‘Tsatirani Mapazi Ake Mosamalitsa’
1. Kodi tingatani kuti tikhale atumiki ogwira mtima?
1 Pa atumiki onse akale, Yesu anali Mtumiki waluso kwambiri ngakhale kuti sanaphunzire sukulu za Arabi. N’zosangalatsa kuti pali mabuku onena za utumiki wake amene tingapindule nawo. Kuti tikhale atumiki ogwira mtima tiyenera ‘kutsatira mapazi ake mosamalitsa.’—1 Pet. 2:21.
2. N’chiyani chingatithandize kukonda anthu monga mmene Khristu ankawakondera?
2 Sonyezani Kuti Mumakonda Anthu: Yesu ankachitira anthu zinthu zosiyanasiyana chifukwa chowakonda. (Maliko 6:30-34) Anthu ambiri m’gawo lathu ‘akumva zopweteka’ ndipo akufunikira kumva choonadi. (Aroma 8:22) Kuganizira za mavuto awo ndiponso kuti Yehova amawakonda kungatilimbikitse kupitiriza ntchito yolalikira. (2 Pet. 3:9) Komanso nthawi zambiri anthu amalabadira uthenga wathu akadziwa kuti timawaganizira kwambiri.
3. Kodi ndi nthawi iti imene Yesu ankalalikira?
3 Lalikirani Paliponse Pamene Mwapeza Mpata: Yesu ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kulalikira uthenga wabwino kwa ena. (Mat. 4:23; 9:9; Yoh. 4:7-10) Nafenso tikamagwira ntchito zathu za tsiku ndi tsiku tifunika kukhala okonzeka kufotokozera ena za choonadi. Ena amayenda ndi Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo n’cholinga choti alalikire ku ntchito, kusukulu, pamene ali pa ulendo, kumsika ndi kwina kulikonse.
4. Kodi tingatani kuti Ufumu ukhale mfundo yaikulu ya ulaliki wathu?
4 Sonyezani Anthu za Kufunika kwa Ufumu: Mfundo yaikulu ya ulaliki wa Yesu inali uthenga wabwino wa Ufumu. (Luka 4:43) Ngakhale kuti ulaliki wathu sungayambe n’kutchula za Ufumu kapenanso sungatchule n’komwe, timadziwa kuti tiyenera kuthandiza mwininyumba kuti aone kufunika kwa Ufumu. Ngakhale pamene timatchula za zinthu zoipa zochitika padzikoli zimene zikusonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza, kwenikweni timakhala ‘tikulengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino.’—Aroma 10:15.
5. Kodi tiyenera kuligwiritsa ntchito motani Baibulo kuti utumiki wathu ukhale wogwira mtima?
5 Dalirani Mawu a Mulungu: Yesu ankadalira Malemba muutumiki wake wonse. Zonse zimene anaphunzitsa sizinali zake. (Yoh. 7:16, 18) Mawu a Mulungu anali chakudya chake ndipo anawagwiritsa ntchito podziteteza ataukiridwa ndi Satana. (Mat. 4:1-4) Tiziwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzirazo n’cholinga choti tiziphunzitsa anthu mogwira mtima. (Aroma 2:21) Tikamayankha mafunso muutumiki, tizifotokoza mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi zimene tikunena ndiponso tiziwerenga Baibulo ngati n’zotheka. Timafuna kuti mwininyumba aone kuti tikufotokoza maganizo a Mulungu osati athu.
6. Kodi Yesu ankachita chiyani kuti afike pamtima omvetsera ake?
6 Phunzitsani Anthu Mowafika Pamtima: Alonda atalephera kugwira Yesu, akulu a ansembe ndi Afarisi anawafunsa chifukwa chake. Poyankha, alondawo anati: “Palibe munthu analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Yoh. 7:46) M’malo mongofotokoza mmene zinthu zilili, Yesu ankafika pa mtima anthu amene anali kuwaphunzitsa. (Luka 24:32) Kuti anthu amvetse zimene akunena, iye ankagwiritsa ntchito mafanizo a zinthu zochitikadi. (Mat. 13:34) Yesu sankauza anthu zinthu zambirimbiri panthawi imodzi. (Yoh. 16:12) Zimene ankaphunzitsa zinachititsa anthu kulemekeza Yehova osati iyeyo. Mofanana ndi Yesu, nafenso tingakhale aphunzitsi abwino ngati ‘tisamala mosalekeza zimene timaphunzitsa.’—1 Tim. 4:16.
7. N’chifukwa chiyani Yesu sanagwe ulesi muutumiki wake?
7 Musagwe Ulesi ndi Anthu Osalabadira Kapena Otsutsa: Ngakhale kuti Yesu anachita zamphamvu zosiyanasiyana, anthu ochepa okha ndi amene anamvera zonena zake. (Luka 10:13) Ngakhale abale ake ankaganiza kuti Yesu “wachita misala.” (Maliko 3:21) Koma Yesu sanagwe ulesi ndi zimenezi chifukwa anali ndi chikhulupiriro chonse kuti akuphunzitsa choonadi chimene chikanamasula anthu. (Yoh. 8:32) Ifenso tiyesetsa kusagwa ulesi popeza kuti Yehova akutithandiza.—2 Akor. 4:1.
8, 9. Pankhani yokhala odzipereka chifukwa cha uthenga wabwino, kodi tingatsanzire bwanji Yesu?
8 Dziperekeni Kuti Mulalikire Nawo Mokwanira: Yesu analolera kukhala wopanda chilichonse chifukwa chofuna kuchita utumiki. (Mat. 8:20) Iye ankalalikira mosatopa ndipo nthawi zina anali kulalikira mpaka usiku. (Maliko 6:35, 36) Ankadziwa kuti anali ndi nthawi yochepa kuti amalize ntchito yake. Popeza kuti “nthawi yotsalayi yafupika,” nafenso potsanzira Yesu, tifunikira kudzipereka pogwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu, ndi chuma chathu.—1 Akor. 7:29-31.
9 Akhristu oyambirira anali atumiki ogwira mtima chifukwa chakuti anaphunzitsidwa ndi Yesu. (Mac. 4:13) Nafenso tingakwaniritse utumiki wathu bwino lomwe tikamatsanzira Mtumiki waluso kwambiri m’mbiri yonse ameneyu.—2 Tim. 4:5.