna m’Baibulo lake.

◼ Werengani ndi kukambirana malemba a m’Baibulo amene akusonyeza kuti zikhulupiriro zathu n’zozikidwa pa Baibulo.

◼ Gwiritsani ntchito mafunso. M’malo moti inuyo muzim’tanthauzira wophunzirayo malemba a m’Baibulo, muloleni iyeyo kuti azitanthauzira.

◼ Musachulutse zonena. Musayese kufotokozera mbali iliyonse ya lemba. Ingofotokozani mbali yokhayo imene ikufunika kuti mumveketse bwino mfundo imene mukufunayo.

◼ M’thandizeni kuona kuti malemba a m’Baibulowo akumukhudza ndiponso mmene akum’khudzira.

Gawo 4: Kuphunzitsa Ophunzira Kuti Adziwe Kukonzekera

Wophunzira amene amawerengeratu zimene adzaphunzire, kuduliratu mizere kunsi kwa mayankho, ndi kulingalira mmene angadzawafotokozere m’mawu akeake, sachedwa kupita patsogolo mwauzimu. Ndiye mukangoti mwakhazikitsa phunziro, mufunika kukonzekera phunziro muli limodzi ndi wophunzirayo kuti mumusonyeze mmene angakonzekerere. Ophunzira ambiri, zimawathandiza kukonzekera nawo limodzi mutu wonse wathunthu.—km-CN 12/04 tsa. 1.

Kudula Mizere ndi Kulemba Notsi

◼ Fotokozani mmene angapezere mayankho a mafunso amene aperekedwa pa nkhaniyo.

◼ Muonetseni wophunzirayo buku lanu lophunzirira limene munadula mizere kunsi kwa mawu okhawo amene ali ofunika.

◼ Thandizani wophunzirayo kuona kuti lemba lililonse losagwidwa mawu limachirikiza mfundo inayake m’ndimemo, ndiponso muonetseni mmene angalembere notsi zachidule m’mphepete mwa buku lake lophunzirira.

Kupenda Nkhani Yonse Mwachidule ndi Kubwereramo

◼ Muonetseni wophunzirayo mmene angapendere mutu wa nkhani, timitu tam’kati, ndi zithunzi asanayambe kukonzekera mwa ndondomeko yake.

◼ Mulimbikitseni wophunzirayo kubwereramo mu mfundo zikuluzikulu akamaliza kukonzekera phunzirolo.

Gawo 5: Kuona Kuchuluka kwa Zimene Mungaphunzire

Kuchuluka kwa zimene mungaphunzitse kudzadalira luso ndi zochita za pamoyo wa nonse awirinu, wophunzirayo ndi wophunzitsanu.—km-CN 1/05 tsa. 1.

Mangani Chikhulupiriro Cholimba

◼ Musalepheretse wophunzirayo kumvetsetsa bwino Mawu a Mulungu mwa kum’phunzitsa zinthu zambirimbiri paulendo umodzi.

◼ Khalani ndi nthawi yokwanira yothandizira wophunzirayo kumvetsetsa ndi kuvomereza zimene akuphunzira.

◼ Khalani ndi nthawi yokwanira yokambirana malemba ofunika amene akuoneka kuti ndi maziko a chiphunzitsocho.

Phunzirolo Liziyenda

◼ Ngati wophunzirayo akukonda kukamba kwambiri zinthu zaumwini, tingakonze zokambirana zimenezo tikamaliza phunzirolo.

◼ Pewani kulankhula zambiri paphunzirolo. Chepetsani kutchula mfundo zina zapambali ndiponso zokumana nazo kuti musalepheretse wophunzirayo kudziwa molondola ziphunzitso zoyambirira za Baibulo.

Gawo 6: Wophunzira Akafunsa Funso

Tikangoti takhazikitsa phunziro la Baibulo, nthawi zonse ndi bwino kuphunzira ziphunzitso za m’Baibulo m’ndondomeko yake osati kumadumpha mitu. Zimenezi zimathandiza wophunzira kumanga maziko odalirika odziwa Mawu a Mulungu molondola ndi kupita patsogolo mwauzimu.—km-CN 3/05 tsa. 7.

Khalani Wozindikira

◼ Mafunso ogwirizana ndi nkhani imene tikuphunzira panthawiyo tingawayankhiretu nthawi yomweyo.

◼ Mafunso amene sakugwirizana ndi zimene tikuphunzira panthawiyo kapena ngati ali ofunika kukafufuza, tingachite bwino kudzawayankha panthawi ina. Kungakhalenso kothandiza kuwalemba mafunsowo.

◼ Ngati wophunzira zikum’vuta kuvomereza chiphunzitso chinachake, yesani kukambirana naye nkhaniyo kuchokera m’buku lina limene limafotokoza momveka bwino za nkhaniyo.

