Kusintha Kosangalatsa kwa Nsanja ya Olonda
1 Kumayambiriro kwa chaka chino, mipingo inalandira chilengezo chosangalatsa kwambiri chakuti: Kuyambira mu January 2008, Nsanja ya Olonda izikonzedwa m’njira ziwiri. Imodzi izidzakhala ya anthu amene si Mboni ndipo inayo ya Mboni za Yehova. Mwina mwakhala mukudzifunsa kuti: ‘Kodi magazini awiriwa azidzasiyana bwanji ndipo zimenezi zidzakhala ndi ubwino wotani? Kodi m’magaziniwa mudzakhala zinthu zatsopano zosangalatsa?’
2 Kusiyana Kwake: Nsanja ya Olonda ya pa 1 mwezi uliwonse izidzatchedwa Magazini Yogawira. Nkhani zonse za m’magazini imeneyi zizidzakonzedwera anthu amene si Mboni. Ndipo magazini ya pa 15 mwezi uliwonse izidzatchedwa Magazini Yophunzira ndipo sitizidzaigawira mu utumiki wa kumunda. Magaziniyi izidzakhala ndi nkhani zonse zophunzira za mwezi umodzi ndiponso nkhani zina zoyenerera Akhristu odzipereka kwa Yehova. Magazini Yogawira ya Nsanja ya Olonda imeneyi idzasangalatsa kwambiri anthu amene si Mboni koma amakhulupirira Baibulo ndipo ifenso Mboni za Yehova tidzasangalala nayo. Koma magazini ya Galamukani! izikonzedwabe kuti anthu ambiri aziiwerenga ngakhale amene sakhulupirira kwenikweni Baibulo, ndiponso amene zipembedzo zawo si zachikhristu.
3 Ubwino Wake: M’Magazini Yophunzira, sitidzafunikiranso kufotokoza mawu monga akuti “mpainiya” n’cholinga choti anthu amene si Mboni amvetse. M’magaziniyi mudzakhalanso mfundo zofunika zokonzedwera makamaka Mboni za Yehova ndiponso ophunzira Baibulo amene akupita patsogolo mwauzimu. Nanga bwanji Magazini Yogawira? Nkhani za m’magaziniyi zizidzalembedwa m’njira yakuti anthu amene si Mboni adzasangalala kuwerenga magazini yonse. Ndiponso, wa Mboni aliyense adzapindula mwa kuwerenga nkhani zonse za m’magaziniyi. Popeza tizingogawira magazini imodzi ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! muutumiki wa kumunda mwezi uliwonse, tizikhala ndi nthawi yambiri yokonzekera bwino maulaliki ogwira mtima.
4 Zinthu Zatsopano: M’Magazini Yogawira ya Nsanja ya Olonda mudzakhala zinthu zatsopano zosangalatsa. Mudzakhala nkhani ina imene izifotokoza mosavuta kwambiri ziphunzitso zofunika za m’Malemba. Nkhani ina izifotokoza mmene Baibulo lingathandizire mabanja. Mudzakhalanso nkhani zothandiza achinyamata kufufuza zinthu m’Baibulo. Ndiponso mudzakhala nkhani yofotokoza mbali zina za m’Baibulo zimene zimatiphunzitsa kwambiri za makhalidwe a Yehova.
5 Tikukhulupirira kuti Yehova adzadalitsa makonzedwe atsopano a Nsanja ya Olonda amenewa. Ndiponso n’cholinga chathu kuti uthenga wabwino womwe udzakhale m’magazini amenewa, limodzi ndi magazini ya Galamukani!, udzathandize anthu ambiri oyenerera.—Mat. 10:11.