Tsatirani Khristu Podzisungira Ulemu
1. Kodi nkhani yodzisungira ulemu ikugwirizana bwanji ndi mutu wa msonkhano wachigawo wa chaka chino?
1 Baibulo limafotokoza kuti Yehova, Mfumu ya Chilengedwe Chonse, ndi wolemekezeka. (Sal. 104:1) Yesu nthawi zonse analankhula ndi kuchita zinthu zimene zinkalemekeza Atate wake ndi zinthu zimene anakhazikitsa. (Yoh. 17:4) Aliyense wa ife adzakhala ndi mpata wabwino wotsanzira Yesu ndi wolemekeza Yehova panthawi ya msonkhano wachigawo umene ukubwerawu wakuti “Tsatirani Khristu!”
2. N’chifukwa chiyani kukhalapo kwathu pachigawo chilichonse kumalemekeza Yehova?
2 Kulambira Kolemekezeka: Tingalemekeze Yehova mwa kukonza zokapezeka pa phwando lauzimu limene watikonzera. Kodi mwalankhula kale ndi abwana anu ndi kukonzekera kudzapita ku msonkhanowu masiku onse atatu, ndi loyamba lomwe? Kodi mwakonza zokafika nthawi yabwino kuti mukapeze malo ndi kuimba nawo nyimbo yoyamba ndiponso kupemphera nawo? Kodi mwakonza zodzatenga chakudya chamasana kuti mukadyere pa malo a msonkhano pomwepo limodzi ndi abale ena? Chigawo chilichonse chikamayamba, ndipo tcheyamani akatipempha kukhala pansi kuti nyimbo zamalimba ziyambe, mwamsanga tiyenera kuthetsa macheza athu ndi kukakhala pansi kudikirira kuti pulogalamu iyambe.
3. Kodi kutchera khutu nkhani zikamakambidwa, kumalemekeza bwanji kulambira kwathu?
3 Kutchera khutu nkhani zikamakambidwa, kumalemekezanso Atate wathu wakumwamba. Mtolankhani wina ataonerera msonkhano wachigawo, analemba kuti anthu angachite chidwi ndi “khalidwe labwino la osonkhanawo, onse ali chete kumvetsera nkhani mwaulemu, kusonyeza kuti amakonda zinthu zauzimu.” Ananenaponso za “ana ambiri . . . , onse atakhala phe osapulupudza, atafatsa kufunafuna mavesi m’Buku Lopatulika, ndipo zimenezi zinali zachilendo.” Nkhani zikamakambidwa, si nthawi yocheza, kutumizirana mauthenga pafoni, kudya, kapena kuyendayenda. Ana ayenera kukhala ndi makolo awo kuti aziwathandiza kumvetsera nkhani. (Deut. 31:12; Miy. 29:15) Pochita zonsezi, timalemekeza ena ndipo timasonyeza kuti tikuyamikira chakudya chauzimu chofunika kwambiri chimene tikupatsidwa.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala ndi kudzikongoletsa modzisungira ulemu tikakhala pa msonkhano?
4 Dzisungireni Ulemu Pakaonekedwe: Abale ambiri anayamikira kwambiri nkhani imene inali pa msonkhano wachigawo chaka chatha yakuti “Sonyezani Ulemu Monga Akhristu Nthawi Zonse.” Nkhani imeneyi inatsindika kuti atumiki a Mulungu aziyesetsa kudzisungira ulemu pakavalidwe ndi kudzikongoletsa. Chaka chinonso tizisamala ndi kaonekedwe kathu chifukwa kamasonyeza mmene timaonera Yehova ndiponso mwayi wathu wokhala Mboni zake. Nthawi zonse tiyenera kuvala ngati anthu “amene amati amalemekeza Mulungu.”—1 Tim. 2:9, 10.
5. Kodi tingachite chiyani kuti kaonekedwe kathu kakhale kodzisungira ulemu popuma pulogalamu itatha?
5 Kodi tiyenera kuvala ndi kudzikongoletsa modzisungira ulemu tikakhala pa msonkhano pokha? Dziwani kuti anthu ambiri adzationa titavala mabaji athu masiku onse a msonkhano. Kaonekedwe kathu kayenera kusiyana ndi ka anthu ena onse. Choncho, ngakhale panthawi yopuma, monga tikapita kokadya pulogalamu itatha, tiyenera kuvala moyenerera atumiki achikhristu oti ali pa msonkhano ndipo sitiyenera kuvala zinthu monga jinzi, kabudula, ndi sikipa. Kuvala ndi kudzikongoletsa kodzisungira ulemu kumapereka umboni wabwino kwa anthu ena. Yehova amasangalala ngati kaonekedwe kathu kakusonyeza kuti ndifedi atumiki ake.