◼ Ngati wophunzirayo sakumvetsetsabe, isiyeni nkhaniyo kuti mudzaione nthawi ina ndiyeno pitirizani phunzirolo.

Khalani Wodzichepetsa

◼ Ngati simukudziwa yankho la funso limene wophunzira wakufunsani, musayankhe malingaliro anuanu.

◼ Muzim’phunzitsa pang’onopang’ono wophunzirayo mmene timafufuzira nkhani.

Gawo 7: Kupereka Pemphero pa Phunziro

Kuti ophunzira Baibulo apite patsogolo mwauzimu, m’pofunika dalitso la Yehova. Choncho, ndi bwino kuyamba ndi kumaliza phunziro ndi pemphero.—km-CN 4/05 tsa. 8.

Mmene Tingayambire Kumapemphera pa Phunziro

◼ Kwa anthu amene ndi okonda zopembedza, tikhoza kumayamba kupemphera pa phunziro loyamba lenilenilo.

◼ Kwa ena, tifunika kuona nthawi yabwino imene tingayenere kuyamba kumapemphera pa phunziro.

◼ Malemba ngati Salmo 25:4, 5 ndi 1 Yohane 5:14 angathe kugwiritsidwa ntchito kufotokoza chifukwa chake timapemphera pa phunziro.

◼ Lemba la Yohane 15:16 mungaligwiritse ntchito kufotokozera kuti tiyenera kupemphera kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu.

Zimene Mungaphatikize M’pemphero

◼ N’koyenera kupereka ulemerero kwa Yehova monga Gwero la malangizo.

◼ Tchulani mawu osonyeza kuti mukukondwera naye wophunzirayo.

◼ Tchulani mawu oyamikira gulu limene Yehova akugwiritsa ntchito.

◼ Pemphani Yehova kuti adalitse khama la wophunzirayo pamene akuyesetsa kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira.

Gawo 8: Kutsogolera Ophunzira ku Gulu

Tikamachititsa maphunziro a Baibulo, cholinga chathu sikungophunzitsa nkhani zokhudza ziphunzitso zokha, koma timafunanso kuthandiza ophunzira kulowa mpingo wachikristu. Muzipatula mphindi zingapo mlungu uliwonse paphunziro lanu kukambirana nawo mfundo imodzi yokhudza gulu la Yehova.—km-CN 5/05 tsa. 1.

Misonkhano ya Mpingo

◼ Fotokozani za msonkhano uliwonse wa mpingo paokhapaokha. Pa phunziro loyambiriralo, apempheni kuti abwere ku misonkhano.

◼ Auzeni mfundo zabwinozabwino zimene zinakambidwa pa misonkhano.

◼ Athandizeni kuchita chidwi kwambiri ndi Chikumbutso, misonkhano ikuluikulu, ndiponso kuchezetsa kwa woyang’anira dera.

◼ Gwiritsani ntchito zithunzi za m’mabuku athu kuti muwathandize kuona m’maganizo mwawo zimene zimachitika pa misonkhano.

◼ Alimbikitseni kuti awerenge bulosha lakuti: Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?

Gwiritsani Ntchito Mavidiyo Kuti Muwathandize Kuyamikira Gulu

◼ Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name

◼ Our Whole Association of Brothers

◼ United by Divine Teaching

◼ To the Ends of the Earth

Gawo 9: Kukonzekeretsa Ophunzira Kuti Adziwe Kulalikira Mwamwayi

Ophunzira Baibulo akayamba kukhulupirira zimene akuphunzira amafunitsitsa kuuza anthu ena zimene akuphunzirazo.—km-CN 6/05 tsa. 1.

Alimbikitseni Kulalikira

◼ Kodi ali ndi mabwenzi kapena achibale amene atha kuwaitana kuti adzakhale nawo limodzi pamene akuphunzira?

◼ Kodi pali anthu ena monga anzake a kuntchito, anzake a kusukulu, kapenanso anthu ena achinansi amene asonyeza chidwi ndi zimene akuphunzirazo?

Aphunzitseni Mmene Angauzire Ena Zimene Amakhulupirira

◼ Mukamakambirana mfundo zina m’kati mwa phunzirolo, m’funseni wophunzirayo kuti, “Kodi mungagwiritse ntchito bwanji Baibulo kuti mufotokoze mfundo yoona iyi kwa a m’banja mwanu?”

◼ M’thandizeni wophunzirayo kuzindikira chifukwa chake ayenera kukhala waulemu ndi wachifundo pamene akulankhula ndi ena za Mulungu ndi zolinga zake.

