Maphunziro Opatsa Moyo
1 Zimalimbikitsa kwambiri kuona anthu akusangalala atadziwa choonadi chochokera m’Mawu a Mulungu. Zoonadi, kuuza ena za Mulungu ndi cholinga chake kwa anthu kumakhutiritsa. Maphunziro amenewa angapatse munthu moyo wosatha.—Yoh. 17:3.
2 Chifukwa Chake Maphunzirowa Amaposa Ena Onse: Masiku ano, kuli sukulu zambiri zimene zimaphunzitsa pafupifupi chilichonse chimene inu mungaganize. (Mlal. 12:12) Komabe nzeru zimenezo phindu lake silingafanane ndi la “zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:11) Kodi maphunziro amene dziko limapereka athandiza anthu kuyandikira kwa Mlengi ndi kudziwa chifuno chake? Kodi athandiza anthu kudziwa kuti tikamwalira timapita kuti kapena chifukwa chake kunja kuno kuli mavuto ambiri? Kodi apatsa anthu chiyembekezo? Kodi amathandiza mabanja kukhala abwino? Ayi. Anthufe tingapeze mayankho enieni a mafunso ofunika pamoyo kudzera m’maphunziro ochokera kwa Mulungu.
3 Maphunziro a Mulungu ali ndi ubwino winawake umene supezeka kudziko masiku ano, monga kulimbikitsa makhalidwe abwino. Mawu a Mulungu amachotseratu mtima wosankhana mitundu ndi wokonda dziko lako mwa anthu amene amavomereza ndi kugwiritsa ntchito ziphunzitso zake. (Aheb. 4:12) Iwo athandiza anthu kusiya chiwawa cha mtundu wina uliwonse ndi ‘kuvala umunthu watsopano.’ (Akol. 3:9-11; Mika 4:1-3) Ndiponso, maphunziro a Mulungu alimbikitsa anthu mamiliyoni ambiri kusiya makhalidwe osakondweretsa Mulungu omwe anazika mizu m’mitima mwawo.—1 Akor. 6:9-11.
4 Chifukwa Chake Ali Ofunika Tsopano: Mlangizi wathu Wamkulu amatiuza za tanthauzo la zimene zikuchitika nthawi imene tikukhalayi. Ulosi wa chiweruzo chake umatiuza za zinthu za panthawi yake zimene tiyenera kulengeza padziko lonse lapansi. (Chiv. 14:6, 7) Kristu akulamulira kumwamba, ndipo ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga udzawonongedwa posachedwapa. Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kuwononga maufumu onse padziko lapansi. (Dan. 2:44; Chiv. 11:15; 17:16) Choncho, anthu afunika adziwe Mfumu imene ikulamulira imene Mulungu wakhazikitsa, afunika kutuluka mu Babulo Wamkulu, ndi kuitana pa dzina la Yehova n’chikhulupiriro. (Sal. 2:11, 12; Aroma 10:13; Chiv. 18:4) Tiyeni titenge nawo mbali mokwanira pophunzitsa ena maphunziro amene amapatsa moyo.