6. Kodi kukhala ndi khalidwe lachikhristu lodzisungira ulemu kuli ndi ubwino wanji?
6 Zotsatira Zake Zimakhala Zabwino: Tikamadzisungira ulemu nthawi imene tili pa msonkhano, timakhala ndi mpata wolalikira mwamwayi ndipo anthu oona amakhala ndi chithunzi chabwino. Pamapeto pa msonkhano wina, mmodzi wa akuluakulu a bwalo la msonkhano anati: “Sitinaonepo anthu akhalidwe labwino chonchi. Inutu mumachita zimene Mulungu amayembekezera anthufe kuchita.” Khalidwe lodzisungira ulemu limalemekeza Yehova ndiponso ndi umboni wakuti timalemekeza ndi kukonda anthu ena. (1 Pet. 2:12) Limasonyezanso kuti timaopa Mulungu ndipo timayamikira mwayi umene tili nawo wophunzitsidwa ndi Atate wathu. (Aheb. 12:28) Tiyesetse kukhala ndi khalidwe lodzisungira ulemu poyembekezera msonkhano wachigawo wa chaka chino wakuti “Tsatirani Khristu!”
[Bokosi patsamba 6]
Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo
◼ Nthawi ya Mapulogalamu: Kwa masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba nthawi ya 8:20 m’mawa. Kutatsala mphindi zochepa kuti pulogalamu iyambe, tcheyamani wa chigawo adzakhala papulatifomu pamene nyimbo zamalimba za Ufumu zikuimba. Tonse tiyenera kukhala pansi kuti msonkhano uyambe bwinobwino. Tsiku loyamba ndi lachiwiri msonkhano udzatha nthawi ya 3:55 madzulo, ndipo tsiku lachitatu udzatha nthawi ya 3:00 madzulo.
◼ Koimika Galimoto ndi Njinga: Kulikonse komwe kudzachitikire msonkhano kudzakhala malo okwanira oimikapo magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani nonse kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto afunikira kudzaonetsetsa kuti zitseko za magalimoto azikhoma bwinobwino, ndipo nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.
◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pagalimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi.
◼ Chakudya Chamasana: Mudzabwere ndi chakudya chanu chamasana m’malo mochoka pa malo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochita zina zapadera ngati zimenezi. Mungatenge zinthu monga sangweji, tchipisi, mabisiketi, zipatso, mpunga, mbatata, chinangwa, mtedza wokazinga, ndi zakumwa. Mowa suloledwa pa malo a msonkhano.
◼ Zopereka: Pokonzekera msonkhano wachigawo pamapita ndalama zambiri. Timasonyeza kuyamikira mwa kupereka ndalama mwaufulu zothandiza pa ntchito ya padziko lonse, ku Nyumba ya Ufumu kapena kumsonkhano komweko. Macheke operekedwa pamsonkhano wachigawo azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.”
◼ Ngozi Ndiponso Matenda Amwadzidzidzi: Ngati munthu pamsonkhano wadwala mwadzidzidzi, dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo adzathe kuona mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.
◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’chinenero cha manja cha ku America, ku misonkhano yachigawo ya Chingelezi ku Blantyre ndi ku Lilongwe. Zimenezi zidzalengezedwa pachiyambiyambi pa chigawo choyamba.
◼ Kujambula Mawu: Musadzalumikize zipangizo zanu zojambulira kumagetsi kapena kuzokuzira mawu za pamsonkhano ndipo muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisasokoneze ena.
◼ Mafomu Odziwitsira Ena za Munthu Wachidwi: Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi panthawi ya msonkhano, gwiritsani ntchito mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43). Ofalitsa angabweretse fomu imodzi kapena awiri kumsonkhano. Mungapereke mafomu osainidwa bwinobwino ku Chipinda cha Mabuku kuti awasamalire kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwerako ku msonkhanowo.
◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli m’kati.
◼ Foni za M’manja: Muyenera kuzitchera kuti zisalire n’kusokoneza ena.