Khalani ndi Luso Lothandiza Ena Kuona Mfundo Yofunika
1. Kodi ndi nkhani iti ya m’Baibulo imene tikambirane, ndipo n’chifukwa chiyani?
1 Nkhani yomwe mtumwi Paulo anakamba ku sunagoge ku Antiokeya wa ku Pisidiya, yopezeka pa Machitidwe 13:16-41, imapereka chitsanzo chabwino chosonyeza mmene tingathandizire ena kuona mfundo yofunika. Paulo anaganizira kwambiri mbiri ya anthuwo ndi kaganizidwe kawo kenako n’kusintha ulaliki wake wa uthenga wabwino kuti ugwirizane ndi anthu amenewo. Pokambirana nkhani imeneyi, tiyeni tiganizire mmene ifenso tingachitire zimenezi mu utumiki.
2. Tikaona mmene Paulo anayambira nkhani yake, kodi tikuphunzirapo chiyani?
2 Pezani Mfundo Imene Mungagwirizanepo: Ngakhale kuti uthenga wa Paulo unagona pa mfundo yonena za udindo wofunika kwambiri umene Yesu ali nawo pokwaniritsa zolinga za Mulungu, Paulo sanayambe kukamba nkhani yake mwa kutchula zimenezi. M’malo mwake, analankhula za zinthu zimene Ayudanso anali kuzidziwa. Anayamba ndi kusimba mbiri ya Ayudawo. (Mac. 13:16-22) Mofanana ndi zimenezi, nafenso tingalankhule mogwira mtima ngati tinena mfundo imene ifeyo ndi omvera athu tingagwirizanepo. Kuti tichite zimenezi, tifunikira kulimbikitsa omvera athu kuti anene maganizo awo pankhani imene tikukambirana nawo powafunsa mafunso mochenjera ndi kumvetsera mosamala pamene akulankhula kuti tidziwe zinthu zimene akuganiza.
3. Kodi n’chifukwa chiyani kunali kovuta kuti omvera a Paulo avomereze kuti Yesu ndiye anali Mesiya wolonjezedwa?
3 Posimba za mbiri ya Ayuda, Paulo anakumbutsa omvera ake za lonjezo la Mulungu lonena za Mpulumutsi amene adzabadwa kudzera mwa fuko la Davide. Komabe, Ayuda ambiri anali kuyembekezera ngwazi ya nkhondo imene inayenera kuwachotsa m’goli la ulamuliro wa Aroma n’kutukula mtundu wawo kuposa mitundu yonse ya anthu. Mwachidziwikire, anthuwo anali kudziwa kuti atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda ku Yerusalemu anam’kana Yesu, anam’pereka kwa olamulira achiroma, ndipo anamupha. Kodi Paulo akanawauza chiyani kuwakhutiritsa kuti Yesu ameneyu ndiye anali Mesiya wolonjezedwa?
4. Kodi ndi luso lotani limene Paulo anagwiritsa ntchito pokambirana ndi Ayuda?
4 Sinthani Kalalikidwe Kanu: Podziwa za kaganizidwe ka omvera ake, Paulo anagwiritsa ntchito Malemba pokambirana nawo za zinthu zimene iwo anali atazivomereza kale. Mwachitsanzo, pofotokoza za Yesu anati ndi mbadwa ya Davide ndi kutinso Yohane Mbatizi, amene anthu ambiri ankamuona monga mneneri wa Mulungu, anam’dziwikitsa iye. (Mac. 13:23-25) Paulo ananena kuti mwa kukana ndi kupha Yesu, atsogoleri achipembedzo ‘anakwaniritsa mawu a aneneri.’ (Mac. 13:26-28) Kenako, anafotokoza kuti panali mboni zimene zinaona ndi maso awo kuti Yesu wauka, ndipo anawapatsa Malemba odziwika bwino amene anakwaniritsidwa pa kuuka kwa Yesuyo.—Mac. 13:29-37.
5. (a) Kodi Paulo anasintha motani kalalikidwe kake polankhula ndi Agiriki? (b) Kodi tingatsatire motani chitsanzo cha Paulo pamene tikulalikira m’gawo lathu?
5 Panthawi ina, polankhula ndi Agiriki ku Areopagi ku Atene, Paulo anasintha kalalikidwe kake. (Mac. 17:22-31) Komabe, mfundo ya uthenga umene anafotokoza inali imodzimodzi, ndipo maulendo onse awiriwa anabala zipatso zabwino. (Mac. 13:42, 43; 17:34) Masiku ano, nafenso tingalalikire mogwira mtima tikamasankha mfundo zimene ife ndi omvera athu tikugwirizanapo ndiponso tikamasintha kalalikidwe kathu kuti kazigwirizana ndi anthuwo ndi kaganizidwe kawo.