◼ Ophunzira angagwiritse ntchito bulosha lakuti Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? kuthandizira anzawo ndiponso a m’banja mwawo kumvetsa zikhulupiriro ndi ntchito zathu zozikidwa m’Baibulo.

Gawo 10: Kuphunzitsa Ophunzira Ulaliki wa Nyumba ndi Nyumba

Akulu akapenda wophunzira Baibulo n’kuona kuti akuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa, wophunzirayo angayambe kugwira nawo ntchito yolalikira limodzi ndi mpingo.—km-CN 7/05 tsa. 1.

Kukonzekera Limodzi

◼ M’sonyezeni wofalitsa watsopanoyo pamene angapeze zitsanzo za maulaliki.

◼ M’thandizeni kusankha chitsanzo cha ulaliki wosavuta wogwirizana ndi gawo lanu.

◼ Mulimbikitseni kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wake.

◼ Yesererani limodzi ulaliki. M’sonyezeni mmene angayankhire mwanzeru mogwirizana ndi mmene anthu amakonda kuyankhira mukamawalalikira.

Kulalikira Limodzi

◼ Muuzeni wophunzirayo kuti aonere kaye mmene mugwiritsire ntchito chitsanzo cha ulaliki umene munakonzekera muli limodzi uja.

◼ Zindikirani umunthu wa wophunzirayo ndiponso luso lake. Nthawi zina, zimakhala bwino kumulola kuchita mbali yochepa ya ulalikiwo.

◼ Thandizani wofalitsa watsopanoyo kukhala ndi ndandanda yokhazikika yopitira mu utumiki wa kumunda.

Gawo 11: Kuthandiza Ophunzira Kupanga Maulendo Obwereza

Kukonzekera ulendo wobwereza kumayambira paulendo woyamba. Muyenera kulimbikitsa wophunzirayo kukhala ndi chidwi kwambiri ndi anthu amene walankhula nawo. M’phunzitseni pang’onopang’ono zimene angachite kuti anthu amene akulankhula nawo azifotokoza maganizo awo, mmene angamvetserere ndemanga zawo, ndiponso mmene angadziwire zinthu zimene zikuwadetsa nkhawa.—km-CN 8/05 tsa. 1.

Kukonzekera Ulendo Wobwereza

◼ Onani zimene munakambirana paulendo woyamba, ndipo m’thandizeni wophunzirayo kusankha mfundo ya uthenga wabwino imene ingakasangalatse mwininyumba.

◼ Konzekerani ulaliki wachidule wokhala ndi lemba limodzi la m’Baibulo ndiponso ndime imodzi kuchokera m’buku logwiritsa ntchito kuchitira phunziro.

◼ Konzani funso limene mukhoza kukafunsa mutamaliza kukambirana.

Chitani Khama Kubwerera kwa Anthu Achidwi

◼ M’limbikitseni wophunzirayo kumabwereranso mofulumira kwa onse amene anachita chidwi.

◼ M’thandizeni wophunzirayo kuona kufunika kochita khama pofuna kufikira anthu amene kumakhala kovuta kuwapeza.

◼ M’sonyezeni wofalitsa watsopanoyo mmene angamapanganirane ndi anthu kuti akabwerenso, ndiponso m’thandizeni kuona kufunika kobwererako mogwirizana ndi mmene analonjezerana.

Gawo 12: Kuthandiza Ophunzira Kuyambitsa ndi Kuchititsa Maphunziro a Baibulo

Kutengera chitsanzo cha Yesu mwa kusonyeza chitsanzo chabwino mu utumiki wanu n’kofunika kwambiri. Wophunzira wanu akamaona chitsanzo chanu cha mu utumiki, adzatha kumvetsetsa kuti cholinga chopangira maulendo obwereza ndicho kuyambitsa maphunziro a Baibulo.—km-CN 9/05 tsa. 7.

Kupempha Ena Kuti Tiziphunzira Nawo Baibulo

◼ M’fotokozereni wophunzirayo kuti si zofunika kuchita kufotokoza mwatsatanetsatane ndondomeko yonse ya mmene timachitira phunziro.

◼ Nthawi zambiri zimakhala bwino kungom’sonyeza mwininyumba mmene timaphunzirira pogwiritsa ntchito ndime imodzi kapena ziwiri kuchokera m’buku limene timaphunzitsira.

◼ Pendani chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo ndi kuyeserera mmene mungachitire.—km-CN 9/05 tsa. 7; km-CN 1/02 tsa. 6.

Kuphunzitsa Ophunzira Kukhala Aphunzitsi

◼ Limbikitsani ophunzira kulembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

◼ Konzani zoti ofalitsa atsopano azipita nanu limodzi kokachititsa maphunziro a Baibulo kumene akhoza kumakatenga nawo mbali pang’ono m’kuphunzitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena