Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/07 tsamba 4
  • Musalephere Kuchititsa Phunziro la Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musalephere Kuchititsa Phunziro la Baibulo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Amosi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kuzimiririka kwa Mtundu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Amosi Kodi Anali Wotchera Nkhuyu Kapena Wobaya Nkhuyu?
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 11/07 tsamba 4

Musalephere Kuchititsa Phunziro la Baibulo

1. Kodi anthu ena ‘sitiwamana’ zabwino mwa kuchita chiyani?

1 Tikamalengeza mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, anthu amene ali m’gawo lathu ‘sitiwamana’ zabwino. (Miy. 3:27) Uthenga wosangalatsa kwambiri umene tingauze anthu ndi wonena za nthawi yabwino imene idzakhalapo mu ulamuliro wa Mulungu. Ngakhale kuti nthawi zambiri mumauza ena chiyembekezo cha Ufumu polalikira mwamwayi kapena pogawira mabuku, bwanji osakhala ndi cholinga chochititsa phunziro la Baibulo, ngati panopo mulibe?

2. Kodi tingalephere kuyambitsa phunziro la Baibulo chifukwa chiyani?

2 Nthawi zina, maganizo amene timakhala nawo ndi amene amatilepheretsa kwambiri kuchititsa phunziro la Baibulo. Ena amalephera kuchititsa phunziro la Baibulo chifukwa chodzikayikira kapena chifukwa chotanganidwa kwambiri. Mfundo zili m’munsimu zingakuthandizeni kuti musalephere kugwira nawo ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo imeneyi.—Mat. 28:19; Mac. 20:20.

3. N’chifukwa chiyani ndife oyenerera kuphunzitsa ena Baibulo?

3 Kudzikayikira: Mwina sukulu simunapite nayo patali, kapena pa zifukwa zina mumadzikayikira ngati mungathe kuchititsa phunziro la Baibulo. Atumiki achikhristu m’masiku a atumwi anali “anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba.” Kodi n’chiyani chinawathandiza kuphunzitsa ena choonadi? Chinali chifukwa choti “anali kuyenda ndi Yesu.” (Mac. 4:13) Anaphunzitsidwa ndi Mphunzitsi Waluso kwambiri, Yesu, yemwe ziphunzitso zake ndiponso njira zake zophunzitsira zinalembedwa m’Baibulo kuti nafenso tiphunzirepo. Ngakhale mutakhala kuti sukulu simunapite nayo patali, maphunziro auzimu amene mukulandira ndi apamwamba kwambiri kuposa maphunziro ena onse.—Yes. 50:4; 2 Akor. 3:5.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Amosi?

4 Nthawi zina Yehova ankatuma aneneri kuti akadzudzule olamulira kapena anthu ena amaudindo akuluakulu omwe anachimwa. Aneneri ena, monga Amosi, poyamba anali anthu wamba. Amosi anati: “Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng’ombe, ndi wakutchera nkhuyu.” (Amosi 7:14) Ngakhale zinali choncho, Amosi sanalephere kupereka uthenga wa Yehova woweruza Amaziya, wansembe yemwe anali kulambira fano la mwana wa ng’ombe. (Amosi 7:16, 17) Nthawi zonse tizikumbukira kuti tikugwira ntchito ya Mulungu ndipo iye adzatithandiza kukhala oyenerera bwino kugwira ntchito imene watipatsayo.—2 Tim. 3:17.

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuyambitsa phunziro la Baibulo ngakhale kuti ndife otanganidwa?

5 Kutanganidwa: Ngakhale kuti mumakhala wotanganidwa, muyenera kuti munakonza kale nthawi yoti muzilowa mu utumiki mokhazikika. Kuchititsa phunziro la Baibulo ndi mbali imodzi ya utumiki wathu imene imasangalatsa kwambiri. Ndi mwayi wapadera kuona Mawu a Yehova akusintha moyo wa munthu. (Aheb. 4:12) Yehova amasangalala tikamadzimana zinthu zina kuti tithe kuthandiza ena “kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Angelo nawonso amasangalala munthu wina akalapa ndi kusiya zochita zake zakale n’kuyamba kupita patsogolo mwauzimu.—Luka 15:10.

6. Kodi ndi ntchito yapadera yotani imene tili nayo pochita chifuniro cha Mulungu?

6 “Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Tilitu ndi ntchito yapadera kwambiri yochita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Motero, tisalephere kuchititsa maphunziro a Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena