Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/06 tsamba 4
  • Phunzitsani Anthu Ofatsa Kuyenda M’njira ya Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunzitsani Anthu Ofatsa Kuyenda M’njira ya Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Muzithandiza Ena Kuti Azimvera Malamulo a Khristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Penyererani Chiphunzitso Chanu Nthaŵi Zonse
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Phunzitsani Mwachikondi Ngati Yesu
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 5/06 tsamba 4

Phunzitsani Anthu Ofatsa Kuyenda M’njira ya Mulungu

1. Kodi kupanga ophunzira kumaphatikizapo chiyani?

1 Ophunzira a Kristu oyambirira ankatchedwa kuti otsata “Njirayo.” (Mac. 9:2) Chikristu choona chimakhudza moyo wonse wa munthu. (Miy. 3:5, 6) Chotero, tikamachititsa maphunziro a Baibulo, sikokwanira kungophunzitsa anthu kudziwa ziphunzitso zolondola za m’Baibulo. Tifunikanso kuthandiza anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo kuyenda m’njira ya Yehova.—Sal. 25:8, 9.

2. Kodi n’chiyani chimene chingalimbikitse wophunzira Baibulo kumvera malamulo a Mulungu?

2 Aphunzitseni kukonda Yehova ndi Yesu: Anthu opanda ungwiro zimawavuta kwambiri kuti aziganiza, kulankhula ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Aroma 7:21-23; Aef. 4:22-24) Koma kukonda Mulungu ndi Mwana wake, kumalimbikitsa anthu ofatsa kuchita zimenezi. (Yoh. 14:15; 1 Yoh. 5:3) Kodi amene timaphunzira nawo Baibulo tingawathandize bwanji kukhala ndi chikondi chimenechi?

3. Kodi tingathandize bwanji amene tikuphunzira nawo kukonda Yehova ndi Yesu?

3 Thandizani amene mumaphunzira naye kum’dziwa bwino Yehova. Mbale wina anafotokoza kuti, “Anthu sangakonde munthu amene samudziwa. Chotero, pachiyambi penipeni paphunziro, ndimawaphunzitsa dzina la Mulungu kuchokera m’Baibulo. Ndipo ndimafuna mipata yogogomezera makhalidwe a Yehova.” Kufotokoza makhalidwe a Mulungu ndiponso chitsanzo cha Yesu ndi njira yabwino kwambiri yochitira zimenezi. (Yoh. 1:14; 14:9) Ndiponso, gwiritsani ntchito bokosi lobwereza limene lili kumapeto a mutu uliwonse wa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kuthandiza amene mukuphunzira naye kuganizira makhalidwe apadera a Mulungu ndiponso a Mwana wake.

4. (a) N’chifukwa chiyani ophunzira ambiri zimawavuta kulalikira? (b) Kodi tingathandize bwanji amene timaphunzira nawo kuti ayambe kuchita nawo utumiki wachikristu?

4 Phunzitsani mwa Kukhala Chitsanzo Chabwino: Kuti tiphunzitse ndi kutsogolera ena kuyenda m’njira ya Mulungu, tifunikira kuchita zimene timaphunzitsazo. (1 Akor. 11:1) Mwachitsanzo, ophunzira Baibulo ambiri sanazolowere kuuza anthu osawadziwa zimene amakhulupirira. Chotero, tifunika kukhala oleza mtima ndiponso aluso kuti tiwathandize kukhala ndi chikondi, chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima. Makhalidwe amenewa ndi ofunika polalikira ndi popanga ophunzira. (2 Akor. 4:13; 1 Ates. 2:2) Mtima wofuna kutsogolera ophunzira athu udzatilimbikitsa kuwathandiza ndi kuyenda nawo limodzi pamene ayamba utumiki wachikristu.

5. Kodi chitsanzo chabwino chimathandiza bwanji ophunzira kuona zimene ayenera kuchita pomvera malamulo a Mulungu?

5 Chitsanzo chanu chingaphunzitse amene mumaphunzira nawo mbali zina zofunika za moyo wachikristu. Mukamakaona odwala kapena kupatsa moni ena mwachikondi pa misonkhano ya mpingo, amaona chikondi chimene mumasonyeza. (Yoh. 15:12) Mukamachita nawo ntchito yoyeretsa Nyumba ya Ufumu kapena kuthandiza ena, ndiye kuti mukuwaphunzitsa kutumikira ena. (Yoh. 13:12-15) Akaona kuti mukukhala moyo wosalira zambiri, amamvetsa tanthauzo la kufunafuna Ufumu choyamba.—Mat. 6:33.

6. Kodi n’chimwemwe chotani chimene timakhala nacho tikamathandiza ena kutumikira Yehova?

6 Ntchito yophunzitsa ena Mawu a Mulungu ndiponso kupanga ophunzira imafuna khama. Koma n’zosangalatsa kwambiri kuona ofatsa akuyendabe m’choonadi.—3 Yoh. 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena