Phunzitsani Ena Kukonda Yehova
1. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena amayamba kukonda Yehova?
1 Kodi mukukumbukira nthawi yoyamba imene munamva za Yehova? Kodi n’chifukwa chiyani munayamba kumukonda? Anthu ambiri okonda choonadi angakuuzeni kuti anayamba kukonda Mlengi wathu atangodziwa za makhalidwe ake apamwamba, makamaka chifundo ndi chikondi chake.—1 Yoh. 4:8.
2, 3. Kodi buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani tingaligwiritse ntchito bwanji pothandiza ophunzira Baibulo kuti azikonda kwambiri Yehova?
2 “Uyu Ndiye Mulungu Wathu”: Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani limafotokoza bwino chikondi cha Yehova ndiponso kufunika kokhala naye paubale. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji buku limeneli pophunzitsa ena kuti azikonda kwambiri Mulungu? Pokambirana mfundo yatsopano, tingawafunse mafunso amene angawathandize kuganiza, monga akuti: “Kodi mfundo imeneyi ikutiuza chiyani za Yehova?” kapena “Kodi mfundo imeneyi ikusonyeza bwanji kuti Yehova ndi Atate wabwino kuposa aliyense?” Kuphunzitsa mwanjira imeneyi kungathandize wophunzira wathu kukhala paubale ndi Yehova kwa moyo wonse.
3 Tikamathandiza ophunzira Baibulo kuzindikira kuti ndi mwayi wapadera kuphunzira za Mulungu woona yekha ndiponso wamoyo, adzafika ponena mawu ngati a Yesaya akuti, “uyu ndiye Mulungu wathu.” (Yes. 25:9) Pofotokoza Mawu a Mulungu, timafunika kunena motsindika kuti Yehova akadzakwaniritsa zolinga zake kudzera mu boma lake lolamulidwa ndi Khristu Yesu, anthu adzadalitsidwa kwambiri.—Yes. 9:6, 7.
4, 5. Kodi kukonda Yehova kumafuna chiyani?
4 Umboni Wakuti Timakonda Yehova: Timadziwa kuti kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi nzeru zathu zonse, kumafuna zambiri osati chabe kungokhudzidwa mtima. Timafunika kuyamba kuganiza ngati mmene iye amaganizira ndi kutsatira maganizo akewo. (Sal. 97:10) Timasonyeza kuti timakonda Mulungu tikamatsatira malamulo ake onse ndi kupitiriza kukhala ndi ‘khalidwe loyera ndi [kugwira] ntchito za kudzipereka kwathu kwa Mulungu,’ ngakhale pamene tikuyesedwa kapena kutsutsidwa.—2 Pet. 3:11; 2 Yoh. 6.
5 Kuchita chifuniro cha Mulungu chifukwa chomukonda n’kosangalatsa. (Sal. 40:8) Wophunzira Baibulo ayenera kufika pozindikira kuti atumiki a Mulungu amapindula ndi malamulo onse amene iye wapereka, ndipo phindu lakelo silitha. (Deut. 10:12, 13) Munthu akamatsatira malangizo a Yehova, amasonyeza kuti akuyamikira kwambiri ntchito zake zonse zodabwitsa. Thandizani wophunzira Baibulo kumvetsa kuti kuyenda m’njira za Yehova zolungama kumathandiza munthu kupewa mavuto ambiri.
6. Kodi munthu angapeze madalitso otani chifukwa chokonda Yehova?
6 Anthu Okonda Mulungu Amapeza Madalitso Ambiri: Yehova amasamalira kwambiri anthu odzichepetsa amene amamukonda, ndipo amawaululira “zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Chifukwa chozindikira zolinga za Yehova, iwo amadziwa bwino tsogolo lawo ndipo amakhala ndi chiyembekezo champhamvu. (Yer. 29:11) Anthu amene amakonda Yehova, amachitiridwa chifundo kwambiri. (Eks. 20:6) Iwo amasangalala kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha popeza kuti Mulungu amawakonda kwambiri.—Yoh. 3:16.
7. Kodi nkhani yophunzitsa ena kukonda Yehova mumaiona bwanji?
7 Tikamadziwa kwambiri Atate wathu wakumwamba, m’pamenenso timakhala ndi zinthu zambiri zouza ena. (Mat. 13:52) Ndiyetu ndi mwayi wosayerekezereka kuphunzitsa ena, makamaka ana athu, kukonda Yehova. (Deut. 6:5-7) Choncho tiyeni tonse, limodzi ndi ophunzira Baibulo athu, tipitirize kusefukira ndi chitamando poona ‘ubwino waukulu wa Yehova.’—Sal. 145:7.